Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesu Anatiphunzitsa Mmene Tingakhalire ndi Moyo Wosangalala

Yesu Anatiphunzitsa Mmene Tingakhalire ndi Moyo Wosangalala

‘Yendani mmene iyeyo [Yesu] anayendera.’—1 Yohane 2:6.

NKHANI yapitayi yatithandiza kuona kuti moyo wa Yesu unali waphindu. Chotero ngati ifenso tikufuna kuti moyo wathu ukhale waphindu komanso wosangalala, tiyenera kutengera chitsanzo chake komanso kutsatira malangizo ake.

Ndipotu lemba lomwe lili pamwambali likusonyeza kuti Yehova amafuna kuti tizitsanzira Yesu. Kuyenda mmene Yesu anayendera kumatanthauza kuchita zinthu zonse mogwirizana ndi zimene iye ankachita komanso kuphunzitsa. Kuchita zimenezi kungapangitse kuti Mulungu azitikonda komanso kuti tikhale ndi moyo wosangalala.

Zimene Yesu anaphunzitsa zikuphatikizapo mfundo zomwe zingatithandize kuti tiziyenda monga mmene iye anayendera. Mfundo zimenezi timazipeza kuchokera pa zimene iye anaphunzitsa pa ulaliki wake wa paphiri. Tiyeni tikambirane zina mwa mfundozi komanso kuona mmene tingazigwiritsire ntchito pa moyo wathu.

MFUNDO YOYAMBA: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.

MMENE MFUNDOYI IMATHANDIZIRA MUNTHU KUKHALA WOSANGALALA:

Yesu anasonyeza kuti anthufe mwachibadwa timafunitsitsa titadziwa za Mulungu. Timafuna kudziwa mayankho a mafunso ngati awa: N’chifukwa chiyani tinalengedwa? N’chifukwa chiyani padziko lapansi pano pali mavuto ambirimbiri? Kodi Mulungu amakhudzidwa ndi mavuto amene timakumana nawo? Kodi akufa adzakhalanso ndi moyo? Tiyenera kudziwa mayankho a mafunso amenewa kuti tikhale ndi moyo wosangalala. Yesu anadziwa kuti Mawu a Mulungu okha ndi amene angatithandize kupeza mayankho a mafunso amenewa. Popemphera kwa Atate wake, iye anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Kodi Baibulo lingatithandizedi kudziwa Mulungu kuti tikhale osangalala?

CHITSANZO:

Esa anali mtsogoleri wa gulu lina loimba ndipo anayamba kutchuka chifukwa cha luso la zoimbaimba. Ngakhale zinali choncho, iye sanali wosangalala kwenikweni. Esa ananena kuti: “Ngakhale kuti ndinkasangalala ndi kuimba, ndinkaonabe kuti ndikusoweka chinachake pa moyo wanga.” Koma patapita nthawi, Esa anakumana ndi wa Mboni za Yehova. Iye anati: “Ndinamufunsa mafunso ambirimbiri ovuta. Koma mayankho ake omveka bwino ochokera m’Baibulo anandigwira mtima ndipo zinapangitsa kuti ndiyambe kuphunzira naye Baibulo.” Zimene Esa anaphunzira m’Baibulo zinamugwira mtima kwambiri ndipo zinamuchititsa kuti abatizidwe posonyeza kudzipereka kwake kwa Yehova. Iye anawonjezera kuti: “Kale ndisanayambe kuphunzira Baibulo, ndinkangogwa m’mavuto. Koma panopa ndimaona kuti moyo wanga ndi waphindu.” *

MFUNDO YACHIWIRI: “Odala ndi anthu achifundo.”—Mateyu 5:7.

MMENE MFUNDOYI IMATHANDIZIRA MUNTHU KUKHALA WOSANGALALA:

Mawu akuti chifundo amatanthauza kumvera munthu chisoni komanso kumuthandiza. Yesu ankachitira chifundo anthu ovutika ndipo ankawathandiza pa mavuto awo. (Mateyu 14:14; 20:30-34) Tikamakhala achifundo ngati mmene Yesu ankachitira, zimatithandiza kukhala osangalala chifukwa anthu ochitira ena chifundo amakhala achimwemwe. (Machitidwe 20:35) Tingasonyeze kuti tikuchitira ena chifundo ngati mawu athu amakhala olimbikitsa komanso ngati timachita zinthu zothandiza anthu amene akuvutika. Kodi kuchitira ena chifundo kumathandizadi munthu kukhala wosangalala?

