Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZITSANI ANA ANU

Kodi Yesu Khristu Tizimukumbukira Bwanji?

Kodi Yesu Khristu Tizimukumbukira Bwanji?

M’mwezi wa December chaka chilichonse, padziko lonse pamapezeka zithunzi zambirimbiri za Yesu ali wakhanda. Amamujambula ali modyera ziweto. Kodi tiyenera kukumbukira Yesu monga mwana wakhanda? * Tiyeko tikambirane njira ina yofunika kwambiri imene tingamukumbukirire. Tingaphunzire pa zimene zinachitikira abusa ena kufupi ndi Betelehemu, omwe anagona kutchire komwe ankadyetsa ziweto zawo usiku.

Mwadzidzidzi, panafika mngelo. Iye anauza abusawo kuti: “Lero wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.” Anawauzanso kuti akamupeza mwanayo ali “wokutidwa m’nsalu, atagona modyeramo ziweto.” Nthawi yomweyo panafikanso angelo ena ambiri ndipo anayamba ‘kutamanda Mulungu.’

Kodi ungamve bwanji utaona angelo akutamanda Mulungu?— Angelowa anasangalala kwambiri. Abusawo atamva zimenezi, anauzana kuti: “Tiyeni tipite ndithu ku Betelehemu tikaone zimene zachitikazo.” Atafika kumeneku anapeza “Mariya ndi Yosefe, komanso mwana wakhandayo atagona modyeramo ziweto.”

Pasanapite nthawi yaitali, anthu enanso anafika ku Betelehemu kumene kunali Mariya ndi Yosefe. Abusa aja atawauza zimene zinachitikazo, iwo anasangalala kwambiri. Kodi iwenso nkhani imeneyi ikukusangalatsa?— Aliyense amene amakonda Mulungu angasangalale nayo. Tsopano tiye tione chifukwa chake kubadwa kwa Yesu kumasangalatsa anthu ambiri. Kuti tidziwe zimenezi, tiye tikambirane kaye zimene zinachitika Mariya asanakwatiwe.

Tsiku lina mngelo wina, dzina lake Gabirieli, anapita kunyumba kwa Mariya. Anamulonjeza kuti adzakhala ndi mwana yemwe “adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba.” Gabirieli ananenanso kuti mwanayo ‘adzalamulira monga mfumu moti ufumu wake sudzatha.’

Mariya anafuna kudziwa kuti zimenezi zidzatheka bwanji chifukwa anali asagonepo ndi mwamuna. Choncho Gabirieli anamufotokozera mmene zidzakhalire.  Iye anati: “Mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.” Zimene Mulungu anachita, potenga moyo wa Mwana wake kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya, zinali zodabwitsa kwambiri.

Kodi unaonapo zithunzi zosonyeza anthu atatu, omwe anthu amati ndi anzeru akum’mawa, atapita kukaona Yesu ali wakhanda atazunguliridwa ndi abusa?— Pa nthawi ya Khirisimasi zithunzi zoterezi zimapezeka zambiri. Koma si zolondola. Amuna atatuwo sanali anzeru koma anali okhulupirira nyenyezi ndipo Mulungu amadana ndi kukhulupirira nyenyezi. Tiye tione zimene zinachitika atafika. Baibulo limati: “Atalowa m’nyumbamo, anaona mwanayo ndi mayi ake Mariya.” Ona kuti Baibulo likunena kuti iwo analowa m’nyumba, osati m’khola. Choncho, pa nthawiyi Yosefe ndi Mariya sankagonanso m’khola koma ankagona m’nyumba. Komanso Baibulo likusonyeza kuti mwanayo sanali modyeramo ziweto koma anali ndi mayi ake.

Kodi okhulupirira nyenyezi aja anadziwa bwanji kumene kunali Yesu?— Iwo anatsogoleredwa ndi chinthu chooneka ngati nyenyezi ndipo chisanawatsogolere ku Betelehemu, chinawatsogolera kaye kwa Mfumu Herode, ku Yerusalemu. Baibulo limanena kuti Herode ankafuna kudziwa kumene kuli Yesu n’cholinga choti amuphe. Ndiye taganiza, ndani anapanga chimene chinkaoneka ngati nyenyezicho kuti chitsogolere okhulupirira nyenyezi aja kwa Herode?— Sanali Yehova Mulungu, koma anali mdani wake wamkulu, Satana Mdyerekezi.

Masiku ano, Satana amafuna kuti anthu azingoganizira za Yesu ngati ndi mwana wamng’ono. Koma mngelo Gabirieli anauza Mariya kuti: “Iye adzalamulira monga mfumu . . . , moti ufumu wake sudzatha.” Choncho panopa Yesu akulamulira monga Mfumu kumwamba ndipo posachedwapa adzawononga adani onse a Mulungu. Motero tiyenera kumamukumbukira Yesu monga Mfumu ndipo tiyenera kuuza ena zimenezi.

^ ndime 3 Ngati mukuwerengera mwana nkhaniyi, mukapeza mzera muime kaye kuti anenepo maganizo ake.