Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Akukumana ndi Mavuto Onsewa?

N’chifukwa Chiyani Anthu Akukumana ndi Mavuto Onsewa?

Kuti timvetse chifukwa chake anthu akukumana ndi mavuto ambiri chonchi ndiponso chifukwa chake anthu akulephera kuwathetsa, tikufunika kudziwa chomwe chimayambitsa mavutowa. Ngakhale kuti zifukwa zimene zimayambitsa mavutowa ndi zosiyanasiyana komanso zovuta kuzimvetsa, Baibulo limatithandiza kuti tizidziwe. M’nkhaniyi tikambirana zifukwa 5 zikuluzikulu zomwe zikuchititsa kuti padzikoli pakhale mavuto ambiri. Tikukupemphani kuti muwerenge mofatsa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi kuti mudziwe zoti Mawu a Mulungu amatithandiza kumvetsa chenicheni chomwe chimayambitsa mavutowa.—2 Timoteyo 3:16.

MABOMA A ANTHU SAKULAMULIRA BWINO

Baibulo limati: “Aliyense woipa akayamba kulamulira, anthu amabuula.”—Miyambo 29:2.

Mbiri yakale imafotokoza za anthu ambiri amene analamulira mayiko awo mwankhanza, moti anthu amene ankawalamulirawo ankakumana ndi mavuto osaneneka. Ndi zoona kuti si olamulira onse omwe amalamulira mwankhanza. Ena amakhala ndi zolinga zabwino zofuna kuthandiza anthu. Komabe zimene zimachitika ndi zoti akayamba kulamulira, zolinga zawo zimalephereka chifukwa cha mikangano komanso kulimbirana ulamuliro komwe kumakhalapo pakati pa anthu omwe ali m’boma. Nthawi zinanso amatha kugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika chifukwa cha dyera ndipo zimenezi zimapweteketsa anthu awo. Mlembi wakale wa boma la America, dzina lake Henry Kissinger, anati: “M’mbiri yonse ya anthu taona kuti zolinga zimene anthu amakhala nazo zimalephereka komanso zomwe anthu amayembekezera sizikwaniritsidwa.”

Baibulo limanenanso kuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Anthu ochimwa alibe nzeru zowathandiza kudziyang’anira okha bwinobwino pa moyo wawo. Ngati munthu sangathe kudzilamulira yekha, ndiye angalamulire bwanji dziko lonse? Mwina pamenepa mukutha kuona chifukwa chake anthu olamulira amalephera kuthetsa mavuto onse. Ndipotu, mavuto ambiri amayamba chifukwa choti anthu akulephera kulamulira bwino.

ZIMENE CHIPEMBEDZO CHONYENGA CHIMACHITA

Yesu ananena kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”—Yohane 13:35.

Atsogoleri a zipembedzo zonse amalalikira za chikondi komanso mgwirizano. Koma zoona zake n’zakuti iwo alephera kuthandiza anthu awo kuti azikondana mochokera pansi pa mtima, zomwe zingathandize kuti asamasankhane. M’malo mophunzitsa anthu chikondi, nthawi zambiri zipembedzo zimayambitsa magawano, tsankho, ndiponso mikangano pakati pa anthu komanso mayiko. M’mawu omaliza amene analemba m’buku lake, katswiri wina wamaphunziro apamwamba a zaumulungu, dzina lake Hans Küng,  anati: “Pa nkhondo zonse kapena mikangano yonse yandale, mikangano yoopsa kwambiri ndi imene inayambitsidwa kapena kuvomerezedwa ndi zipembedzo.”—Christianity and the World Religions.

Kuwonjezera pamenepa, atsogoleri a zipembedzo zambiri amavomereza poyera kuti anthu azigonana asanalowe m’banja, azisiya mwamuna kapena mkazi wawo n’kumagonana ndi munthu wina, ndiponso amavomereza kuti amuna kapena akazi okhaokha azigonana. Izi zachititsa kuti matenda afalikire kwambiri, anthu ambiri azichotsa mimba, azitenga mimba zosakonzekera komanso kuti mabanja azitha, ndipo zimenezi zachititsa kuti moyo ukhale wovuta.

MTIMA WADYERA KOMANSO UCHIMO

“Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake. Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.”—Yakobo 1:14, 15.

Chifukwa chakuti tinatengera uchimo kwa makolo athu, nthawi zambiri timalephera kuchita zinthu zabwino komanso timalimbana ndi “kuchita zofuna za thupi.” (Aefeso 2:3) Ndipo zimakhala zovuta kwambiri kudziletsa ngati munthu amene ali ndi maganizo oipa wapeza mwayi wochita zoipazo. Choncho, ngati titamalakalaka zinthu zoipa tikhoza kupanga tchimo.

Wolemba mabuku wina, dzina lake P. D. Mehta, analemba kuti: “Mavuto ambiri amene timakumana nawo amabwera chifukwa chokonda zosangalatsa, mtima wadyera ndiponso mtima wofuna kulemera kapena kutchuka.” Zimenezi n’zoona chifukwa kukonda kwambiri zinthu monga mowa, mankhwala ozunguza bongo, juga komanso chiwerewere kumapangitsa kuti munthu akumane ndi mavuto ambiri komanso kumavutitsa banja lake ndi anzake. Pozindikira kuti anthu ndi ochimwa, mpake kuti Baibulo limati: “Tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.”—Aroma 8:22.

MIZIMU YOIPA

Baibulo limanena kuti Satana ndi “mulungu wa nthawi ino” ndipo amalamulira limodzi ndi mizimu yoipa komanso yamphamvu, yomwe ndi ziwanda.—2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:9.

Mofanana ndi Satana, ziwanda zimenezi zimayesetsa kulamulira zochita za anthu komanso kuwasocheretsa. Mtumwi Paulo ankadziwa zimenezi ndipo n’chifukwa chake ananena kuti: “Sitikulimbana ndi anthu athupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma, maulamuliro, olamulira dziko a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.”—Aefeso 6:12.

Ziwanda zimasangalala zikamavutitsa anthu koma cholinga chawo chachikulu ndi kupatutsa anthu kuti asakhale kumbali ya Yehova Mulungu, yemwe ndi Wam’mwambamwamba. (Salimo 83:18) Pofuna kusocheretsa anthu, ziwanda zimagwiritsa ntchito zinthu monga kukhulupirira nyenyezi, matsenga komanso kulosera. N’chifukwa chake Yehova amatichenjeza za zinthu zimenezi ndiponso amatetezera anthu amene amatsutsa Satana ndi ziwanda zake.—Yakobo 4:7.

TIKUKHALA ‘M’MASIKU OTSIRIZA’

Zaka 2,000 zapitazo, Baibulo linaneneratu kuti: “Dziwa kuti, masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.”

Ponena zimene zizidzachitika m’nthawi yovutayi, Baibulo linanena kuti: “Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” Choncho, mavuto ambiri amene tikukumana nawowa akuchitika chifukwa chakuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’—2 Timoteyo 3:1-4.

Malinga ndi zimene takambirana m’nkhaniyi, mpake kuti anthu akulephera kuthetsa mavuto ngakhale kuti akuyesetsa kuti awathetse. Ndiye kodi ndani angatithandize? Tiyenera kudalira kuti Mlengi wathu ndi amene angatithandize chifukwa analonjeza kuti ‘adzawononga ntchito za Mdyerekezi’ limodzi ndi otsatira ake. (1 Yohane 3:8) Nkhani yotsatira ifotokoza zimene Mulungu adzachite kuti athetse mavuto onse amene tikukumana nawowa.