Pitani ku nkhani yake

Kodi Malamulo Khumi a Mulungu Ndi Chiyani?

Kodi Malamulo Khumi a Mulungu Ndi Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Malamulo Khumi ndi mndandanda wa malamulo omwe Mulungu anapereka kwa Aisiraeli. Malamulowa amadziwikanso kuti Mawu 10 ndipo anachokera ku mawu a Chiheberi. (ʽaseʹreth had·deva·rimʹ) Mawu akuti “Mawu 10,” amapezeka katatu m’mabuku 5 oyambirira a Baibulo omwe amadziwikanso kuti Tora. (Ekisodo 34:28; Deuteronomo 4:13; 10:4) M’Chigiriki mawu akuti “Decalougue” omwe anapangidwa kuchokera ku mawu akuti de’ka, omwe amatanthauza 10, komanso mawu akuti lo’gous omwe amatanthauza “mawu.”

Mulungu analemba Malamulo Khumi pamiyala iwiri n’kuwapereka kwa mneneri Mose, ali paphiri la Sinai. (Ekisodo 24:12-18) Malamulowa, amapezeka pa Ekisodo 20:1-17 ndi pa Deuteronomo 5:6-21.

 Mndandanda wa Malamulo Khumi

  1. Uzilambira Yehova Mulungu yekha.​—Ekisodo 20:3.

  2. Usamapembedze mafano.​—Ekisodo 20:4-6.

  3. Usamagwiritse ntchito dzina la Mulungu mosasamala.​—Ekisodo 20:7.

  4. Uzisunga Sabata.​—Ekisodo 20:8-11.

  5. Uzilemekeza makolo ako.​—Ekisodo 20:12.

  6. Usaphe.​—Ekisodo 20:13.

  7. Usachite chigololo.​—Ekisodo 20:14.

  8. Usabe.​—Ekisodo 20:15.

  9. Usamapereke umboni wabodza.​—Ekisodo 20:16.

  10. Usamasilire.​—Ekisodo 20:17.

 N’chifukwa chiyani mndandanda wa Malamulo Khumi umasiyana?

Baibulo silinaike manambala ku malamulowa. Choncho anthu samvana chimodzi pa nkhani yakuti malamulowa ayenera kusanjidwa bwanji. Mndandanda womwe uli pamwambawo ukusonyeza mmene malamulowa amasanjidwira nthawi zambiri. Komabe, ena amasanja malamulowa mosiyanako. Anthuwa amasemphana maganizo kuti ndi lamulo liti lomwe liyenera kukhala loyamba, lachiwiri komanso lomaliza. *

 Kodi cholinga cha Malamulo Khumi chinali chiyani?

Malamulo Khumi amenewa anali mbali ya Chilamulo cha Mose. M’chilamulochi munalinso malamulo ena oposa 600, okhudza mgwirizano kapena mapangano omwe analipo pakati pa Mulungu ndi Aisiraeli. (Ekisodo 34:27) Mulungu analonjeza Aisiraeli kuti zinthu zidzawayendera bwino akamatsatira Chilamulo cha Mose. (Deuteronomo 28:​1-​14) Komabe cholinga chachikulu cha Chilamulochi chinali kukonzekeretsa Aisiraeli, za kubwera kwa Khristu yemwe anali Mesiya wolonjezedwa.​—Agalatiya 3:​24.

 Kodi Akhristu ayenera kutsatira Malamulo Khumi?

Ayi. Mulungu anapereka Chilamulo, kuphatikizapo Malamulo Khumi kwa mtundu wa Aisiraeli okha. (Deuteronomo 5:​2, 3; Salimo 147:19, 20) Chilamulo cha Mose sichikukhudza Akhristu. Ndipotu nawonso Akhristu Achiyuda ‘anamasulidwa ku Chilamulocho.’ (Aroma 7:6) * Chilamulo cha Mose chinalowedwa m’malo ndi “chilamulo cha Khristu,” chomwe chimaphatikizapo zonse zomwe Yesu anaphunzitsa otsatira ake.​—Agalatiya 6:2; Mateyu 28:19, 20.

 Kodi mfundo za m’Malamulo Khumi ndi zothandizabe masiku ano?

Inde. Malamulo Khumi amenewa amatithandiza kudziwa mmene Mulungu amaonera zinthu. Choncho tikamawaphunzira, akhoza kutithandiza kwambiri. (2 Timoteyo 3:​16, 17) Malamulo Khumi anachokera ku mfundo zodalirika zomwe sizidzasiya kugwira ntchito. (Salimo 111:7, 8) Ndipotu ziphunzitso za m’Chipangano Chatsopano zinachokera ku mfundo zomwe zinkapezeka m’Chilamulo.​—Onani mbali yakuti “ Mfundo za m’Malamulo Khumi zomwe zimapezeka m’Chipangano Chatsopano.”

Yesu anaphunzitsa kuti Chilamulo chonse cha Mose kuphatikizapo Malamulo Khumi zinagona pa malamulo awiri akuluakulu. Iye anati: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa, kuphatikizaponso Zolemba za aneneri.” (Mateyu 22:34-​40) Ndiye ngakhale kuti Akhristu sayenera kusunga Chilamulo cha Mose, amalamulidwa kukonda Mulungu komanso anzawo.​—Yohane 13:34; 1 Yohane 4:​20, 21.

  Mfundo za m’Malamulo Khumi zomwe zimapezeka m’Chipangano Chatsopano

Mfundo

Pomwe Imapezeka m’Chipangano Chatsopano

Muzilambira Yehova Mulungu yekha

Chivumbulutso 22:8, 9

Musamapembedze mafano

1 Akorinto 10:14

Muzilemekeza dzina la Mulungu

Mateyu 6:9

Muzisonkhana nthawi zonse

Aheberi 10:24, 25

Muzilemekeza makolo anu

Aefeso 6:1, 2

Musaphe munthu

1 Yohane 3:15

Musamachite chigololo

Aheberi 13:4

Musamabe

Aefeso 4:28

Musamapereke umboni wabodza

Aefeso 4:25

Musamasirire mwansanje

Luka 12:15

^ ndime 23 Pa chikhalidwe Chachiyuda, amaona kuti mawu oyamba a pa “Ekisodo chaputala 2, ngati lamulo loyamba ndipo a pavesi 3 mpaka 6 ngati lamulo limodzi lomwe amati ndi lachiwiri.” (The Jewish Encyclopedia) Komanso achipembedzo cha Chikatolika amaona kuti mawu a pa Ekisodo chaputala 20:1-6 ndi lamulo limodzi ndipo amaona kuti lachiwiri lake ndi loletsa kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu molakwika. Pofuna kuti malamulowo akwane 10, amagawa lamulo lomaliza lomwe limanena za kusilira mkazi komanso katundu wa mwiniwake, ngati malamulo awiri osiyana.

^ ndime 27 Palemba la Aroma 7:7, anagwiritsa ntchito lamulo lomwe likupezeka pa nambala 10 ngati chitsanzo cha “Chilamulo.” Zimenezi zikusonyeza kuti Chilamulo cha Mose chinalidi ndi Malamulo Khumi.