Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

Yankho la m’Baibulo

 Inde. Baibulo linachokera kwa “Mulungu, amene amalimbikitsa osautsika mtima.” (2 Akorinto 7:6) Ngakhale kuti si buku lothandiza anthu ovutika maganizo, Baibulo lathandiza anthu ambiri omwe anali ndi maganizo ofuna kudzipha. Ndipo malangizo ake angakuthandizeninso inuyo.

 Kodi Baibulo limapereka malangizo otani pa nkhaniyi?

 • Muziuza ena mmene mukumvera.

   Zimene Baibulo limanena: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

   Mfundo yake: Tonsefe timafuna kuti anthu ena atithandize tikakumana ndi mavuto.

   Ngati simungauze anzanu mmene mukumvera, zimakhala ngati mwanyamula chimwala cholemera ndipo simukufuna kuchitula pansi. Koma mukawafotokozera, zimakhala ngati mwachitula ndipo zinthu zimayamba kukuyenderani bwino.

   Tayesani izi: Fotokozani mmene mukumvera kwa munthu wina lero, mwina wa m’banja lanu kapena mnzanu amene mumadalira. a Kapenanso mungalembe papepala mmene mukumvera.

 • Kaonaneni ndi dokotala.

   Zimene Baibulo Limanena: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—Mateyu 9:12.

   Mfundo yake: Tikadwala, tiziyesetsa kupeza thandizo la kuchipatala.

   Ngati munthu akufuna kudzipha, chikhoza kukhala chizindikiro cha matenda ovutika maganizo. Choncho, musamachite manyazi kukumana ndi dokotala ngati mmene mumachitira mukadwala matenda ena alionse. Ndipotu n’zotheka kuchira matenda ovutika maganizo.

   Tayesani izi: Kaonaneni ndi dokotala wodziwa ntchito kuti akuthandizeni mofulumira.

 • Muzikumbukira kuti Mulungu amakuwerengerani.

   Zimene Baibulo limanena: “Mpheta zisanu amazigulitsa makobidi awiri ochepa mphamvu, si choncho kodi? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imene imaiwalika kwa Mulungu. . . . Musachite mantha. Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.”—Luka 12:6, 7.

   Mfundo yake: Yehova amaona kuti ndinu wofunika kwambiri.

   Mukhoza kuganiza kuti palibe amene amakuganizirani, koma Mulungu amadziwa mavuto onse omwe mukukumana nawo. Iye amakukondani ngakhale mutayamba kuganiza kuti simukufunanso kukhala ndi moyo. Lemba la Salimo 51:17 limanena kuti: “Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika.” Izi zikusonyeza kuti Mulungu amafuna kuti mukhalebe ndi moyo chifukwa choti amakukondani.

   Tayesani izi: Fufuzani m’Baibulo kuti muone umboni wakuti Mulungu amakukondani. Mwachitsanzo, werengani mutu 24 m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova.

 • Muzipemphera kwa Mulungu.

   Zimene Baibulo limanena: ‘Mutulireni [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.

   Mfundo yake: Mulungu akukupemphani kuti muzimasuka kumuuza chilichonse chimene chikukudetsani nkhawa.

   Mulungu akhoza kukupatsani mtendere wa mumtima komanso mphamvu kuti muthe kupirira mavuto amene mukukumana nawo. (Afilipi 4:6, 7, 13) Mulungu amagwiritsa ntchito njira imeneyi pothandiza anthu omwe akumupempha kuti awathandize.—Salimo 55:22.

   Tayesani izi: Pempherani kwa Mulungu lero. Mugwiritse ntchito dzina lake lakuti Yehova ndipo muuzeni mmene mukumvera. (Salimo 83:18) Mupempheni kuti akuthandizeni kupirira.

 • Muziganizira zinthu zabwino zimene Baibulo limatilonjeza.

   Zimene Baibulo limanena: “Chiyembekezo chimene tili nachochi chili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika.”—Aheberi 6:19.

   MMfundo yake: Maganizo athu akhoza kusokonezeka ngati mmene imachitira sitima yomwe yakumana ndi chimphepo pamadzi, koma zinthu zabwino zimene Baibulo limatilonjeza zingathandize kuti maganizowo akhale m’malo.

   Zimene tikuyembekezerazi si nkhambakamwa chabe, koma ndi zimene Mulungu watilonjeza.—Chivumbulutso 21:4.

   Tayesani izi: Werengani nkhani zina zokhudza zimene Baibulo limatilonjeza mu phunziro 5 la kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu.

 • Muzichita zinthu zomwe zimakusangalatsani.

   Zimene Baibulo limanena: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.”—Miyambo 17:22.

   Mfundo yake: Tikamachita zinthu zomwe timakonda, timakhala osangalala ndiponso timakhala ndi thanzi labwino.

   Tayesani izi: Muzichita zinthu zomwe mumati mukazichita mumamva bwino. Mwachitsanzo, kumvera nyimbo zabwino, kuwerenga nkhani inayake yolimbikitsa kapena kuchita masewera enaake omwe amakusangalatsani. Mukhozanso kumakhala osangalala mukamathandiza ena, ngakhale pa zinthu zing’onozing’ono.—Machitidwe 20:35.

 • Muzisamalira thanzi lanu.

