Pitani ku nkhani yake

Kodi Zimene Anthu Ena Omwe Anatsala Pang’ono Kumwalira Amati Anaona, Zimakhaladi Zenizeni?

Kodi Zimene Anthu Ena Omwe Anatsala Pang’ono Kumwalira Amati Anaona, Zimakhaladi Zenizeni?

Yankho la m’Baibulo

 Anthu ambiri amene anatsala pang’ono kumwalira amanena kuti akukumbukira zoti moyo wawo unachoka m’thupi lawo, kapenanso kuti anaona kuwala kwambiri mwinanso anaona malo okongola kwambiri. Pa nkhaniyi, buku lina linati: ‘Anthu ena amati umenewu ndi mwayi wapadera woti aoneko pang’ono chabe ulemerero wa kudziko lina osati lapansili.’ (Recollections of Death) Ngakhale kuti m’Baibulo mulibe nkhani yosonyeza kuti munthu akatsala pang’ono kumwalira amaona masomphenya a kumoyo wina, koma muli mfundo zofunika kwambiri zosonyeza kuti zimene anthu amati amaonazo si zoona.

 Akufa sadziwa kanthu.

Baibulo limati “akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Munthu akafa sikuti amasamukira kudziko kapena kumoyo wina, koma sakhalaponso. Zimene anthu ena amaphunzitsa zakuti anthufe tili ndi mzimu umene sufa tikamwalira, n’zosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena. (Ezekieli 18:4) Choncho, zimene munthu anganene kuti anaona, sizingakhale kumwamba, kumoto kapena kudziko lina kumene anthu ena amati munthu akamwalira amapitako.

 Kodi Lazaro ananena kuti anapita kumoyo wina atamwalira?

Nkhani ya m’Baibulo yonena za Lazaro imafotokoza zimene zimachitikadi munthu akamwalira. Iye anaukitsidwa ndi Yesu patapita masiku 4 atamwalira. (Yohane 11:​38-44) Zikanakhala kuti Lazaro atamwalira anapita kudziko lina n’kumakasangalala, ndiye kuti zimene Yesu anachita pomuukitsa kuti akhalenso ndi moyo padziko lapansili zikanakhala nkhanza. Ndipotu Baibulo silinena chilichonse chosonyeza kuti Lazaro ataukitsidwa anafotokoza za moyo umene anali nawo kudziko lina atamwalira padziko lapansili. Zikanakhala kuti anapitadi kudziko lina, n’zachidziwikire kuti Lazaro akananena zimenezo. Komanso n’zochititsa chidwi kuti Yesu ananena kuti Lazaro atamwalira zinali ngati ali m’tulo, kusonyeza kuti Lazaroyo sankadziwa chilichonse.​—Yohane 11:​11-14.