Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Ndizichita Chiyani?

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Ndizichita Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Mulungu amafuna kuti muzimudziwa bwino, kukhala naye pa ubwenzi, kumukonda ndiponso kumutumikira ndi mtima wanu wonse. (Mateyu 22:37, 38; Yakobo 4:8) Mungadziwe mmene mungachitire zimene Mulungu amafuna mukamaphunzira zimene Yesu ankachita ndiponso kuphunzitsa. (Yohane 7:16, 17) Yesu sankangouza anthu zimene Mulungu amafuna koma ankazichita. Iye ananena kuti cholinga chake chachikulu chinali ‘kuchita chifuniro cha amene anamutuma, osati chifuniro chake.’—Yohane 6:38.

Kodi ndifunika kuona masomphenya kapena chizindikiro chinachake kuti ndidziwe zimene Mulungu akufuna kuti ndizichita?

 Ayi. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo limatiuza zimene Mulungu amafuna. Baibulo lili ndi zimene mumafunikira kuti mukhale “wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Mulungu amafuna kuti muzigwiritsa ntchito Baibulo ndiponso “luntha la kuganiza” kuti muphunzire zimene akufuna kuti muzichita.—Aroma 12:1, 2; Aefeso 5:17.

Kodi ndingakwanitsedi kuchita zimene Mulungu amafuna?

 Inde mungakwanitse chifukwa Baibulo limati: “Malamulo [a Mulungu] ndi osalemetsa.” (1 Yohane 5:3) Koma izi sizikutanthauza kuti kutsatira malamulo a Mulungu n’kophweka nthawi zonse. Ngakhale zili choncho, tikamawatsatira, zinthu zimatiyendera bwino kwambiri. Yesu anati: “Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”—Luka 11:28.