Maliko 14:1-72

14  Tsopano kunangotsala masiku awiri kuti pasika+ ndi chikondwerero+ cha mikate yopanda chofufumitsa zichitike.+ Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anali kufunafuna njira yogwirira Yesu mochenjera ndi kumupha.+  Iwo nthawi zonse anali kunena kuti: “Tisadzamugwire pa chikondwerero, mwina anthu angadzachite chipolowe.”+  Ndiyeno Yesu ali ku Betaniya m’nyumba ya Simoni wakhate+ uja, ali pa chakudya, kunafika mayi wina ali ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala la mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado weniweni, okwera mtengo kwambiri. Atatsegula botolo la alabasitala lija mochita kuswa, anayamba kuthira mafutawo m’mutu mwa Yesu.+  Poona izi, ena anakhumudwa ndi kunena kuti: “N’chifukwa chiyani akuwononga chonchi mafuta onunkhirawa?+  Pakuti mafuta onunkhirawa akanagulitsidwa ndalama zoposa madinari 300 n’kuzipereka kwa osauka!” Chotero iwo anakhumudwa kwambiri ndi mayiyo.+  Koma Yesu anati: “Mulekeni. N’chifukwa chiyani mukum’vutitsa mayiyu? Iyetu wandichitira zinthu zabwino.+  Pakuti osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ ndipo nthawi iliyonse imene mwafuna mungathe kuwachitira zabwino. Koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+  Mayiyu wachita zimene angathe. Iye wapakiratu thupi langa mafuta onunkhira kukonzekera kuikidwa kwanga m’manda.+  Ndithu ndikukuuzani, Kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe m’dziko lonse,+ anthu azidzanenanso zimene mayiyu wachita kuti azidzam’kumbukira.”+ 10  Kenako Yudasi Isikariyoti, mmodzi wa ophunzira 12 aja, anachoka ndi kupita kwa ansembe aakulu kuti akapereke Yesu kwa iwo.+ 11  Atamva zimenezo, iwo anasangalala ndi kumulonjeza kuti am’patsa ndalama zasiliva.+ Choncho iye anayamba kufunafuna mpata wabwino umene angamuperekere.+ 12  Tsopano pa tsiku loyamba la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ pamene mwa mwambo anali kupereka nsembe nyama ya pasika, ophunzira ake+ anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tipite kuti kumene tikakukonzereni malo odyerako pasika?”+ 13  Pamenepo Yesu anatuma awiri mwa ophunzira akewo ndi kuwauza kuti: “Pitani mumzinda, ndipo mwamuna wina wosenza mtsuko wa madzi akakumana nanu.+ Mukam’tsatire ameneyo, 14  ndipo m’nyumba imene akalowe, mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi akufunsa kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti, mmene ine ndidyeremo pasika+ pamodzi ndi ophunzira anga?”’+ 15  Iye akakusonyezani chipinda chachikulu cham’mwamba, chokonzedwa bwino. Mukatikonzere pasika mmenemo.”+ 16  Choncho ophunzirawo anapita ndi kulowa mumzinda, ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Chotero anakonzekera pasika kumeneko.+ 17  Chakumadzulo ndithu, Yesu anafika limodzi ndi ophunzira ake 12 aja.+ 18  Ndipo akudya chakudya patebulo, Yesu anati: “Ndithu ndikukuuzani, Mmodzi wa inu, amene akudya+ nane limodzi, andipereka.”+ 19  Pamenepo chisoni chinawagwira ndipo anayamba kumufunsa mmodzimmodzi kuti: “Kodi ndine kapena?”+ 20  Iye anati: “Ndi mmodzi wa inu 12, amene akusunsa nane m’mbale imodzi.+ 21  Zoona, Mwana wa munthu akuchokadi, monga Malemba amanenera za iye. Koma tsoka kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu! Zikanakhala bwino munthu ameneyu akanapanda kubadwa.”+ 22  Pamene anali kudya, iye anatenga mkate ndi kupempha dalitso. Kenako anaunyemanyema ndi kuwapatsa, ndipo anati: “Tengani, mkate uwu ukuimira thupi langa.”+ 23  Kenako anatenga kapu ndi kuyamika, n’kuipereka kwa iwo, ndipo onse anamwa.+ 24  Ndiyeno anawauza kuti: “Vinyoyu akuimira ‘magazi+ anga a pangano,’+ amene adzakhetsedwa+ chifukwa cha anthu ambiri.+ 25  Ndithu ndikukuuzani, sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa kufikira tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”+ 26  Potsirizira pake, atatha kuimba nyimbo zotamanda Mulungu,+ anatuluka n’kupita kuphiri la Maolivi.+ 27  Tsopano Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthawa kundisiya ndekha, chifukwa Malemba amati, ‘Ndidzapha m’busa,+ ndipo nkhosa zidzabalalika.’+ 28  Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya+ inu musanafikeko.” 29  Ndiyeno Petulo anauza Yesu kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, koma ine ndekha sindidzatero.”+ 30  Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza, iweyo lero, usiku womwe uno, tambala asanalire kawiri, undikana katatu.”+ 31  Koma iye ananena molimba mtima kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” Ndipo ena onse anayamba kunenanso chimodzimodzi.+ 32  Kenako anafika pamalo otchedwa Getsemane, ndipo anauza ophunzira akewo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikukapemphera.”+ 33  Popita kumeneko anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane,+ ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika kwambiri mumtima mwake.+ 34  Ndiyeno anawauza kuti: “Moyo wanga ukumva chisoni chofa nacho.+ Khalani pompano ndipo mukhalebe maso.”+ 35  Choncho atapita patsogolo pang’ono anadzigwetsa pansi ndipo anayamba kupemphera kuti ngati zikanatheka, asakumane ndi mayesero amenewa.+ 36  Kenako anati: “Abba,* Atate,+ zinthu zonse n’zotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”+ 37  Tsopano anabwerera ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Simoni, zoona ukugona? Kodi unalibe mphamvu kuti ukanakhalabe maso ola limodzi?+ 38  Amuna inu, khalani maso ndipo muzipemphera,+ kuti musalowe m’mayesero. Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+ 39  Atatero anachokanso kupita kukapemphera, motchula mawu omwe aja.+ 40  Atabweranso anawapezanso akugona, pakuti zikope zawo zinali zitalemera ndi tulo, ndipo iwo anasowa chomuyankha.+ 41  Anabweranso kachitatu ndi kuwauza kuti: “Koma zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula! Basi! Nthawi yakwana!+ Taonani! Mwana wa munthu akuperekedwa m’manja mwa ochimwa.+ 42  Nyamukani, tiyeni tizipita.+ Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”+ 43  Nthawi yomweyo, mawu adakali m’kamwa, Yudasi, mmodzi wa ophunzira ake 12 aja, anafika limodzi ndi khamu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu ndi alembi ndi akulu, atanyamula malupanga ndi zibonga.+ 44  Apa n’kuti womupereka ameneyu atawapatsa chizindikiro chimene anagwirizana nawo, chakuti: “Amene ndim’psompsone ndi ameneyo. Mum’gwire ndi kupita naye osam’taya.”+ 45  Pamenepo Yudasi anayenda molunjika ndi kufika kwa iye. Kenako anati: “Rabi!” Ndipo anam’psompsona.+ 46  Choncho iwo anam’gwira ndi kum’manga.+ 47  Koma wina mwa amene anaimirira chapafupi anasolola lupanga lake ndi kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+ 48  Koma Yesu anawafunsa kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukukalimbana ndi wachifwamba?+ 49  Tsiku ndi tsiku ndinali nanu m’kachisi kuphunzitsa,+ koma simunandigwire. Komabe, izi zikuchitika kuti Malemba+ akwaniritsidwe.”+ 50  Pamenepo ophunzira ake onse anathawa ndi kumusiya+ yekha.