Maliko 2:1-28

2  Koma patapita masiku angapo, analowanso mu Kaperenao ndipo anthu anamva kuti ali panyumba.+  Choncho anthu ochuluka anasonkhana kumeneko, moti panalibenso malo okhala, chifukwa anthu anadzaza mpaka pakhomo, ndipo anayamba kuwauza uthenga wabwino.+  Tsopano kunafika anthu anayi atanyamula munthu wakufa ziwalo ndi kubwera naye kwa iye.+  Koma popeza kuti sanathe kum’fikitsa kwa Yesu chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, anasasula denga* pamene iye anali, ndipo ataboola padengapo, anatsitsirapo machira a munthu wakufa ziwalo uja.+  Yesu ataona chikhulupiriro chawo,+ anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Mwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+  Tsopano alembi ena anali pomwepo, ndipo anayamba kuganiza m’mitima mwawo kuti:+  “N’chifukwa chiyani munthu ameneyu akulankhula chonchi? Akunyoza Mulungu ameneyu. Ndaninso wina amene angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?”+  Koma nthawi yomweyo Yesu anazindikira mumtima mwake kuti iwo anali kuganiza zimenezo, ndipo anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi m’mitima mwanu?+  Chapafupi n’chiti, kuuza wakufa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo nyamula machira ako uyende’?+ 10  Koma kuti anthu inu mudziwe kuti Mwana wa munthu+ ali ndi mphamvu zokhululukira machimo padziko lapansi,”+ . . . anauza wakufa ziwalo uja kuti: 11  “Ndikunena ndi iwe, Nyamuka, tenga machira akowa, uzipita kwanu.”+ 12  Pamenepo munthuyo anadzuka, ndipo nthawi yomweyo ananyamula machira akewo ndi kuyenda yekha pamaso pa onse,+ moti onsewo anadabwa kwambiri, ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Zoterezi sitinazionepo.”+ 13  Kenako iye anapitanso m’mbali mwa nyanja. Anthu onse anakhamukira kumeneko ndipo anayamba kuwaphunzitsa. 14  Koma pamene anali kudutsa, anaona Levi+ mwana wa Alifeyo, atakhala pansi mu ofesi yokhomera msonkho, ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Pamenepo Levi ananyamuka ndi kumutsatira.+ 15  Pa nthawi ina Yesu anali kudya patebulo m’nyumba ya Levi, ndipo okhometsa msonkho+ ndi ochimwa ambiri anali kudya pamodzi ndi iye ndi ophunzira ake. Kumeneko kunali anthu ambiri ndipo anayamba kumutsatira.+ 16  Koma alembi a Afarisi, ataona kuti iye akudya limodzi ndi anthu ochimwa ndi okhometsa msonkho, anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “Bwanji akudya limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?”+ 17  Yesu atamva zimenezi anawayankha kuti: “Anthu amphamvu safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”+ 18  Ophunzira a Yohane ndi Afarisi anali kusala kudya. Choncho iwo anabwera kwa iye ndi kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma ophunzira anu sasala kudya?”+ 19  Ndipo Yesu anawayankha kuti: “Pamene mkwati ali limodzi ndi anzake, anzake a mkwatiwo sangasale kudya,+ si choncho kodi? Chotero chifukwa chakuti mkwati ali nawo limodzi, sangasale kudya.+ 20  Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya.+ 21  Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Ngati wina atachita zimenezi, mphamvu yonse ya chigambacho imakoka ndi kung’amba malayawo. Chigamba chatsopanocho chimang’amba malaya akalewo, ndipo kung’ambikako kumawonjezeka kwambiri.+ 22  Ndiponso, palibe munthu amene amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa akale. Akachita zimenezo, vinyoyo amaphulitsa matumbawo. Kenako vinyoyo amatayika ndipo matumbawo amawonongeka.+ Koma anthu amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa atsopano.”+ 23  Tsopano nthawi inayake Yesu anali kudutsa m’munda wa tirigu pa tsiku la sabata. Akuyenda, ophunzira ake anayamba kubudula+ ngala za tirigu.+ 24  Pamenepo Afarisi anapita kwa iye n’kumufunsa kuti: “Taonani! N’chifukwa chiyani akuchita zosaloleka pa sabata?”+ 25  Koma Yesu anati: “Kodi simunawerengepo zimene Davide+ pamodzi ndi amuna amene anali naye anachita atamva njala, alibiretu chilichonse?+ 26  M’nkhani yonena za Abiyatara+ wansembe wamkulu, Davide analowa m’nyumba ya Mulungu ndi kudya mitanda ya mkate woonetsa+ kwa Mulungu. Anatenga mitanda ina ya mkatewo n’kupatsanso amuna amene anali naye limodzi.+ Oyenera kudya mkate umenewu ndi ansembe okha basi ndipo anthu ena onse saloledwa kudya.+ Kodi inu simunawerenge nkhani imeneyi?” 27  Chotero anapitiriza kuwauza kuti: “Sabata linakhalako chifukwa cha munthu,+ osati munthu chifukwa cha sabata.+ 28  Choncho Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa sabata.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “tsindwi.”