Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

”Ndinali Munthu Wachiwawa”

”Ndinali Munthu Wachiwawa”
  • CHAKA CHOBADWA: 1960

  • DZIKO: FINLAND

  • POYAMBA: NDINKAIMBA NYIMBO ZAPHOKOSO KWAMBIRI

KALE LANGA:

Ndinakulira mumzinda wa Turku ndipo m’dera limene ndinkakhala, anthu ambiri anali osauka. Bambo anga anali katswiri wa masewera a nkhonya ndipo ineyo ndi mchimwene wanga tinkachita nawonso masewerawa. Nthawi zambiri kusukulu ndinkakonda kuchita ndewu. Ndisanakwanitse zaka 20, ndinalowa m’gulu linalake la achinyamata ovuta ndipo zimenezi zinandipangitsa kuti ndikhale munthu wachiwawa kwambiri. Ndinayambanso kuimba nyimbo zaphokoso ndipo ndinkafuna kudzakhala katswiri wa nyimbozi.

Ndinagula zida zoimbira ndipo ndinayambitsa gulu langa loimba. Pasanapite nthawi ndinakhala katswiri woimba m’gululi. Ndikamaimba, ndinkakonda kusokosera kwambiri. Chifukwa chakuti gulu lathu loimba linkakonda kuimba nyimbo zaphokoso kwambiri komanso tinkaoneka mosiyana ndi anthu ena, tinayamba kutchuka kwambiri. Izi zinapangitsa kuti tikamaimba kuzibwera anthu ambiri. Tinajambula maabamu angapo ndipo abamu yomaliza ndi imene anthu anaikonda kwambiri. Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1980, tinapita ku America kumene tinakatchukitsa gulu lathu loimba. Tinaimba m’madera angapo ku New York ndi ku Los Angeles. Tisanabwerere kwathu ku Finland, tinadziwana ndi makampani ena ojambula nyimbo.

Ngakhale kuti ndinkasangalala ndi kuimba, ndinkaonabe kuti ndikusoweka chinachake pa moyo wanga. Sindinkasangalala ndi khalidwe la mpikisano komanso kudyerana masuku pamutu kumene anthu ogulitsa nyimbo zathu ankachita. Komanso ndinkakhumudwa ndi khalidwe langa loipa moti ndinkachita mantha chifukwa ndinkaganiza kuti ndikadzafa, ndidzakawotchedwa kumoto. Ndinkayesetsa kupeza mayankho a mafunso anga m’mabuku osiyanasiyana achipembedzo komanso ndinkapemphera kwambiri kuti Mulungu andithandize ngakhale ndinkaona kuti n’zosatheka kumukondweretsa.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Kuti ndizipeza ndalama, ndinayamba kugwira ntchito ku positi ofesi. Tsiku lina ndinazindikira kuti mnzanga amene ndinkagwira naye ntchito anali wa Mboni za Yehova. Ndinamufunsa mafunso ambirimbiri ovuta koma mayankho ake omveka bwino ochokera m’Baibulo anandigwira mtima ndipo zinapangitsa kuti ndiyambe kuphunzira naye Baibulo. Nditaphunzira Baibulo kwa milungu ingapo, gulu  lathu loimba linapatsidwa mwayi wojambulitsa nyimbo ku America ndipo zimenezi zikanatipezetsa ndalama zambiri. Uwu ndinaona kuti unali mwayi wanga umene sindinafunike kuuphonya.

Ndinauza amene ankandiphunzitsa Baibulo uja kuti ndinkafunitsitsa nditangotulutsa abamu imodzi ndipo ndikatero ndisiya kuimba n’kuyamba kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wanga. Iye sanandisankhire zochita koma anangondipempha kuti ndiwerenge mawu a Yesu amene amapezeka pa Mateyu 6:24. Lembali limati: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri.” Nditazindikira tanthauzo la lemba limeneli, ndinadabwa kwambiri. Patapita masiku angapo, munthu amene ankandiphunzitsa Baibulo uja nayenso anadabwa ndi zimene ndinamuuza. Ndinamuuza kuti ndachoka m’gulu loimba pofuna kutsatira mawu a Yesuwa.

Baibulo linali ngati galasi loonera limene linkandithandiza kudziwa za khalidwe langa loipa. (Yakobo 1:22-25) Ndinazindikira kuti ndinali munthu wachiwawa komanso wonyada, ndinkatukwana, kuchita ndewu, kusuta ndiponso kumwa mwauchidakwa. Nditazindikira kuti ndinkachita zinthu zosemphana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, ndinakhumudwa kwambiri. Komabe, ndinkayesetsa kusintha khalidwe langa loipali.—Aefeso 4:22-24.

“Mulungu ndi wachifundo ndipo amafuna kuti anthu amene analapa machimo awo asamadziimbe mlandu chifukwa cha machimo omwe anachita m’mbuyo”

Nditangoyamba kuphunzira Baibulo, ndinkadzimvera chisoni ndikaganizira zoipa zimene ndinkachita ndisanayambe kuphunzira Baibulo. Koma wa Mboni amene ankandiphunzitsa anandithandiza kwambiri. Iye anandisonyeza zimene lemba la Yesaya 1:18 limanena. Lembali limati: “Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.” Lembali komanso malemba ena a m’Baibulo anandithandiza kudziwa kuti Mulungu ndi wachifundo ndipo amafuna kuti anthu amene analapa machimo awo asamadziimbe mlandu chifukwa cha machimo omwe anachita m’mbuyo.

Nditaphunzira za Yehova n’kuyamba kumukonda, ndinaganiza zoyamba kumutumikira. (Salimo 40:8) Choncho ndinabatizidwa m’chaka cha 1992 pa msonkhano waukulu wa Mboni za Yehova umene anthu ake anachokera m’mayiko osiyanasiyana. Msonkhanowu unachitikira mumzinda wa St. Petersburg, ku Russia.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Panopa ndili ndi anzanga ambiri omwenso ndimalambira nawo limodzi. Nthawi zambiri timaimbira limodzi nyimbo zabwino ndipo timasangalala kwambiri ndi mphatso imeneyi yomwe ndi yochokera kwa Mulungu. (Yakobo 1:17) Mphatso ina yapadera ndi mkazi amene ndinakwatira dzina lake Kristina. Ineyo ndi mkazi wangayu, timachitira zinthu zambiri limodzi pa mavuto komanso pamtendere ndipo ndi munthu amene ndimauzana naye zakukhosi.

Ndikanakhala kuti sindine wa Mboni za Yehova mwina bwenzi pano nditamwalira. Kale ndisanayambe kuphunzira Baibulo, ndinkangogwa m’mavuto koma panopa ndimaona kuti moyo wanga ndi waphindu.