Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinathandiza mayi wina wa ku Philippines kuti asiye kumwa mowa mwauchidakwa komanso kuti banja lake liyambe kuyenda bwino? Nanga n’chiyani chinathandiza munthu wina wa ku Australia, amene ankakonda kwambiri masewera a karati, kuti asinthe n’kuyamba kumalalikira uthenga wabwino? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene anthuwa ananena.

“Sizinali zophweka kuti ndisinthe.”​—CARMEN ALEGRE

CHAKA CHOBADWA: 1949

DZIKO: PHILIPPINES

POYAMBA: NDINALI CHIDAKWA

KALE LANGA: Ndinabadwira m’tauni ya San Fernando yomwe ili m’chigawo cha Camarines Sur. Koma nditakula, ndinakhala kwambiri m’tauni ya Antipolo, m’chigawo cha Rizal. Tauni imeneyi ili m’dera lamapiri komanso mitengo yambiri. Pa nthawi imene ndinkafika m’tauniyi n’kuti ili yaing’ono ndipo nthawi zambiri anthu sankayenda usiku. Koma panopa tauniyi yakula kwambiri ndipo kuli anthu ambiri.

Nditakhala m’tauniyi zaka zingapo, ndinakumana ndi munthu wina dzina lake Benjamin ndipo kenako tinakwatirana. Banja lathu linali ndi mavuto ngakhale kuti si zimene ndinkayembekezera. Choncho pofuna kuti ndiziiwalako mavuto angawa ndinayamba kumwa mowa mwauchidakwa. Koma kumwa mowa kunachititsa kuti ndikhale wovuta kwambiri ndipo izi zinkaonekera kwambiri ndi mmene ndinkachitira zinthu ndi mwamuna komanso ana anga. Sindinkachedwa kupsa mtima ndiponso sindinkalemekeza mwamuna wanga. Banja lathu linali losasangalala.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Mchemwali wake wa mwamuna wanga, dzina lake Editha, ndi wa Mboni za Yehova ndipo anatiuza kuti zingakhale bwino titayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni. Tinavomera pokhulupirira kuti zimenezi zithandiza kuti banja lathu liyambe kuyenda bwino.

Kuphunzira Baibulo kunatithandiza kudziwa mfundo zambiri zosangalatsa. Mfundo imene inandisangalatsa kwambiri ndi imene ili pa Chivumbulutso 21:4. Lembali limafotokoza za anthu amene adzakhale m’paradaiso padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu ndipo limati Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” Ndinkalakalaka kudzakhala m’gulu la anthu amene adzasangalale ndi madalitso amenewa.

Ndinazindikira kuti ndinkafunika kusintha khalidwe langa. Sizinali zophweka kuti ndisinthe komabe m’kupita kwa nthawi ndinasiya kumwa mowa mwauchidakwa. Ndinaphunziranso kuchita zinthu mokoma mtima komanso moleza mtima ndi banja langa. Komanso ndinaphunzira kulemekeza mwamuna wanga ndi kumugonjera monga mutu wa banja.

Ine ndi mwamuna wanga titayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova, tinachita chidwi kwambiri ndi zimene tinaona. Tinaona kuti a Mboni sachita juga, samwa mowa mwauchidakwa, komanso alibe tsankho. Iwo amalemekeza munthu aliyense. Tinakhulupirira ndi mtima wonse kuti tapeza chipembedzo choona.—Yohane 13:34, 35.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopa banja lathu likuyenda bwino kwambiri ndipo timasangalala kuphunzitsa anthu Baibulo. Ana athu awiri komanso akazi awo nawonso anayamba kuphunzira Baibulo ndipo tikukhulupirira kuti posachedwapa ayamba kutumikira Yehova. Tikuona kuti kutumikira Yehova kwatithandiza kuti tikhale ndi moyo wosangalatsa kwambiri.

