Kodi Mukudziwa?
Kuwonjezera pa zimene Baibulo limanena, kodi pali umboni wina wosonyeza kuti Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo?
Baibulo limasonyeza kuti Yosefe atatengedwa ndi Amidiyani kupita ku Iguputo, Yakobo ndi banja lake anasamukanso ku Kanani kupita ku Iguputo. Iwo anakakhala kudera labwino kwambiri la ku Goseni chakumapeto kwa mtsinje wa Nailo. (Gen. 47:1, 6) Aisiraeliwo anapitiriza “kuchulukana ndi kukhala amphamvu koposa.” Choncho Aiguputo anayamba kuchita mantha ndipo anachititsa kuti akhale akapolo awo.—Eks. 1:7-14.
Anthu ena amatsutsa nkhani ya m’Baibuloyi n’kumanena kuti ndi yongopeka. Komatu pali umboni wina wotsimikizira kuti ana a Semu * anakhala ku ukapolo ku Iguputo.
Mwachitsanzo, asayansi afukula zinthu zina kumpoto kwa Iguputo zosonyeza kuti kunkakhala anthu. Dr. John Bimson ananena kuti pali umboni wa malo 20 kapena kuposerapo wosonyeza kuti kumpoto kwa Iguputo kunkakhala ana a Semu. Wasayansi winanso amene amafufuza zinthu zakale ku Iguputo dzina lake James K. Hoffmeier ananena kuti: “Kuyambira m’ma 1800 kufika m’ma 1540 B.C., dziko la Iguputo linali labwino kwambiri moti ana a Semu akumadzulo kwa Asia [kumene banja la Yakobo linachokera] ankasamukirako.” Iye anapitiriza kuti: “Nthawi imeneyi ikugwirizana ndi nthawi ya makolo a Aisiraeli choncho ikugwirizananso ndi nkhani yam’buku la Genesis.”
Umboni wina ndi wochokera kum’mwera kwa dziko la Iguputo. Kumeneku anthu anapeza zolemba za m’zaka za m’ma 2000 mpaka 1600 B.C.E. zokhala ndi mayina a akapolo aamuna ndi aakazi omwe ankagwira ntchito m’nyumba za anthu. Pa mayinawo, mayina oposa 40 anali a ana a Semu. Ena mwa akapolowo ankagwira ntchito yophika, yoluka komanso ntchito zina. Hoffmeier ananenanso kuti: “Ngati kadera kochepa ka kum’mwera kwa Iguputo kanali ndi akapolo oposa 40 omwe anali ana a Semu, ndiye kuti anthu amtunduwu analiko ambiri, makamaka chakumapeto kwa mtsinje wa Nailo.”
Wasayansi winanso dzina lake David Rohl ananena kuti mayina amene anapezekawa ndi “ofanana ndi amene amapezeka m’Baibulo.” Mwachitsanzo, panali mayina monga Isakara, Aseri ndi Sifira. (Eks. 1:3, 4, 15) Rohl anamaliza ndi mawu akuti: “Umenewu ndi umboni wotsimikizira kuti Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo.”
Dr. Bimson ananena kuti: “M’mbiri yakale muli umboni wotsimikizira kuti Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo kenako anachokako.”
^ ndime 4 Semu anali mmodzi mwa ana atatu a Nowa. Ndipo ana ake anali amitundu monga Aelamu, Asuri, Akasidi, Aheberi, Asiriya ndi mafuko ena a Chiarabu.