Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO: N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU AKUVUTIKA CHONCHI? NANGA MAVUTO AMENEWA ADZATHA LITI?

Anthu Ambiri Osalakwa Akuphedwa

Anthu Ambiri Osalakwa Akuphedwa

Noelle anali mwana wosangalatsa ndipo ankakonda kujambula. Tsiku lina madzulo ankayenda kuseri kwa nyumba yawo ndipo mwangozi anagwera mu damu la pakhomopo n’kumwalira. Zimenezi zinachitika kutangotsala milungu iwiri kuti akwanitse zaka 4.

Pa 14 December 2012, anthu 26 anafa atawomberedwa ndi mfuti pa sukulu ina ku Connecticut, ku America, ndipo 20 mwa anthuwa anali ana azaka 6 kapena 7. Ena mwa anawa mayina awo anali Charlotte, Daniel, Olivia ndi Josephine. Pa mwambo wokumbukira imfa ya anthuwa, pulezidenti Obama anatchula mayina a anawo kenako anauza anthu amene anapezeka pamwambowo kuti: “Mavuto amenewa ayenera kutha.”

Mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Bano, anasamuka limodzi ndi banja lawo ku Iraq mu 1996 kupita ku Norway. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti Bano anali m’gulu la anthu 77, omwe anaphedwa pa 22 July 2011 ndi chigawenga china. Chigawengachi chinalankhula moyerekedwa kuti: “Ndikufuna ndipepese kuti sindinakwanitse kupha anthu ambiri.”

Nkhani zomvetsa chisoni ngati zimenezi zakhala zikuchitika kawirikawiri m’madera osiyanasiyana padziko lapansi. Taganizirani za chisoni chimene anthu amakhala nacho kukachitika ngozi, zachiwawa, nkhondo, zauchigawenga ndiponso zinthu zina. Anthu ambiri osalakwa amaphedwa kapena kuvulala.

Zimenezi zikachitika, anthu ena amaimba Mulungu mlandu. Iwo amati Mlengi wathu samakhudzidwa ndi mavuto amene anthu akukumana nawo. Ena amati Mulungu amaona mavuto amene anthu akukumana nawo koma safuna kuwathandiza. Pomwe ena amati Mulungu analemberatu kuti zinthu zimenezi zidzachitike. Zikuoneka kuti anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Kodi mayankho odalirika tingawapeze kuti? Nkhani zotsatirazi zifotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mavuto komanso mmene adzathere.