NSANJA YA OLONDA April 2013 | Kodi N’zotheka Kukhala ndi Moyo Waphindu?

Mlengi wathu akufuna kuti tipeze moyo waphindu. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipeze moyo umenewu?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi N’zotheka Kukhala ndi Moyo Waphindu?

Tikamakumana ndi mavuto kapena tikakhala ndi chisoni ndi pamene timafuna kwambiri kudziwa ngati n’zothekadi kukhala ndi moyo waphindu.

NKHANI YAPACHIKUTO

Zimene Zinapangitsa Kuti Moyo wa Yesu Ukhale Waphindu

Ganizirani zinthu 4 zokhudza moyo wa Yesu zimene zinapangitsa kuti akhale ndi moyo waphindu.

NKHANI YAPACHIKUTO

Yesu Anatiphunzitsa Mmene Tingakhalire ndi Moyo Wosangalala

Zimene zachitikira anthu ena pa moyo wawo zimasonyeza kuti kutsatira zimene Yesu ananena pa ulaliki wa paphiri kumathandiza kuti munthu akhale ndi moyo waphindu.

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

”Ndinali Munthu Wachiwawa”

Ngakhale kuti zinthu zinkamuyendera bwino pa nkhani ya zoimba, Esa ankaonabe kuti moyo wake ulibe phindu. Werengani kuti mumve mmene munthu wokonda nyimbo zaphokoso ameneyu anapezera moyo wosangalaladi.

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani mzinda wa Nineve womwe unali likulu la ufumu wa Asuri unkatchedwa “mzinda wokhetsa magazi”? N’chifukwa chiyani Ayuda ankamanga kampanda padenga la nyumba zawo?

YANDIKIRANI MULUNGU

“Pemphanibe, Ndipo Adzakupatsani”

Werengani mafanizo awiri amene Yesu ananena pa Luka chaputala 11 ofotokoza zimene tingachite kuti Mulungu azimva mapemphero athu.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

Nowa ”Anayenda ndi Mulungu Woona”

Kodi tingaphunzire chiyani kwa Nowa ndi mkazi wake, komanso banja lake?

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Yehova Mulungu amafuna kuti tidziwe zoona zokhudza iyeyo. Angakuthandizeni kuti muzimvetsa bwino Malemba.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Phunziro la Baibulo N’chiyani?

Pezani mayankho a mafunso okhudza phunziro la Baibulo laulere.