+ 51  Koma mnyamata wina amene anafunda nsalu yake yabwino popanda chovala china mkati, anayamba kumutsatira chapafupi ndithu. Anthuwo anayesa kumugwira,+ 52  koma iye anawasiyira m’manja nsalu yake ija, ndi kuthawa ali maliseche.* 53  Tsopano iwo anatengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo ansembe aakulu komanso akulu ndi alembi onse anasonkhana kumeneko.+ 54  Koma Petulo, anali kum’tsatira chapatali ndithu,+ mpaka anafika m’bwalo lamkati kunyumba ya mkulu wa ansembe. Kumeneko iye anakhala pansi pamodzi ndi antchito a m’nyumbamo, n’kumawotha moto walawilawi. 55  Pa nthawiyi ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda* anali kufunafuna umboni kuti amunamizire mlandu Yesu ndi kumupha,+ koma sanali kuupeza.+ 56  Ndipo anthu ambiri anali kupereka umboni wonama kutsutsana naye,+ koma maumboni awowo anali kutsutsana.+ 57  Komanso, ena anali kuimirira ndi kupereka umboni womunamizira kuti: 58  “Ife tinamva iyeyu akunena kuti, ‘Ine ndidzagwetsa kachisi uyu amene anamangidwa ndi manja, ndipo m’masiku atatu okha ndidzamanga wina osati womangidwa ndi manja.’”+ 59  Komabe ngakhale pa mfundo zimenezi, umboni wawo sunali wogwirizana. 60  Potsirizira pake, mkulu wa ansembe anaimirira pakati pawo ndi kufunsa Yesu kuti: “Sukuyankha chilichonse? Kodi n’zoona zimene awa akukunenezazi?”+ 61  Koma iye anangokhala chete osanena chilichonse.+ Apanso mkulu wa ansembe anayamba kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsidwayo?”+ 62  Pamenepo Yesu anati: “Inde ndinedi, ndipo anthu inu mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera ndi mitambo yakumwamba.”+ 63  Tsopano mkulu wa ansembe atamva zimenezi anang’amba malaya ake amkati+ ndi kunena kuti: “Nanga n’kufunanso mboni zina pamenepa?+ 64  Mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu.+ Mukuona bwanji pamenepa?” Onse anati ayenera kuphedwa basi. 65  Pamenepo ena anayamba kumulavulira,+ kumuphimba nkhope ndi kumukhoma nkhonya. Iwo anali kunena kuti: “Losera!” Atamuwomba mbama, asilikali a pakhoti anamutenga.+ 66  Tsopano pamene Petulo anali m’munsi, m’bwalo lamkati, mmodzi wa atsikana antchito a mkulu wa ansembe anabwera.+ 67  Ataona Petulo akuwotha moto, anamuyang’anitsitsa ndi kunena kuti: “Inunso munali ndi Yesu, Mnazareti uja.”+ 68  Koma iye anakana kuti: “Ngakhale kumudziwa, sindikumudziwa ameneyo, ndipo sindikumvetsa kuti ukunena chiyani.” Atatero anatuluka panja ndi kupita kukachipinda ka kuchipata.+ 69  Kumenekonso mtsikana wantchito atamuona, anayamba kuuzanso amene anali ataimirira chapafupi kuti: “Bambo awanso ali m’gulu la ophunzira ake.”+ 70  Apanso anakana. Patapitanso kanthawi pang’ono, amene anali ataimirira chapafupi anayamba kuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli m’gulu la ophunzira ake. Ndipo ndiwenso Mgalileya.”+ 71  Koma iye anayamba kudzitemberera ndi kulumbira kuti:+ “Munthu amene mukunenayu ine sindikumudziwa ayi.”+ 72  Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri.+ Pamenepo Petulo anakumbukira mawu amene Yesu anamuuza aja, akuti: “Tambala asanalire kawiri, udzandikana katatu.”+ Ndipo anamva chisoni ndi kuyamba kulira.+

Mawu a M'munsi

Mawu achiaramu otanthauza “ababa,” kapena, “Bambo anga!”
Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “ali maliseche” angatanthauze kuti “atavala zovala zamkati zokha,” osati ali mbulanda kapena asanavale chilichonse.
Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”