Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZITSANI ANA ANU

Zimene Timachita Zikhoza Kukhumudwitsa Mulungu—Kodi Tingatani Kuti Tizimusangalatsa?

Zimene Timachita Zikhoza Kukhumudwitsa Mulungu—Kodi Tingatani Kuti Tizimusangalatsa?

Kodi unalirapo chifukwa chakuti winawake wakukhumudwitsa? * Aliyense zimenezi zinamuchitikirapo ndipo nthawi zina tikakhumudwa timalira. Mwachitsanzo, munthu wina akhoza kutinenera zabodza. Zimenezi zingakhale zopweteka eti?— Mulungunso amamva kupweteka mumtima anthu akamamunenera zabodza. Tiye tikambirane nkhani imeneyi kuti tione zimene tingachite kuti tizisangalatsa Mulungu osati kumukhumudwitsa.

Baibulo limanena kuti anthu ena amene ankanena kuti amakonda Mulungu “anali kumukhumudwitsa.” Izi zikutanthauza kuti “anamvetsa chisoni” Mulungu. Tiye tikambirane chifukwa chake Mulungu amakhumudwa tikapanda kuchita zimene iye amafuna.

Anthu awiri oyambirira amene Yehova anawalenga anamukhumudwitsa kwambiri. Mulungu anaika anthuwa ‘m’munda wa Edeni’ womwe unali Paradaiso. Kodi mayina awo anali ndani?— Woyamba kulengedwa anali Adamu kenako Hava. Tiye tione zimene anachita zomwe zinakhumudwitsa Yehova.

Yehova atawaika m’munda wa Edeni, anawauza kuti aziusamalira. Anawauzanso kuti akhale ndi ana kuti azisangalala nawo limodzi m’mundamo mpaka kalekale. Koma Adamu ndi Hava asanabereke ana, zinthu zinasokonekera kwambiri. Kodi ukudziwa chimene chinachitika?— Mngelo ananyengerera Hava komanso Adamu kuti asamvere Yehova. Tiye tione mmene zimenezi zinachitikira.

Mngeloyo anachititsa kuti njoka izikhala ngati ikulankhula. Hava anakopeka ndi zimene njokayo inamuuza zoti ‘adzafanana ndi Mulungu’ ndipo anachita zimene njokayo inamuuza. Kodi ukudziwa zimene njokayo inamuuza kuti achite?

 Hava anadya chipatso cha mtengo umene Yehova anawauza kuti asadye. Mulungu asanalenge Hava, anauza Adamu kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.”

Hava ankadziwa lamulo limeneli. Koma chifukwa chakuti anapitiriza kuyang’ana mtengowo “anayamba kuona kuti zipatso za mtengowo n’zokoma kudya [komanso] zokhumbirika . . . Choncho anathyola chipatso cha mtengowo n’kudya.” Kenako anatenga chipatsocho n’kupatsa Adamu ndipo “nayenso anadya.” Kodi ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Adamu anadya chipatsocho?— Adamu anachita zimenezi chifukwa ankakonda kwambiri Hava kuposa Yehova. Anasankha dala kusangalatsa Hava m’malo mosangalatsa Mulungu. Kumvera Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kumvera munthu aliyense.

Kodi ukukumbukira za njoka imene inalankhula ndi Hava ija? Anthu amatha kupangitsa chidole kuti chizioneka ngati chikulankhula koma amene amakhala akulankhula ndi munthuyo. N’chimodzimodzinso ndi njokayi. Winawake anaipangitsa kuti izioneka ngati ikulankhula. Kodi ndi ndani amene ankalankhula kudzera mwa njokayo?— Inali “njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.”

Kodi ukudziwa zimene uyenera kuchita kuti uzisangalatsa Yehova?— Ungamusangalatse ngati utamamvera zimene amanena nthawi zonse. Satana amanena kuti akhoza kuchititsa aliyense kusamvera Mulungu. Choncho Yehova akutipempha kuti: “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.” Satana amatonza Yehova. Amanena kuti akhoza kuchititsa aliyense kuti asatumikire Mulungu. Choncho ungasangalatse Yehova ngati utamamvera zimene amanena ndiponso ngati ukumutumikira. Kodi uyesetsa kumamvera komanso kutumikira Yehova?

^ ndime 3 Ngati mukuwerengera mwana nkhaniyi, mukapeza mzera muime kaye ndi kumulimbikitsa kuti anenepo maganizo ake.