Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 YANDIKIRANI MULUNGU

“Pemphanibe, Ndipo Adzakupatsani”

“Pemphanibe, Ndipo Adzakupatsani”

“Ambuye, tiphunzitseni kupemphera.” (Luka 11:1) Mawu amenewa ananena ndi mmodzi mwa ophunzira a Yesu ndipo ankauza Yesuyo. Poyankha, Yesu ananena mafanizo awiri omwe amatiphunzitsa zimene tingachite kuti Mulungu azimva mapemphero athu. Ngati nthawi zina mumakayikira zoti Mulungu amamva mapemphero anu, zimene Yesu ananena zingakuthandizeni.—Werengani Luka 11:5-13.

M’fanizo loyamba Yesu ananena za munthu amene akupemphera. (Luka 11:5-8) Iye anafotokoza za munthu amene analandira mlendo usiku ndipo analibe chakudya chom’patsa. Koma anaona kuti ayenera kupeza chakudya choti apatse mlendoyo. Ngakhale kuti unali usiku, iye anapita kwa mnzake kuti akabwereke chakudyacho. Poyamba mnzakeyo sanafune kudzuka chifukwa iye ndi banja lake anali atagona kalekale. Koma munthuyo analimbikira kupempha mnzakeyo kuti amupatsebe mpaka mnzakeyo anadzuka n’kumupatsa chakudyacho. *

Kodi fanizo limeneli likutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya pemphero? Apa mfundo ya Yesu inali yoti tiyenera kulimbikira kupemphera. Iye ananena kuti tizipemphabe, kufunafunabe komanso kugogodabe. (Luka 11:9, 10) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi? Kodi Yesu ankatanthauza kuti Mulungu amanyalanyaza kuyankha mapemphero athu? Ayi. Yesu ankatanthauza kuti mosiyana ndi bwenzi limene nthawi zina silifuna kupatsa mnzake zinthu, Mulungu amafunitsitsa kutipatsa zimene tapempha ngati tapempha ndi chikhulupiriro. Tikamalimbikira kupemphera timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro choti atipatsa. Komanso timasonyeza kuti tikufunadi zimene tikupemphazo ndipo tikukhulupirira kuti Mulungu atipatsadi ngati zili zogwirizana ndi chifuniro chake.—Maliko 11:24; 1 Yohane 5:14.

Fanizo lachiwiri ndi lonena za Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Yesu anafunsa kuti: “Kodi kapena pakati panu alipo bambo amene mwana wake atam’pempha nsomba, angam’patse njoka m’malo mwa nsomba? Kapena atam’pempha dzira iye angam’patse chinkhanira?” Apa yankho ndi lodziwikiratu. Palibe bambo wachikondi amene angapatse ana ake zinthu zoipa. Kenako Yesu anafotokoza tanthauzo la fanizoli. Mfundo yake inali yoti, ngati anthu opanda ungwiro ‘amapatsa mphatso zabwino’ ana awo, “kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” *Luka 11:11-13; Mateyu 7:11.

Mulungu amafunitsitsa kutipatsa zimene tapempha ngati tapempha ndi chikhulupiriro

Kodi fanizo limeneli likutiphunzitsa chiyani za Yehova, yemwe ndi “Wakumva pemphero”? Yesu ankafuna tiziona kuti Yehova ndi Atate wachikondi amene amafunitsitsa kupatsa ana ake zimene apempha. Choncho olambira Yehova angapemphere momasuka kwa iye kuti awapatse zosowa zawo. Chifukwa chodziwa kuti iye amawafunira zabwino, iwo amayembekezera kuti ayankha mapemphero awo ngakhale zitakhala kuti yankholo silingafanane ndi zimene amayembekezera. *

Mavesi amene mungawerenge mu April

Luka chaputala 7 mpaka 21

^ ndime 4 Fanizo la Yesuli linali logwirizana ndi zimene zinkachitika pa nthawiyo. Ayuda ankaona kuti kuchereza alendo kunali kofunika kwambiri. Banja linkangophika chakudya chokwana tsiku limodzi, choncho nthawi zambiri sankakhala ndi chakudya chotsala. Komanso ngati ali osauka, banja lonse linkagona pansi m’chipinda chimodzi.

^ ndime 6 Nthawi zambiri Yesu ankagwiritsa ntchito mawu akuti “kuli bwanji,” pofuna kumveketsa mfundo yoti ngati chaching’ono chimachita zinazake ndiye kuti chachikulu chingachite zoposa pamenepo.

^ ndime 7 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene mungachite kuti Mulungu azimva mapemphero anu, werengani mutu 17 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.