Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi anthu akale ankayenda bwanji panyanja?

PA NTHAWI ya Paulo kunalibe sitima zimene zinkangonyamula anthu basi. Choncho anthu ofuna kuyenda panyanja ankayenera kufunsa ena ngati akudziwa sitima zonyamula katundu zomwe zinkapita kumene akufuna. Ankafufuzanso ngati oyendetsa ake angawalole kukwera. (Mac. 21:2, 3) Ngakhale kuti sitimayo sinkapita kumalo amene ankafuna, ankatha kukwera kenako n’kutsika pamalo ena kuti apeze sitima ina yopita kumene akufunako.​—Mac. 27:1-6.

Sitima zinkangoyenda pa nthawi zina pa chaka ndipo sizinkayendera ndandanda. Oyendetsa sankayenda ngati nyengo sili bwino komanso amene ankakhulupirira mizimu sankayendanso pa zifukwa zina. Mwachitsanzo, iwo sankayenda ngati khwangwala walira pasitima yawo kapena ngati aona sitima itasweka m’mbali mwa nyanja. Oyendetsa sitima ankayenda ngati mphepo ikulowera kumene ankafuna kupita. Munthu akadziwa sitima imene angakwere ankapita kudoko ndi katundu wake n’kumadikira chilengezo choti sitimayo ikunyamuka.

Wolemba mbiri yakale dzina lake Lionel Casson ananena kuti: “Ku Roma kunali dongosolo lothandiza kuti anthu asamavutike kwambiri kupeza sitima yoti akwere. Doko lakumzindawu linali pafupi ndi mtsinje wa Tiber. M’tauni yapafupi ya Ostia munali bwalo lalikulu lozunguliridwa ndi maofesi. Maofesi ambiri anali a eniake a sitima zochokera kumayiko osiyanasiyana. Mwachitsanzo, kunali ofesi ya sitima za ku Narbonne [panopa ndi France] komanso ya sitima za ku Carthage [panopa ndi Tunisia]. Munthu amene ankafufuza sitima kuti akwere ankangopempha kumaofesi oyang’anira sitima zodutsa kumizinda yomwe inali panjira imene ankafuna kupita.”

Kuyenda panyanja kunkathandiza kuti anthu afike msanga kumene ankapita komabe kunali ndi mavuto. Mwachitsanzo, sitima zimene Paulo ankakwera pamaulendo ake aumishonale zinkasweka nthawi zina.​—2 Akor. 11:25.