Maliko 4:1-41

4  Tsopano Yesu anayambanso kuphunzitsa m’mphepete mwa nyanja.+ Ndipo chikhamu cha anthu chinasonkhana kwa iye, mwakuti iye anakwera ngalawa n’kupita panyanjapo ndi kukhazikika chapatali pang’ono, koma khamu lonse la anthulo linakhala m’mphepete mwa nyanjayo.+  Atatero anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri+ mwa mafanizo. Powaphunzitsapo anali kuwauza kuti:+  “Tamverani! Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu.+  Pamene anali kufesa, mbewu zina zinagwera m’mbali mwa msewu, ndipo kunabwera mbalame ndi kuzidya.+  Mbewu zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira, ndipo zinamera mwamsanga chifukwa dothilo linali losazama.+  Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinawauka ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.+  Mbewu zina zinagwera paminga, ndipo mingazo zinakula ndi kulepheretsa mbewuzo kukula, moti sizinabale chipatso chilichonse.+  Koma zina zinagwera panthaka yabwino,+ ndipo zinamera ndi kukula, mwakuti zinayamba kubala zipatso. Mbewu ina inabala zipatso 30, ina 60, ndipo ina 100.”+  Kenako anawonjezera mawu akuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+ 10  Tsopano pamene anakhala payekha, ena amene anali naye chapafupi limodzi ndi atumwi 12 aja, anayamba kum’funsa za mafanizo aja.+ 11  Ndipo iye anayamba kuwauza kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira chinsinsi chopatulika+ cha ufumu wa Mulungu. Koma kwa amene ali kunja zonse zimachitika mwa mafanizo,+ 12  kuti kupenya azipenya ndithu, koma osaona, ndi kuti kumva azimva ndithu, koma osazindikira tanthauzo lake, kutinso asatembenuke ndi kukhululukidwa.”+ 13  Komanso anawauza kuti: “Ngati simukumvetsa fanizo ili, ndiye mungamvetse bwanji mafanizo ena onse? 14  “Wofesayo amafesa mawu.+ 15  Chotero anthu amenewa, ndiwo mbewu zimene zimagwera m’mphepete mwa msewu kumene mawu afesedwa. Koma atangomva mawuwo, Satana amabwera+ ndi kuchotsa mawu ofesedwa mwa iwo.+ 16  Momwemonso, pali anthu amene amafesedwa pamiyala. Akangomva mawuwo, iwo amawalandira ndi chimwemwe.+ 17  Amakhala opanda mizu mwa iwo okha, ndipo amapitirizabe kwakanthawi. Koma chisautso kapena mazunzo akangobuka chifukwa cha mawuwo, iwo amapunthwa.+ 18  Ndiyeno palinso mbewu zina zofesedwa paminga. Zimenezi ndiwo anthu amene amamva mawu,+ 19  koma nkhawa+ za m’nthawi* ino, chinyengo champhamvu cha chuma,+ komanso zilakolako+ za zinthu zina, zimalowa ndi kulepheretsa mawuwo kukula, ndipo sabala zipatso.+ 20  Potsirizira pake, zimene zinafesedwa panthaka yabwino, ndiwo anthu amene amamvetsera mawu ndi kuwalandira bwino, ndipo amabala zipatso wina 30, wina 60, ndi wina 100.”+ 21  Tsopano anapitiriza kuwauza kuti: “Nyale saivundikira ndi dengu loyezera zinthu kapena kuiika pansi pa bedi, amatero kodi? Koma amaiika pachoikapo nyale, si choncho kodi?+ 22  Pakuti chilichonse chobisidwa chidzaululika. Chilichonse chimene chimasungidwa mwachinsinsi kwambiri chidzadziwika.+ 23  Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+ 24  Anawauzanso kuti: “Samalani zimene mukumvazi.+ Muyezo umene mukuyezera, nanunso adzakuyezerani womwewo.+ Inde, adzakuwonjezerani zochuluka.+ 25  Pakuti amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka. Koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.”+ 26  Iye anapitiriza kulankhula kuti: “Chotero ufumu wa Mulungu uli ngati mmene munthu amamwazira mbewu panthaka,+ 27  ndipo amagona usiku n’kumadzuka kukacha. Mbewuzo zimamera ndi kukula. Koma mmene zimenezi zimachitikira, mwiniwakeyo sadziwa ayi.+ 28  Pang’onopang’ono, payokha nthaka ija imabala zipatso. Choyamba mmera umabiriwira, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera m’ngalamo. 29  Koma zipatsozo zikacha, iye amamweta ndi chikwakwa, chifukwa nthawi yokolola yakwana.” 30  Iye anapitiriza kuti: “Kodi ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani? Kapena kodi tingaufotokoze ndi fanizo lotani?+ 31  Uli ngati kanjere kampiru,* kamene pa nthawi yofesa kamakhala kakang’ono kwambiri mwa njere zonse za padziko lapansi+ . . . 32  koma akakafesa, kamamera ndi kukula kuposa mbewu zonse zakudimba ndipo kamapanga nthambi zikuluzikulu,+ moti mbalame zam’mlengalenga+ zimatha kupeza malo okhala mumthunzi wake.”+ 33  Chotero anawauza mawu mwa mafanizo ambiri+ oterewa, malinga ndi zimene akanakwanitsa kumva. 34  Ndithudi, sanalankhule nawo chilichonse popanda fanizo, koma kumbali anali kufotokoza zonse kwa ophunzira ake.+ 35  Tsiku limenelo madzulo, iye anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.”+ 36  Choncho atauza khamu la anthulo kuti lizipita, ophunzirawo anachoka naye pa ngalawa imene anakwera ija, koma analinso ndi ngalawa zina.+ 37  Kenako kunayamba chimphepo champhamvu chamkuntho, ndipo mafunde anali kuwomba ngalawayo, mwakuti ngalawayo inangotsala pang’ono kumira.+ 38  Koma Yesu anali kumbuyo kwa ngalawayo akugona, atatsamira pilo. Chotero anam’dzutsa ndi kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi sizikukukhudzani kuti tikufa?”+ 39  Pamenepo anadzuka ndi kudzudzula mphepoyo ndi kuuza nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!”+ Chotero mphepoyo inaleka. Kenako panachita bata lalikulu.+ 40  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi? Kodi mudakali opandiratu chikhulupiriro?” 41  Koma iwo anagwidwa mantha aakulu, ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi ameneyu ndani kwenikweni, chifukwa ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera?”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakang’ono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita anayi ndipo kamachita nthambi.