Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani zinali zothandiza kuti munthu azitha kupereka njiwa kapena nkhunda monga nsembe?

CHILAMULO cha Mose chinkalola kuti anthu azitha kupereka njiwa kapena nkhunda monga nsembe kwa Yehova. Nthawi zonse mbalame za mitundu iwiri zimenezi zinkatchulidwa limodzi m’Chilamulo pankhani yopereka nsembe, moti ngati munthu alibe nkhunda ankatha kupereka njiwa. (Lev. 1:14; 12:8; 14:30) Kodi n’chifukwa chiyani zimenezi zinali zothandiza? Chifukwa china n’chakuti nthawi zina njiwa zinkavuta kupeza. Chifukwa chiyani?

Njiwa

Njiwa ndi mbalame zimene zimasamukasamuka ndipo zimapezeka ku Isiraeli m’miyezi yotentha. Mu October zimasamukira m’mayiko a kum’mwera komwe kumakhala kotentha ndipo zimabwerera ku Isiraeli nyengo yozizira ikatha. (Nyimbo 2:11, 12; Yer. 8:7) Choncho zinali zovuta kwa Aisiraeli kupereka njiwa monga nsembe m’nyengo yozizira.

Nkhunda

Nkhunda sizisamukasamuka choncho zinkapezeka ku Isiraeli chaka chonse. Kuwonjezera pamenepa nkhunda zinkawetedwa. (Yerekezerani ndi Yohane 2:14, 16.) Buku lina lofotokoza za nyama ndi zomera linanena kuti, “m’midzi komanso m’matauni onse a ku Palesitina munkapezeka nkhunda zoweta. Pa nyumba iliyonse, anthu ankaboola khoma n’cholinga choti nkhundazo zizikhalamo.”​—Yerekezerani ndi Yesaya 60:8.

Nkhunda ili pabowo la pakhoma

Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ankakonda komanso kuganizira anthu ake, powalola kuti azipereka nsembe mbalame zimene zinkapezeka ku Isiraeli chaka chonse.