Pitani ku nkhani yake

Moyo Komanso Imfa

Moyo

Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?

Kodi munayamba mwaganizirapo funso lakuti, ‘Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’ Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Ndizichita Chiyani?

Kodi mukufunika kuona masomphenya kapena chizindikiro chinachake kuti mudziwe zimene Mulungu akufuna kuti muzichita? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe yankho la m’Baibulo.

Kodi Zingatheke Bwanji Kuti Mudzakhale ndi Moyo Wosatha?

Baibulo limalonjeza kuti anthu amene amachita zimene Mulungu amafuna akhoza kudzakhala ndi moyo wosatha. Onani zinthu zitatu zimene Mulungu amafuna kuti tizichita.

Kodi Munthu Akamwalira Mzimu Wake Umapitirizabe Kukhala Ndi Moyo?

Kodi pali chinachake chimene chimakhala mkati mwanu? Kodi sichingafe mutamwalira?

Kodi ndi Mayina a Anthu Otani Amene Amalembedwa “M’buku la Moyo”?

Mulungu walonjeza anthu amene amamumvera kuti adzawakumbukira. Kodi dzina lanu lilimo “m’buku la moyo”?

Imfa

N’chifukwa Chiyani Anthu Amafa?

Yankho limene Baibulo limapereka pa nkhaniyi ndi lolimbikitsa komanso lopatsa chiyembekezo

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

Kodi munthu akamwalira amadziwa zinthu zimene zikuchitika?

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yowotcha Mtembo wa Munthu?

Kodi pali njira zinanso zovomerezeka zomwe tingatsatire pofuna kuika mtembo wa munthu?

Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

Kodi Baibulo limapereka malangizo otani kwa munthu amene akufuna kudzipha?

Kodi Mungatani Kuti Musamaope Kwambiri Imfa?

Kusaopa kwambiri imfa kungakuthandizeni kuti muzisangalala ndi moyo.

Kodi Zimene Anthu Ena Omwe Anatsala Pang’ono Kumwalira Amati Anaona, Zimakhaladi Zenizeni?

Kodi anthu ena akatsala pang’ono kumwalira amaona kumwamba, kumoto kapena kudziko lina? Nkhani ya m’Baibulo yonena za Lazaro ingatithandize kudziwa zoona zake pa nkhaniyi.

Kodi Mulungu Analemberatu Nthawi Yomwe Munthu Adzamwalire?

N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti pali “nthawi yobadwa ndi nthawi ya kufa”?

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yomalizitsa Munthu Amene Akuvutika Kwambiri ndi Ululu?

Bwanji ngati zadziwika kuti munthuyo sachira, kodi pali vuto ndi kutalikitsako moyo wake?

Kumwamba Komanso Kuwotcha Anthu Pamoto

Kodi Mawu Akuti Kumwamba Amatanthauza Chiyani?

Malinga ndi zimene Baibulo limanena, mawuwa amagwiritsidwa ntchito poimira zinthu zitatu.

Kodi Ndi Ndani Amene Amapita Kumwamba?

Anthu ambiri amaganiza kuti anthu onse abwino amapita kumwamba. Koma kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhaniyi?

Kodi Anthu Oipa Akamwalira, Amakawotchedwa Kumoto?

Kodi anthu oipa amakawotchedwa kumoto? Kodi kuwotcha anthu ndi malipiro a uchimo? Werengani mayankho ochokera M’malemba a mafunso amenewa kuti mudziwe zoona.

Kodi Nyanja ya Moto N’chiyani? Kodi ndi Yofanana ndi Gehena?

Yesu ali ndi “makiyi a manda,” koma alibe makiyi a kunyanja ya moto?

Kodi Munthu Wachuma Komanso Lazaro Anali Ndani?

Kodi fanizo limene Yesu anafotokozali limatiphunzitsa kuti anthu abwino amapita kumwamba komanso kuti oipa amakazunzidwa ku moto wa ku gehena?

Kodi Mawu Oti Puligatoliyo Amapezeka M’Baibulo?

Mungadabwe ndi mmene chiphunzitso cha puligatoliyo chinayambira.

Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba?

Baibulo siliphunzitsa kuti ziweto kapena agalu, zidzapita kumwamba

Akufa Adzauka

Kodi Mawu Akuti Kuuka kwa Akufa Amatanthauza Chiyani?

Mungadabwe mutadziwa zimene Baibulo limanena zokhudza anthu amene adzaukitsidwe.