Pitani ku nkhani yake

Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?

Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Anthu ambiri amafuna kudziwa mayankho amafunso ukhudza moyo. Amatha kufunsa kuti, “N’chifukwa chiyani tili padzikoli”? Kapena, “Kodi moyo wangawu uli ndi cholinga chilichonse”? Baibulo limasonyeza kuti cholinga cha moyo wathu ndi kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Taonani mfundo zoona zotsatirazi zimene Baibulo limaphunzitsa.

  •   Mulungu ndi Mlengi wathu. Baibulo limanena kuti: “Iye [Mulungu] ndi amene anatipanga, sitinadzipange tokha.”—Salimo 100:3; Chivumbulutso 4:11.

  •   Zinthu zonse zimene Mulungu anazilenga, kuphatikizapo ifeyo, ali nazo cholinga.—Yesaya 45:18.

  •   Mulungu anatilenga mwanjira yakuti tizitha kuzindikira zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu zomwe zikuphatikizapo kufuna kudziwa cholinga cha moyo. (Mateyu 5:3) Iye akufuna kuti tidziwe cholinga cha moyo wathu.—Salimo 145:16.

  • Timasonyeza kuti tikuzindikira zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu tikamayesetsa kukhala paubwenzi ndi Mulungu. Ngakhale kuti ena angaone ngati n’zosatheka kuti anthufe tikhale paubwenzi ndi Mulungu, Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8; 2:23.

  •   Kuti tikhale paubwenzi ndi Mulungu, tiyenera kumachita zinthu zimene iye amafuna. Baibulo limanena zimene Mulungu amafuna kuti tizichita palemba la Mlaliki 12:13. Lembali limati: “Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.”

  •   M’tsogolomu, Mulungu adzapereka moyo wosatha wopanda mavuto alionse kwa anthu amene akumulambira ndipo ali naye paubwenzi wabwino. Mulungu adzachita zimenezi chifukwa ndi cholinga chimene anali nacho poyambirira pamene ankalenga anthu.—Salimo 37:10, 11.