Maria ndi Carlos

CHITSANZO:

Maria ndi mwamuna wake, Carlos ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yochitira ena chifundo. Iwo anatenga bambo ake a Maria, omwe akazi awo anali atamwalira, n’kumakhala nawo. Zaka zaposachedwapa bambowa anadwala ndipo sakuthanso kuyenda. Nthawi zambiri Maria ndi Carlos sagona ndipo nthawi zina amafunika kuthamangira ndi bambowa kuchipatala usiku chifukwa cha matenda awo ashuga.  Zimenezi zimapangitsa kuti Maria ndi Carlos azikhala otopa kwambiri. Komatu iwo amakhala osangalala, monga mmene Yesu ananenera, chifukwa amadziwa kuti akukwanitsa udindo wawo wosamalira bambo awo.

MFUNDO YACHITATU: “Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere.”—Mateyu 5:9.

MMENE MFUNDOYI IMATHANDIZIRA MUNTHU KUKHALA WOSANGALALA:

Kodi kukhala mwamtendere ndi anthu ena kungatithandize bwanji kukhala osangalala? Tikamakhala mwamtendere ndi anzathu, zimapangitsa kuti tizigwirizana ndi anthu. Tiyenera kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” (Aroma 12:18) Palembali, mawu akuti “anthu onse” akuphatikizapo anthu a m’banja mwathu komanso anthu ena amene sitili nawo m’chipembedzo chimodzi. Kodi kukhala mwamtendere ndi “anthu onse” kungatichititsedi kukhala osangalala?

Nair

CHITSANZO:

Taganizirani zimene zinachitikira mzimayi wina dzina lake Nair. Kwa zaka zambiri, iye wakhala akukumana ndi mavuto osiyanasiyana amene akanam’pangitsa kuti asamakhale mwamtendere ndi anthu ena, makamaka ana ake. Iye wakhala akulera yekha ana kuchokera pamene mwamuna wake anamusiya zaka pafupifupi 15 zapitazo. Mwana wake wina amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo nthawi zambiri amavutitsa kwambiri mayi akewo komanso mchemwali wake. Nair amakhulupirira kuti zimene waphunzira m’Baibulo zimamuthandiza kukhala mwamtendere ndi mwana wakeyo ngakhale kuti mwanayo ndi wovuta kwambiri. Iye amayesetsa kuti asamakangane naye kapena kutsutsana naye. Amayesetsanso kukhala wachifundo, wokoma mtima komanso womvetsetsa. (Aefeso 4:31, 32) Nair amaona kuti kuchita zimenezi kumamuthandiza kukhala bwino ndi anthu.

KUDZIWA ZIMENE YEHOVA ADZACHITE M’TSOGOLOMU KUMATHANDIZA

Ngati titatsatira malangizo a Yesu, tidzakhala osangalala komanso okhutira ndi zimene tikuchita pa moyo wathu. Komabe kuti moyo wathu ukhaledi waphindu, tiyeneranso kudziwa zimene Mulungu adzachite m’tsogolo. Tikutero chifukwa anthufe timakalamba, kudwala kenako n’kufa. Choncho ngati tilibe chiyembekezo chilichonse, moyo wathu sungakhale waphindu.

Komabe n’zosangalatsa kuti Yehova analonjeza kuti onse amene akuyesetsa “kuyenda mmene [Yesu] anayendera,” adzawadalitsa kwambiri. Yehova amalonjeza kuti adzabweretsa dziko latsopano lolungama, limene anthu onse okhulupirika adzakhala monga mmene iyeyo anafunira poyamba. M’dziko limeneli anthu adzakhala ndi thanzi labwino. Baibulo limati: “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Maria, agogo a zaka 84 amene tawatchula m’nkhani yoyambirira ija, amasangalala akamaganizira nthawi imene mawu amenewa adzakwaniritsidwe. Kodi inunso mumasangalala mukamva za lonjezo limeneli? Kodi mukufuna mutadziwa zambiri zokhudza “moyo weniweni,” womwe tidzakhale nawo Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira padziko lapansili? (1 Timoteyo 6:19) Ngati mukufuna kuphunzira zambiri pa nkhaniyi, funsani Mboni za Yehova m’dera lanu kapena lemberani ofesi ya Mboni za Yehova. *

^ ndime 8 Mungawerenge zokhudza moyo wa Esa onani nkhani ya mutu wakuti, ”Baibulo Limasintha Anthu—Ndinali Munthu Wachiwawa”.

^ ndime 18 Buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lathandiza anthu kumvetsa nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo.