KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO
Yeremiya 29:11—“Ndikudziwa Bwino Zimene Ndikuganiza Zokhudza Inu”
“‘Ndikudziwa bwino zimene ndikuganiza zokhudza inu. Ndikuganiza zokupatsani mtendere osati masoka ndiponso zokupatsani tsogolo labwino ndi chiyembekezo chabwino,’ akutero Yehova.” a—Yeremiya 29:11, Baibulo la Dziko Latsopano.
“‘Ndikudziwa zolinga zomwe ndili nazo zokhudza inu,’ akutero AMBUYE, ‘zolinga zokupatsani ulemerero osati zokuwonongani, zolinga zokupatsani chiyembekezo komanso tsogolo.’”—Yeremiya 29:11, New International Version.
Tanthauzo la Yeremiya 29:11
Yehova Mulungu analonjeza atumiki ake kuti adzawathandiza kukhala ndi tsogolo labwino. Ngakhale kuti mawu amenewa analembera atumiki ake akale, akusonyezanso maganizo amene Mulungu ali nawo masiku ano. Iye ndi “Mulungu amene amapereka chiyembekezo.” (Aroma 15:13) Ndipotu anaonetsetsa kuti malonjezowa alembedwe m’Baibulo, “nʼcholinga choti tikhale ndi chiyembekezo” komanso tsogolo labwino.—Aroma 15:4.
Nkhani yonse ya Yeremiya 29:11
Mawu amenewa anali mbali ya kalata yopita kwa Aisiraeli omwe anatengedwa ukapolo kuchoka ku Yerusalemu kupita ku Babulo. b (Yeremiya 29:1) Mulungu anauza Aisiraeli omwe anali kuukapolowo kuti adzakhala kumeneko kwa nthawi yaitali ndipo ankayenera kumanga nyumba, kulima minda komanso kukwatira n’kukhala ndi ana. (Yeremiya 29:4-9) Komabe, Mulungu ananenanso kuti: “Zaka 70 zikadzakwana muli ku Babulo, ndidzakusamalirani ndipo ndidzakwaniritsa lonjezo langa pokubwezeretsani kumalo ano [ku Yerusalemu].” (Yeremiya 29:10) Apatu Mulungu anawatsimikizira kuti sadzawaiwala komanso kuti chiyembekezo choti adzabwerera kwawo chidzakwaniritsidwa.—Yeremiya 31:16, 17.
Mulungu anachitadi zimene analonjeza Aisiraeli. Mogwirizana ndi zimene iye ananeneratu, mzinda wa Babulo unagonjetsedwa ndi Koresi, mfumu ya Perisiya. (Yesaya 45:1, 2; Yeremiya 51:30-32) Zitatero, Koresi analola kuti Ayuda abwerere kudziko lakwawo. Choncho, pambuyo pokhala kuukapolo kwa zaka 70, Ayuda anabwerera kwawo ku Yerusalemu.—2 Mbiri 36:20-23; Ezara 3:1.
Kukwaniritsidwa kwa lonjezo la pa Yeremiya 29:11, kumathandiza anthu amene amakhulupirira malonjezo a Mulungu masiku ano. Limodzi mwa malonjezowa ndi lonena za mtendere umene udzakhale padziko lonse mu Ufumu wa Mulungu, womwe mfumu yake ndi Yesu Khristu.—Salimo 37:10, 11, 29; Yesaya 55:11; Mateyu 6:10.
Maganizo Olakwika Okhudza Yeremiya 29:11
Maganizo olakwika: Mulungu anakonzeratu zokhudza munthu wina aliyense.
Zoona zake: Mulungu amalola kuti anthu azisankha zimene akufuna kuchita pa moyo wawo. Mawu a pa Yeremiya 29:11, ankapita kwa gulu lonse la Aisiraeli omwe anali ku Babulo ndipo Mulunguyo ankaganizira zodzawapatsa mtendere. (Yeremiya 29:4) Komabe, iye ankalola kuti munthu wina aliyense payekha asankhe ngati akufuna kudzapindula ndi malonjezowo kapena ayi. (Deuteronomo 30:19, 20; Yeremiya 29:32) Anthu amene anasankha kufunafuna Mulungu ankapemphera mochokera pansi pa mtima.—Yeremiya 29:12, 13.
Maganizo olakwika: Ulemerero umene Mulungu adzapatse atumiki ake, ndi chuma.
Zoona zake: Mawu akuti “ulemerero,” omwe amapezeka m’Mabaibulo ena pa Yeremiya 29:11, anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chiheberi omwe amatanthauza “mtendere, moyo wathanzi komanso moyo wabwino.” Nkhani yonse yokhudza vesili ikusonyeza kuti Mulungu analonjeza Aisiraeli omwe anali kuukapolo kuti adzawapatsa mtendere komanso moyo wabwino osati chuma. Anawatsimikizira kuti mtundu wawo sudzatha ndipo tsiku lina adzabwerera kwawo ku Yerusalemu.—Yeremiya 29:4-10.
Werengani Yeremiya chaputala 29, mawu a m’munsi ofotokozera tanthauzo la vesilo komanso malifalensi ake.
a Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.
b Ponena za Yeremiya 29:11, Baibulo lina linanena kuti: “Ili ndi limodzi mwa malonjezo abwino kwambiri opezeka m’Malemba amene akufotokoza chifundo chomwe Yahweh [Yehova] anasonyeza anthu omwe anali kuukapolo, n’kuwathandiza kukhala ndi chiyembekezo.”—The Expositor’s Bible Commentary, Volume 7, tsamba 360.