Ndinkaona kuti palibe amene angandigonjetse.”​—MICHAEL BLUNSDEN

CHAKA CHOBADWA: 1967

DZIKO: AUSTRALIA

POYAMBA: NDINKAKONDA KWAMBIRI KARATI

KALE LANGA: Ndinakulira mumzinda wokongola komanso wotukuka wotchedwa Albury, ku New South Wales. Mofanana ndi mizinda yambiri, mumzindawu mumachitikanso zinthu zoipa. Komabe, anthu ambiri amaona kuti mzindawu siwoopsa kukhalamo.

Ukwati wa makolo anga unatha ndili ndi zaka 7 komabe sindinakule movutika. Iwo ankaonetsetsa kuti ineyo, mchimwene wanga komanso azichemwali athu awiri sitikusowa chilichonse. Ndinkaphunzira kusukulu inayake yapamwamba ndipo bambo anga ankafuna kuti ndikadzamaliza sukulu ndidzakhale bwana pakampani. Koma ineyo ndinkakonda kwambiri kuchita masewera ndipo ndinali katswiri pa masewera opalasa njinga komanso masewera a karati. Zimenezi zinachititsa kuti nditamaliza sukulu, ndiyambe ntchito pakampani ina yokonza magalimoto ndipo ndinkapeza nthawi yokwanira yochita masewera ndinkakondawo.

Ndinkakonda kwambiri kuchita masewera olimbitsa thupi kuti ndizioneka wamphamvu ndipo nthawi zina ndinkaona kuti palibe amene angandigonjetse. Chifukwa choti ndinali ndi mphamvu zambiri, nthawi zina ndinkasowetsa mtendere anthu ena. Munthu amene ankandiphunzitsa karati ataona kuti ndikugwiritsa ntchito mphamvu zanga molakwika, anayamba kugwiritsa ntchito mfundo zokhwima n’cholinga choti ndikhale waulemu kwambiri. Nthawi zambiri ankandiphunzitsa kufunika kokhala womvera komanso wokhulupirika.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Nditayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova, ndinazindikira kuti Yehova amadana ndi chiwawa. (Salimo 11:5) Poyamba ndinkaganiza kuti karati si masewera achiwawa, koma ndi abwinobwino chifukwa ndinkaona kuti mfundo zimene amatsatira pa masewerawa ndi zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. A Mboni amene ankandiphunzitsa Baibulowo anali oleza mtima kwambiri. Iwo sanandiuze kuti ndisiye karati, m’malomwake ankangondiphunzitsa zimene Baibulo limanena.

Koma nditayamba kudziwa zambiri za m’Baibulo komanso kukonda kwambiri Yehova, ndinayamba kuona kuti masewerawa ndi olakwika. Ndinachita chidwi kwambiri nditaphunzira chitsanzo cha Yesu. Ngakhale kuti Yesu anali ndi mphamvu zambiri, sankachita chiwawa. Ndinakhudzidwa kwambiri ndi mawu ake opezeka pa Mateyu 26:52, amene amati: “Onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.”

Kuphunzira zambiri za Yehova kunachititsa kuti ndiyambe kumukonda komanso kumulemekeza kwambiri. Zinandikhudza kwambiri nditadziwa kuti Mlengi wathu yemwe ndi wanzeru komanso wamphamvu kwambiri amandikonda. Ndinakhudzidwanso nditaphunzira kuti ngati nditapitirizabe kuyesetsa kutumikira Yehova, iye sanganditaye ngakhale nditamulakwira kapena kuganiza zosiya kumutumikira chifukwa choona kuti sindingakwanitse. Ndinalimbikitsidwa kwambiri ndi lonjezo lake lakuti: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’” (Yesaya 41:13) Nditazindikira kuti Yehova wandisonyeza chikondi choterechi, ndinaona kuti ndiyenera kuyesetsa kuti apitirizebe kundikonda.

