Pitani ku nkhani yake

Kodi Phunziro la Baibulo lomwe a Mboni za Yehova Amachititsa Limakhala Lotani?

Kodi Phunziro la Baibulo lomwe a Mboni za Yehova Amachititsa Limakhala Lotani?

 Kodi phunziro la Baibulo limachitika bwanji?

 Pali munthu amene azikuthandizani kudziwa Baibulo poliphunzira motsatira mutu wa nkhani. Muziphunzira mokambirana buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale kuti mwapang’onopang’ono mudziwe uthenga wa m’Baibulo komanso mmene Baibulolo lingakuthandizireni. Kuti mudziwe zambiri, onerani vidiyoyi.

 Kodi ndiyenera kulipira kuti ndiphunzire?

 Ayi. Timatsatira malangizo amene Yesu anapatsa ophunzira ake akuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:8) Anthu amene amaphunzitsa salipiridwa komanso mungalandire Baibulo kapena buku lakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale kwaulere.

 Kodi limatenga nthawi yaitali bwanji?

 M’bukuli muli maphunziro 60. Mungasankhe mmene mukufuna kuphunzirira koma ambiri amakonda kumaliza phunziro limodzi kapena oposerapo mlungu uliwonse.

 Kodi ndingayambe bwanji?

  1.  1. Mulembe fomu imene ili pawebusaiti yathu. Tidzagwiritsa ntchito zimene mwalemba kuti munthu ayambe kuphunzira nanu basi.

  2.  2. Munthu amene azidzaphunzira nanu adzakupezani. Iye adzakufotokozerani mmene phunziro lanu liziyendera komanso adzayankha mafunso amene mungakhale nawo.

  3.  3. Inu ndi munthuyo mudzapangana mmene muzidzaphunzirira. Mukhoza kuphunzira pogwiritsa ntchito foni, vidiyo, polemberana makalata kapena maimelo. Nthawi zambiri, anthu amaphunzira kwa ola limodzi koma mukhoza kuchepetsa kapena kutalikitsa nthawiyo malinga ndi zimene mungafune.

 Kodi ndikhoza kungoyesa kaye?

 Inde. Kuti muchite zimenezi, lembani fomu pawebusaiti yathu. Munthu akadzakupezani, mumuuze kuti mukufuna kungoyesa kaye phunzirolo kuti muone ngati mungalikonde. Iye adzagwiritsa ntchito kabuku kakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale, komwe kali ndi maphunziro atatu oyambirira, kuti muone ngati mungasangalale ndi phunziro.

 Ngati ndiyamba kuphunzira Baibulo, kodi adzandikakamiza kuti ndikhale wa Mboni za Yehova?

 Ayi. A Mboni za Yehova amakonda kwambiri kuphunzira Baibulo ndi anthu, koma sitiwakakamiza kuti alowe chipembedzo chathu. M’malomwake, timaphunzitsa mwaulemu zimene Baibulo limanena ndipo timazindikira kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha zimene akufuna kukhulupirira.—1 Petulo 3:15.

 Kodi ndingagwiritse ntchito Baibulo langa?

 Inde, mukhoza kugwiritsa ntchito Baibulo lililonse limene mukufuna. Timakonda kugwiritsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika chifukwa ndi lomveka bwino komanso linamasuliridwa molondola. Koma timadziwa kuti anthu ambiri amakonda kugwiritsa ntchito Baibulo limene alizolowera.

 Kodi ndingapemphe anthu ena kuti akhale nafe pa phunzirolo?

 Inde. Mukhoza kupempha anthu onse a m’banja lanu kapena mnzanu wina aliyense.

 Ngati ndinaphunzirapo Baibulo ndi Mboni za Yehova m’mbuyomu, kodi ndingaphunzirenso?

 Inde. Ndipotu mwina mungakonde phunziro lathu latsopano kuposa lakalelo chifukwa talisintha mogwirizana ndi zimene anthu amafuna masiku ano. Limakhala ndi mavidiyo ndi zithunzi zambiri komanso ndi lokambirana kuposa lakalelo.

 Kodi ndingaphunzire Baibulo popanda munthu kundiphunzitsa?

 Inde. Ngakhale kuti anthu ambiri amaphunzira bwino akakhala ndi munthu wowaphunzitsa, ena amakonda kuyamba kaye ndi kuphunzira paokha. Gawo lathu lakuti Zokuthandizani Pophunzira Baibulo limasonyeza zinthu zaulere zomwe mungagwiritse ntchito pophunzira Baibulo. Zinthu zina zimene zingakuthandizeni ndi izi: