Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani Nahumu anati mzinda wa Nineve unali “mzinda wokhetsa magazi”?

Zipilala zosonyeza asilikali akuunjika pamodzi mitu ya anthu amene agonjetsedwa

Mzinda wa Nineve unali likulu la ufumu wa Asuri. Unali mzinda wamphamvu kwambiri komanso unali ndi nyumba zikuluzikulu zachifumu, akachisi akuluakulu, misewu ikuluikulu ndi mipanda yolimba. Mneneri wachiheberi Nahumu anati mzindawu unali “mzinda wokhetsa magazi.”—Nahumu 3:1.

Limeneli linali dzina loyeneradi mzindawu chifukwa munali ziboliboli zochokera kunyumba ya Mfumu Senakeribu, zomwe zinkasonyeza nkhanza zimene ufumu wa Asuri unkachitira anthu. Chiboliboli china chinkasonyeza munthu akusolola lilime la kapolo yemwe anamukhomera pansi. Pamiyala ina analembapo kuti anthu ogwidwa kunkhondo ankawakoka ndi zingwe za ngowe imene ankawaboolera mphuno kapena mulomo. Atsogoleri a anthu ogwidwa kunkhondo ankawaveka m’khosi mutu wa mfumu yawo womwe ankauboola pakati kuti ulowe bwino m’khosi.

Katswiri wina wa mbiri ya Asuri, dzina lake Archibald Henry Sayce, anafotokoza zinthu zankhanza zimene Asuri ankachita akalanda tauni. Iye anati: “Ankadula mitu ya anthu n’kuiunjika pamodzi. Anyamata ndi atsikana ankawawotcha amoyo kapena kuwasunga kuti adzawaphe mwankhanza. Azibambo ankapachikidwa, kusendedwa khungu ali amoyo, kuwakoloola maso kapena kuwadula manja, mapazi, makutu komanso mphuno.”

Kodi n’chifukwa chiyani Ayuda ankamanga kampanda padenga la nyumba yawo?

Mulungu analamula Ayuda kuti: “Ukamanga nyumba yatsopano uzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopera kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.” (Deuteronomo 22:8) Kampanda kameneka kanali kofunika chifukwa kankathandiza Ayuda kupewa ngozi akamagwiritsa ntchito madenga a nyumba zawo m’njira zosiyanasiyana.

Madenga ambiri a nyumba za Aisiraeli ankakhala afulati. Aisiraeli ankakonda kukhala padengapo kuti aziothera dzuwa, kupuma kapena kugwira ntchito zina zapakhomo. M’nthawi yotentha, ankagona pamadengawa. (1 Samueli 9:26) Alimi ankayanika mphesa zawo kapena mbewu zina pamadengawa asanazipere.—Yoswa 2:6.

Ayuda ankagwiritsanso ntchito madengawa ngati malo olambirira. Ankalambirirapo Mulungu woona ndipo ena ankalambirapo milungu yonyenga. (Nehemiya 8:16-18; Yeremiya 19:13) Mwachitsanzo, mtumwi Petulo anakwera padenga masana kuti akapemphere. (Machitidwe 10:9-16) Pakakhala kuti pakhomopo pali mitengo ya mphesa kapena ya mgwalangwa, pamwamba pa madengawa pankakhala mthunzi wabwino.

Buku lina linanena kuti Aisiraeli ankapanga masitepe kapena makwerero okwerera pamwambapa omwe ankakhala “kunja kwa nyumba.” (The Land and the Book) Choncho munthu ankatha kutsika kapena kukwera padengapo popanda kulowa m’nyumba. Zimenezi zikutithandiza kumvetsa zomwe Yesu anatanthauza pamene anachenjeza anthu kuti adzathawe mumzinda mwamsanga. Iye anati: “Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike kukatenga katundu m’nyumba mwake.”—Mateyu 24:17.