Ndinkaona kuti kunali kovuta kwambiri kusiya karati koma ndinkadziwa kuti kuchita zimenezi kusangalatsa Yehova. Choncho ndinaona kuti ndiyenera kusiya kuti ndithe kumutumikira. Ndimaona kuti chimene chinandithandiza kwambiri kuti ndisiye karati ndi mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 6:24 akuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri.” Ndinazindikira kuti sindikanatha kutumikira Yehova mokwanira kwinaku n’kumapitirizabe kuchita masewera a karati chifukwa bwenzi ndikutha nthawi yambiri ndikuchita masewerawa m’malo motumikira Yehova. Choncho ndinaona kuti ndiyenera kusankha woti akhale mbuye wanga, Yehova kapena karati ndipo ndinasankha Yehova.

Koma sizinali zophweka kuti ndisiye kuchita masewerawa. Nthawi zina ndinkasangalala podziwa kuti zimene ndikuchita zikusangalatsa Yehova. Komabe pena ndinkaona kuti ndachita zinthu zosakhulupirika kwa aphunzitsi anga a karati aja. Nthawi zambiri anthu amene amachita masewera a karati amaona kuti kukhumudwitsa munthu wina ndi tchimo losakhululukidwa. Anthu ena mpaka amasankha kungodzipha poopa kuti anthu azingokamba za iwowo.

Sindinathe kuwafotokozera aphunzitsi anga a karati chifukwa chake ndinasankha kusiya masewerawa poopa kuti akhumudwa kwambiri. Choncho ndinkangowazemba ndiponso ndinasiya kucheza ndi anzanga amene ndinkasewera nawo karati. Ndinkadziwa kuti ndinachita bwino kwambiri kusiya karati. Komabe ndinkaonanso kuti sindinachite bwino posawafotokozera anzangawo zimene ndinali nditayamba kukhulupirira chifukwa umenewu ukanakhala mwayi wanga woti ndiwalalikire. Choncho ndinkangoona ngati ndakhumudwitsa Yehova ndisanayambe n’komwe kumutumikira. Zimenezi zinkandivutitsa maganizo kwambiri. Nthawi zambiri ndikayamba kupemphera kwa Yehova ndisanamalize ndinkayamba kulira.

Koma Yehova ayenera kuti anaona chinachake chabwino mwa ine chifukwa anachititsa kuti anthu a mumpingo azindithandiza kwambiri. Iwo anali aubwenzi, ankandikonda komanso ankandilimbikitsa kwambiri. Komanso ndinalimbikitsidwa kwambiri ndi nkhani ya m’Baibulo ya Davide ndi Bati-seba. Ngakhale kuti Davide anachita machimo akuluakulu, atalapa mochokera pansi pa mtima Yehova anamukhululukira. Kuganizira kwambiri nkhani imeneyi, kunandithandiza kuona kuti Yehova angandikhululukire zolakwa zanga.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndisanayambe kuphunzira Baibulo, sindinkasamala za munthu, ndinkangoganiza za ine ndekha basi. Koma Yehova, ndiponso mkazi wanga amene ndakhala naye pa banja zaka 7, wandithandiza kuti ndiziganizira za anthu ena. Timaona kuti ndi mwayi wathu kuphunzitsa anthu ambiri Baibulo, omwenso ena mwa iwo anali ndi mavuto osaneneka. Ndimasangalala kwambiri ndikaona anthu akusintha chifukwa chophunzira za Yehova kuposa mmene ndinkasangalalira pa nthawi imene ndinali katswiri wamphamvu wa masewera a karati.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

“Zinandikhudza kwambiri nditadziwa kuti Mlengi wathu yemwe ndi wanzeru komanso wamphamvu kwambiri amandikonda”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 15]

“Zikomo Kwambiri Chifukwa cha Nkhani Zimenezi”

Kodi mwasangalala kuwerenga nkhani zapitazi? Nkhani zimenezi ndi ziwiri chabe mwa nkhani 50 za mutu wakuti “Baibulo Limasintha Anthu” zimene zakhala zikutuluka mu Nsanja ya Olonda kuyambira mu August 2008. Anthu ambiri amene amawerenga magazini athu amakonda kwambiri nkhani zimenezi. Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri amazikonda nkhanizi?