   Zimene Baibulo limanena: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”—1 Timoteyo 4:8.

   Mfundo yake: Zinthu zimatiyendera bwino tikamachita masewera olimbitsa thupi, kugona mokwanira komanso kudya chakudya chopatsa thanzi.

   Tayesani izi: Konzani kaulendo koti mungowongolako miyendo mwina kwa 15 minitsi yokha.

 • Muzikumbukira kuti zinthu zimatha kusintha.

   Zimene Baibulo limanena: “Simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.”—Yakobo 4:14.

   Mfundo yake: Zinthu zimene zikukudetsani nkhawa panopa, ngakhale zimene zikuoneka kuti simungathe kuzithetsa, zikhoza kukhala kuti n’zakanthawi chabe.

   Ngakhale mutapanikizika kwambiri panopa, dziwani kuti nthawi ina zinthu zidzayenda. Choncho muzipeza njira yomwe ingakuthandizeni kupirira. (2 Akorinto 4:8) Nthawi ikamapita zinthu zimatha kukhalanso m’malomwake, koma ngati mutadzipha, basi mwafa.

   Tayesani izi: Werengani nkhani za anthu a m’Baibulo omwe anafooka mpaka kuyamba kuganiza zoti afe. Ndipo onani mmene zinthu zinasinthira pamoyo wawo n’kuyamba kuyenda bwino, ngakhale kuti sankayembekezera kuti zinthu zingasinthe. Taganizirani zitsanzo zotsatirazi.

 Kodi Baibulo limatchula za anthu omwe ankalakalaka atafa?

 Inde. Baibulo limafotokoza za anthu ena omwe anali ndi maganizo ofuna kufa. Mulungu sanawadzudzule, koma anawathandiza. Ndipotu akhoza kuchitanso zomwezo kwa inuyo.

Eliya

 •  Kodi anali ndani? Eliya anali mneneri wolimba mtima. Koma nthawi ina nayenso anafooka. Lemba la Yakobo 5:17 limanena kuti: “Eliya anali munthu monga ife tomwe.”

 •  N’chifukwa chiyani ankalakalaka atafa? Pa nthawi ina Eliya ankadziona kuti watsala yekhayekha, anali ndi nkhawa ndiponso ankadziona kuti ndi wosafunika. Ndiyeno anapempha kuti: “Chotsani moyo wanga Yehova.”—1 Mafumu 19:4.

 •  N’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe maganizo akewa? Eliya anafotokozera Mulungu mmene ankamvera. Nanga Mulungu anamulimbikitsa bwanji? Mulungu anasonyeza kuti anakhudzidwa nazo ndipo anamuonetsa zinthu zosonyeza kuti Iye ndi wamphamvu. Anamutsimikiziranso kuti adakali munthu wofunika ndipo anamupatsa munthu wabwino komanso wachikondi woti azimuthandiza.

 •  Werengani nkhani ya Eliya: 1 Mafumu 19:2-18.

Yobu

 •  Kodi anali ndani? Anali munthu wolemera, anali ndi banja lalikulu ndipo ankatumikira Mulungu woona mokhulupirika.

 •  N’chifukwa chiyani ankalakalaka atafa? Mwadzidzidzi, Yobu anakumana ndi mavuto ambiri motsatizana. Katundu wake yense anabedwa komanso kuwonongeka. Ana ake onse anafa nyumba itawagwera. Iyeyo anadwala matenda opweteka kwambiri. Ndipo pamapeto pake, anzake anamukhumudwitsa kwambiri pomunena kuti mavuto amene akukumana nawowo anachita kuwaputa dala. Yobu ananena kuti: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”—Yobu 7:16.

 •  N’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe maganizo akewa? Yobu anapemphera kwa Mulungu ndiponso anafotokozera anthu ena mavuto akewo. (Yobu 10:1-3) Analimbikitsidwa ndi mnzake wina dzina lake Elihu, yemwe anali wachikondi ndipo anamuthandiza kuona mavuto akewo moyenera. Koma chofunika kwambiri n’chakuti, Yobu anamvera malangizo amene Mulungu anamupatsa.

 •  Werengani nkhani ya Yobu: Yobu 1:1-3, 13-22; 2:7; 3:1-13; 36:1-7; 38:1-3; 42:1, 2, 10-13.

Mose

 •  Kodi anali ndani? Mose anali mtsogoleri wa Aisiraeli ndiponso anali mneneri wokhulupirika.

 •  N’chifukwa chiyani ankalakalaka atafa? Mose ankapanikizika chifukwa cha udindo waukulu, anthu ankangokhalira kumunyoza, mpaka anafika potopa nazo. Chifukwa cha zimenezi, anadandaulira Mulungu kuti: “Ingondiphani.”—Numeri 11:11, 15.

 •  N’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe maganizo akewa? Mose anafotokozera Mulungu mmene ankamvera. Ndipo Mulungu anamuthandiza pomuchepetsera ntchito yake kuti asamapanikizike.

 •  Werengani nkhani ya Mose: Numeri 11:4-6, 10-17..

a Ngati mukuona kuti maganizo ofuna kudzipha akukulabe koma palibepo aliyense oti angakuthandizeni, imbirani foni anthu amene anaphunzitsidwa ntchito yothandiza anthu ovutika maganizo ngati alipo m’dera lanu.