NSANJA YA OLONDA September 2013 | N’chifukwa Chiyani Anthu Akuvutika Chonchi? Nanga Mavuto Amenewa Adzatha Liti?

Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya mavuto amene anthu amakumana nawo, nanga adzatha liti?

NKHANI YAPACHIKUTO

Anthu Ambiri Osalakwa Akuphedwa

Padzikoli, anthu ambiri osalakwa akuvutika. Kodi ndi Mulungu amene amachititsa mavuto amenewa?

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Anthu Akukumana ndi Mavuto Onsewa?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu zikuluzikulu 5 zomwe zikuchititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto komanso mudziwa amene tingamudalire kuti adzathetsa mavuto onsewa.

NKHANI YAPACHIKUTO

Mavuto Onsewa Atha Posachedwapa

Mulungu walonjeza kuti adzachotsa zinthu zonse zomwe zimabweretsa mavuto. Kodi adzachita bwanji zimenezi ndipo adzazichita liti?

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndife Osauka Koma Olemera Mwauzimu

Zimene zinamuchitikira Alexander Ursu zinamuthandiza kudziwa kuti munthu akhoza kupita patsogolo mwauzimu ngakhale atakumana ndi mavuto ngati amene anthu omwe anali pansi pa ulamuliro wa Soviet Union anakumana nawo. Werengani nkhani yochititsa chidwiyi kuti mumve zimene anakumana nazo.

Kodi Zinenero Zathu Zinayambira pa “Nsanja ya Babele”?

Kodi “Nsanja ya Babele” n’chiyani? Kodi zinenero zathu zinayamba bwanji?

YANDIKIRANI MULUNGU

“Mulungu Amakonda Munthu Wopereka Mokondwera”

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe ubwino wokhala ndi zolinga zabwino popereka mphatso kapena pochitira zinthu anthu ena.

PHUNZITSANI ANA ANU

Zimene Timachita Zikhoza Kukhumudwitsa Mulungu—Kodi Tingatani Kuti Tizimusangalatsa?

Kodi mukudziwa kuti zimene mumachita zingakhumudwitse kapena kusangalatsa Yehova? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Adamu ndi Hava anachita zomwe zinakhumudwitsa Yehova.

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Malangizo a m’Baibulo okhudza banja amathandiza kuti banja likhale losangalala chifukwa malangizowo amachokera kwa Yehova Mulungu, yemwe ndi Woyambitsa ukwati.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndalama Zoyendetsera Ntchito ya a Mboni za Yehova Zimachokera Kuti?

Dziwani mmene ntchito yolalikira padziko lonse ikuyendera bwino popanda kupemphetsa ndalama kapena kupereka chakhumi.