Maliko 1:1-45

1  Chiyambi cha uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu:  Monga mmene analembera m’buku la mneneri Yesaya kuti: “(Taona! Ine ndikutumiza mthenga wanga pamaso pako, amene adzakonza njira yako.)*+  Tamverani! Winawake akufuula m’chipululu kuti, ‘Konzani njira ya Yehova* anthu inu, wongolani misewu yake,’”+  Yohane m’batizi anafika m’chipululu, ndipo anali kulalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+  Choncho onse okhala m’dera la Yudeya ndi onse okhala mu Yerusalemu anakhamukira kwa iye. Chotero iye anawabatiza mumtsinje wa Yorodano ndipo anthuwo anali kuulula machimo awo poyera.+  Yohane ameneyu anali kuvala chovala cha ubweya wa ngamila ndi lamba wachikopa m’chiuno mwake,+ ndipo anali kudya dzombe+ ndi uchi.+  Iye anali kulalikira kuti: “Pambuyo pangapa pakubwera winawake wamphamvu kuposa ine; ine sindili woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake.+  Ine ndakubatizani ndi madzi, koma iye adzakubatizani ndi mzimu woyera.”+  M’masiku amenewo, Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu Yorodano.+ 10  Atangovuuka m’madzimo, iye anaona kumwamba kukutseguka, ndiponso mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera.+ 11  Pamenepo panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwera nawe.”+ 12  Nthawi yomweyo mzimuwo unamulimbikitsa kupita kuchipululu.+ 13  Chotero iye anakhala m’chipululumo masiku 40,+ akuyesedwa ndi Satana.+ M’chipululumo munalinso nyama zakutchire. Pambuyo pake, angelo anam’tumikira.+ 14  Tsopano Yohane ataponyedwa m’ndende, Yesu anapita ku Galileya+ kukalalikira uthenga wabwino wa Mulungu+ 15  kuti: “Nthawi yoikidwiratu yakwaniritsidwa!+ Ufumu wa Mulungu wayandikira! Lapani+ anthu inu! Khulupirirani uthenga wabwino!” 16  Pamene anali kuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya* Yesu anaona Simoni+ ndi Andireya m’bale wake wa Simoni, akuponya maukonde awo m’nyanjamo, pakuti anali asodzi.+ 17  Chotero Yesu anawauza kuti: “Nditsatireni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+ 18  Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatira.+ 19  Atapita patsogolo pang’ono, anaona Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi m’bale wake Yohane, ali mu ngalawa yawo akusoka maukonde awo.+ 20  Nthawi yomweyo anawaitana. Iwonso anasiya bambo wawo Zebedayo m’ngalawamo limodzi ndi anthu aganyu, ndipo anam’tsatira. 21  Onsewo anachoka ndi kupita ku Kaperenao.+ Litangofika tsiku la sabata anakalowa m’sunagoge ndi kuyamba kuphunzitsa. 22  Mmenemo anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake,+ chifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu wokhala ndi ulamuliro, osati monga alembi.+ 23  Komanso pa nthawi yomweyo, m’sunagoge mwawomo munali munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa, ndipo munthuyo anafuula,+ 24  kuti: “Kodi tili nanu chiyani, Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani+ bwino kwambiri, ndinu Woyera+ wa Mulungu.”+ 25  Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye!”+ 26  Pamenepo mzimu wonyansawo unam’tsalimitsa ndipo unafuula mokweza. Kenako unatuluka mwa munthuyo.+ 27  Ataona zimenezi, anthu onse anazizwa kwambiri moti anayamba kukambirana kuti: “Kodi chimenechi n’chiyani? N’chiphunzitso chatsopano! Ngakhale mizimu yonyansa akuilamula mwamphamvu, ndipo ikumumvera.”+ 28  Chotero mbiri yake inawanda mofulumira kwambiri m’chigawo chonse cha Galileya.+ 29  Nthawi yomweyo iwo anatuluka m’sunagogemo ndi kupita kunyumba kwa Simoni+ ndi Andireya. Yakobo ndi Yohane nawonso anapita nawo. 30  Koma apongozi aakazi a Simoni+ anali chigonere, akudwala malungo.*+ Mwamsanga iwo anamuuza za mayiyo. 31  Pamenepo iye anapita kumene kunali mayiyo n’kumuimiritsa, atamugwira dzanja. Atatero malungowo anatheratu+ moti mayiyo anayamba kuwatumikira.+ 32  Chakumadzulo dzuwa litalowa, anthu anayamba kumubweretsera odwala onse+ ndi ogwidwa ziwanda,+ 33  ndipo anthu onse a mumzindawo anasonkhana pakhomopo. 34  Choncho Yesu anachiritsa ambiri amene anali kudwala matenda osiyanasiyana,+ ndipo anatulutsa ziwanda zambiri. Koma sanalole kuti ziwandazo zilankhule, chifukwa zinali kum’dziwa kuti ndi Khristu.+ 35  M’mawa kwambiri kukali mdima, Yesu anadzuka ndi kutuluka panja, ndipo anapita kumalo kopanda anthu.+ Kumeneko anayamba kupemphera.+ 36  Koma Simoni ndi ena amene anali naye anam’funafuna 37  ndi kumupeza, ndipo anamuuza kuti: “Anthu onse akukufunafunani.” 38  Koma iye anawayankha kuti: “Tiyeni tipite kwina kumidzi yapafupi, kuti ndikalalikire+ kumenekonso, pakuti ndicho cholinga chimene ndinabwerera.”+ 39  Iye anapitadi ndipo anali kulalikira m’masunagoge mwawo mu Galileya yense ndi kutulutsa ziwanda.+ 40  Kumenekonso munthu wina wakhate anafika kwa iye, ndipo anagwada pansi ndi kum’dandaulira, kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+ 41  Pamenepo anagwidwa chifundo,+ ndipo anatambasula dzanja lake n’kumukhudza. Kenako anamuuza kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.”+ 42  Nthawi yomweyo khate lakelo linatha, ndipo anakhala woyera.+ 43  Kenako anamupatsa malangizo amphamvu, ndi kumuuza kuti apite nthawi yomweyo. 44  Anamuuza kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi, koma upite ukadzionetse kwa wansembe+ ndipo ukapereke zinthu zimene Mose analamula+ chifukwa cha kuyeretsedwa kwako, kuti zikhale umboni kwa iwo.”+ 45  Koma atachoka, munthu uja anayamba kulengeza zimenezo paliponse ndi kufalitsa nkhaniyo m’madera ena, moti Yesu sanathenso kulowa mumzinda uliwonse moonekera, koma anapitiriza kukhala kunja kopanda anthu. Komabe anthu anali kubwerabe kuchokera kumbali zonse.+

Mawu a M'munsi

Mawu amene ali m’mikutiramawu Maliko anawagwira pa Mki 3:1.
Onani Zakumapeto 2.
M’Baibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesarete, komanso nyanja ya Tiberiyo.
Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”