Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Zinthu Zakale Zosonyeza Kuti Baibulo Ndi Lolondola

Malo Otchulidwa M'Baibulo

Zolemba Zakale Zimapereka Umboni Wosonyeza Malo Amene Aisiraeli Ankakhala

Mapale a ku Samariya amasonyeza kuti zomwe Baibulo limanena zokhudza mbiri yakale ndi zoona.

Kuwonongedwa kwa Nineve

Ulamuliro wa Asuri utakhala wamphamvu, mneneri wa Mulungu ananeneratu kuti padzachitika zosayembekezereka.

Kodi Mukudziwa?—July 2015

Baibulo limasonyeza kuti m’madera ena a dziko lolonjezedwa munali mitengo yambiri. Koma masiku ano m’madera ambiri m’dzikoli mulibe mitengo. Kodi zimene Baibulo limanena ndi zoona?

Kodi Mukudziwa?—April 2013

N’chifukwa chiyani mzinda wa Nineve womwe unali likulu la ufumu wa Asuri unkatchedwa “mzinda wokhetsa magazi”? N’chifukwa chiyani Ayuda ankamanga kampanda padenga la nyumba zawo?

Anthu a M'Baibulo

Kodi Mukudziwa?​​​—March 2020

Kuwonjezera pa zimene Baibulo limanena, kodi pali umboni wina wosonyeza kuti Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo?

Dzina la M’Baibulo Linapezeka Pamtsuko Wakale

Mu 2012 anthu ofukula zinthu zakale anasangalala atapeza mapale a mtsuko winawake womwe unaumbidwa zaka 3,000 zapitazo. Kodi chinali chapadera n’chiyani ndi zimene anapezazi?

Zimene Asayansi Afukula Zikutsimikizira Kuti Mfumu Davide Analikodi

Anthu ena amanena kuti Mfumu Davide kunalibe ndipo nkhani yake ndi yongopeka. Kodi asayansi apeza umboni wotani?

Kodi Mukudziwa?​—February 2020

Kodi zimene asayansi apeza zikutsimikizira bwanji kuti Belisazara anali mfumu ku Babulo?

Zithunzi Zakale—Koresi Wamkulu

Kodi Koresi anali ndani, nanga ndi ulosi wochititsa chidwi uti wonena za iye umene unanenedwa kutatsala zaka 150 kuti iye abadwe?

Umboni Wina Wosonyeza Kuti Baibulo Ndi Lolondola

Mwina simunamvepo za Tatenai, komabe ofukula zakale anapeza umboni wotsimikizira kuti iye anakhalako.

Kodi Yohane M’batizi Anakhalapodi?

Katswiri wolemba mbiri yakale dzina lake Josephus anatsimikizira mfundo yakuti Yohane M’batizi anakhalapodi. Choncho ifenso tiyenera kukhulupirira mfundo imeneyi.

Kodi Nkhani Yonena za Yesu Ndi Yongopeka?

Kodi akatswiri a mbiri yakale amanena zotani pa nkhani ya Yesu Khristu?

Kodi Nkhani ya Moyo wa Yesu Imene Ili M’Baibulo Ndi Yolondola?

Dziwani mfundo zokhudza nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino ndiponso mipukutu yakale kwambiri imene ikudziwika masiku ano.

Anali Wochokera M’banja la Kayafa

Kupezeka kwa bokosi la mafupa a Miriamu ndi umboni woti Baibulo limafotokoza za anthu enieni komanso mabanja awo.

Kodi Mukudziwa?—November 2015

N’chifukwa chiyani Yosefe anayamba wameta asanakaonane ndi Farao? N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti bambo a Timoteyo anali Mgiriki?

Kodi Mukudziwa?—May 2015

Kodi zimene akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena? Kodi mikango inasiya liti kupezeka m’madera otchulidwa m’Baibulo?

Zochitika za M'Baibulo

Kodi Nkhani ya Nowa Komanso Chigumula Ndi Nthano Chabe?

Baibulo limafotokoza kuti Mulungu anabweretsa chigumula kuti awononge anthu oipa. Kodi Baibulo lili ndi umboni wotani wotsimikizira kuti linalembedwadi ndi Mulungu?

Kodi Zinenero Zathu Zinayambira pa “Nsanja ya Babele”?

Kodi “Nsanja ya Babele” n’chiyani? Kodi zinenero zathu zinayamba bwanji?

Kodi Mukudziwa?​—June 2022

Kodi Aroma ankalola kuti munthu amene waphedwa popachikidwa pamtengo, ngati mmene zinalili ndi Yesu, aikidwe m’manda ngati anthu ena onse?

Chipilala Chakale cha ku Iguputo Chili Ndi Umboni wa Nkhani ya M’Baibulo

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene zolemba zakale za ku Iguputo zimasonyezera kuti anthu omwe analemba Baibulo anali oona mtima.

Kodi Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Ukapolo wa Ayuda ku Babulo N’zolondola?

Kodi zimene akatswiri ofufuza anapeza zikugwirizana bwanji ndi zimene Mulungu ananena zokhudza moyo wa Ayuda ali ku ukapolo ku Babulo?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga—November 2015

Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti mzinda wakale wa Yeriko unagonjetsedwa m’kanthawi kochepa?

Moyo wa Anthu Otchulidwa M'Baibulo

Galeta lomwe nduna ya ku Itiyopiya inakwera

Kodi nduna ya ku Itiyopiya inakwera galeta lotani pomwe inakumana ndi Filipo?

Kodi Mukudziwa?​—June 2022

Kodi kale anthu ankadziwa bwanji pamene payambira mwezi kapena chaka?

Kodi Zidindo Zakale Zinkagwira Ntchito Yanji?

N’chifukwa chiyani zidindo zakale zinali zofunika, nanga olamulira ankazigwiritsa ntchito bwanji?

“M’mapiri Ake Mudzakumbamo Mkuwa”

Posachedwapa, anthu ena ofukula zinthu zakale apeza zinthu zimene zingatithandize kudziwa mmene anthu akale ankagwiritsira ntchito mkuwa.

Kodi Mukudziwa?​—October 2017

Kodi Ayuda anali ndi chizolowezi chotani chomwe chinachititsa Yesu kuuza anthu kuti asamalumbire?

Kodi Mukudziwa?​—Nsanja ya Olonda Na. 5 2017

Kodi zimene Yesu ananena zokhudza “tiagalu” zinali zonyoza?

Kodi Mukudziwa?—June 2017

Kodi amalonda amene ankagulitsa nyama kukachisi mu Yerusalemu analidi ngati “achifwamba”?

Kodi Mukudziwa?—October 2016

M’nthawi ya atumwi, kodi Aroma ankapereka ufulu wotani kwa Ayuda amene ankalamulira ku Yudeya? Kodi zinkachitikadi kuti munthu ankafesa namsongole m’munda umene mnzake wafesamo mbewu?

Kodi Mukudziwa?—December 2015

Kodi Ayuda omwe anapita ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E., analidi ochokera ‘mu mtundu uliwonse wa pansi pa thambo’? Kodi anthu amene ankapita ku zikondwerero ku Yerusalemu ankagona kuti?

Kodi Mukudziwa?—March 2015

Kodi kukhala nzika ya Roma kunathandiza bwanji mtumwi Paulo? Kodi kale abusa ankawalipira bwanji?

Kodi Mukudziwa?—May 2014

N’chifukwa chiyani Ayuda anapempha Pilato kuti athyole miyendo ya Yesu? Kodi Davide anaphadi Goliyati ndi gulaye?

Kodi Mukudziwa?—February 2014

Kodi aloye amene ankagwiritsidwa ntchito kale anali chiyani? Kodi ndi nsembe zotani zimene zinali zovomerezeka pakachisi ku Yerusalemu?

Kodi Mukudziwa?—January 2014

Kodi anthu a m’nthawi ya Yesu, ankapereka bwanji zopereka zawo? Kodi zimene zili m’Baibulo zomwe Luka analemba ndi zolondola?