Maliko 13:1-37
13 Pamene Yesu anali kutuluka m’kachisi, mmodzi wa ophunzira ake anamuuza kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikuonekera!”+
2 Koma Yesu ananena kuti: “Kodi waziona nyumba zapamwamba zimenezi?+ Pano sipadzatsala mwala+ uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”+
3 Tsopano atakhala pansi m’phiri la Maolivi, kachisi akuonekera bwino, Petulo,+ Yakobo, Yohane ndi Andireya anayamba kumufunsa kumbaliko kuti:+
4 “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro chosonyeza kuti zinthu zonsezi zili m’nthawi yake yamapeto n’chiyani?”+
5 Choncho Yesu anayamba kuwauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusocheretseni.+
6 Ambiri adzabwera m’dzina langa, ndi kunena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.+
7 Komanso, mukadzamva phokoso la nkhondo ndi mbiri za nkhondo, musadzachite mantha. Zimenezi ziyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.+
8 “Pakuti mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndiponso ufumu ndi ufumu wina.+ Kudzakhala zivomezi+ m’malo osiyanasiyana ndiponso kudzakhala njala.+ Zimenezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.+
9 “Koma inu khalani wochenjera. Anthu adzakuperekani kumakhoti aang’ono,+ ndipo adzakukwapulani m’masunagoge+ ndi kukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo.+
10 Komanso, m’mitundu yonse uthenga wabwino+ uyenera ulalikidwe choyamba.+
11 Koma pamene akupita nanu kukakuperekani, musafulumire kuda nkhawa kuti mukanena chiyani.+ Zimene mukapatsidwe mu ola lomwelo, mukanene zimenezo, pakuti wolankhula si inu, koma mzimu woyera.+
12 Komanso, munthu adzapereka m’bale wake ku imfa, ndipo bambo adzapereka mwana wake,+ ndi ana adzaukira makolo awo ndi kuwaphetsa.+
13 Ndipo anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+ Koma amene adzapirire mpaka pa mapeto,+ ndiye amene adzapulumuke.+
14 “Koma mukadzaona chinthu chonyansa+ chosakaza+ chitaimirira pamene sichiyenera kuima (wowerenga adzazindikire),+ pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri.+
15 Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike, kapena kulowa mkati kukatenga chilichonse m’nyumba mwakemo.+
16 Ndipo munthu amene ali m’munda, asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya, kukatenga malaya ake akunja.+
17 Tsoka kwa akazi apakati ndi oyamwitsa ana m’masiku amenewo!+
18 Pitirizani kupemphera kuti zisadzachitike mu nyengo yachisanu.+
19 Pakuti masiku amenewo adzakhala masiku a chisautso+ chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu analenga kudzafika nthawi imeneyo, ndipo sichidzachitikanso.+
20 Kunena zoona, Yehova akanapanda+ kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwawo,+ amene iye anawasankha,+ wafupikitsa masikuwo.+
21 “Komanso pa nthawiyo, munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’+ ‘Onani! Ali uko,’ musadzakhulupirire zimenezo.+
22 Pakuti kudzafika onamizira kukhala Khristu ndiponso aneneri onyenga,+ ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa+ kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse osankhidwawo.+
23 Choncho inuyo khalani ochenjera.+ Ine ndakuuziranitu zinthu zonse.+
24 “Koma m’masiku amenewo, chisautso chimenecho chikadzatha, dzuwa lidzachita mdima, ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake.
25 Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka.+
26 Kenako adzaona Mwana wa munthu+ akubwera m’mitambo ndi mphamvu yaikulu ndiponso ulemerero.+
27 Ndiyeno adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa pamodzi osankhidwa+ ake kuchokera kumphepo zinayi, kuchokera kumalekezero ake a dziko lapansi kukafika kumalekezero a m’mlengalenga.+
28 “Tsopano phunzirani pa fanizo ili la mkuyu: Pamene nthambi yake yanthete yaphuka ndi kuchita masamba, mumadziwa kuti dzinja lili pafupi.+
29 Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zinthu izi zikuchitika, dziwani kuti iye ali pafupi. Dziwani kuti ali pakhomo penipeni.+
30 Ndithu ndikukuuzani kuti m’badwo uwu sudzatha konse, kufikira zinthu zonsezi zitachitika.+
31 Kumwamba+ ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu+ anga sadzachoka ayi.+
32 “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, koma Atate okha.+
33 Khalani maso, khalani tcheru,+ pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.+
34 Zili ngati munthu amene anali kupita kutali kudziko lina,+ amene anasiya nyumba m’manja mwa akapolo ake, aliyense pa ntchito yake, ndi kulamula mlonda wa pachipata kuti azikhala maso.
35 Choncho khalani maso,+ pakuti simukudziwa nthawi yobwera mwininyumba. Simukudziwa ngati adzabwere madzulo, pakati pa usiku, atambala akulira, kapena m’mawa,*+
36 kuti akadzafika mwadzidzidzi, asadzakupezeni mukugona.+
37 Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.”+