Anthu amene amafotokoza nkhanizi amakhala osiyanasiyana. Ena mwa anthu amenewa, asanayambe kuphunzira za Yehova Mulungu, ankaona kuti zinthu zikuwayendera bwino komabe sankasangalala ndi moyo. Ena anali achiwawa, ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo ena anali zidakwa. Palinso ena amene anaphunzira za Yehova ali ana koma pa nthawi ina anasiya kumutumikira koma kenako anayambiranso. Nkhani zonsezi zikusonyeza kuti munthu akhoza kusintha n’kuyamba kukondweretsa Mulungu. Ndipo nthawi zonse kuchita zimenezi kumapindulitsa. Taonani mmene nkhanizi zinakhudzira anthu amene amakonda kuwerenga magazini athu.

Mayi wina anafotokoza mmene nkhani imene ili mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2009 inathandizira akaidi ena aakazi pandende ina.

▪ Iye anati: “Akaidi ambiri anamvetsa mmene anthu a m’nkhaniyi ankamvera chifukwa nawonso anakumanapo ndi zimene anthuwa anakumana nazo. Akaidiwa anakhudzidwa kwambiri ndi mbiri ya anthu a m’nkhaniyi ndiponso zithuzi za anthuwa asanayambe kuphunzira Baibulo komanso atayamba kuphunzira Baibulo. Akaidi awiri atawerenga nkhanizi, anayamba kuphunzira Baibulo.”—C. W.

Nkhani zimenezi zimakhudza kwambiri mitima ya anthu amene amawerenga magazini athu. Mwachitsanzo mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2011 muli nkhani ya munthu wina, dzina lake Guadalupe Villarreal, yemwe anasiya khalidwe lake logona ndi amuna anzake n’kuyamba kutumikira Yehova. Ambiri mwa anthu amene amawerenga magazini athu atawerenga nkhaniyi, anatilembera makalata. Taonani zina mwa zimene anthu awiri analemba.

▪ “Nkhani ya Guadalupe inandikhudza kwambiri. N’zochititsa chidwi kuona mmene kukonda Yehova ndiponso Mawu ake kungathandizire munthu kuti asinthe kwambiri khalidwe lake.”—L. F.

▪ “Poyamba ndinkayesetsa kulalikira kwa munthu aliyense ngakhalenso anthu amene amagona ndi amuna kapena akazi anzawo. Komabe kenako ndinasiya kulalikira kwa anthu oterewa ndiponso ndinayamba kuwapewa. Koma nkhani imeneyi inandithandiza kwambiri chifukwa ndinayamba kuwaona anthu oterewa mmene Yehova amawaonera. Yehova amawaona kuti akhoza kusintha n’kuyamba kumutumikira.”—M. K.

Nkhani inanso imene inakhudza mitima ya anthu ambiri ndi ya Victoria Tong imene inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2011. Victoria anafotokoza kuti anakula movutika kwambiri. Iye ananena kuti ngakhale kuti anali atatumikira Yehova kwa zaka zambiri, zinkamuvutabe kuvomereza kuti Yehova amamukonda. Koma anafotokozanso zimene kenako zinamuthandiza kuti ayambe kuona kuti Yehova amamukonda. Anthu ena atawerenga nkhani yakeyi ananena zotsatirazi.

▪ “Zimene zinamuchitikira Victoria zinandikhudza kwambiri. Nanenso ndakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wanga. Ngakhale kuti papita zaka zambiri kuchokera pamene ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni, ndimaganizabe kuti mwina Mulungu sangandikonde. Koma nkhani ya Victoria inandithandiza kuti ndiyambe kuona zabwino zimene Yehova amaona mwa ine.”—M. M.

▪ “Ndili mwana, ndinayesetsa kuti ndisiye kuonerera zolaula. Koma posachedwapa ndinapezeka kuti ndaoneranso zolaula. Ndinapempha akulu a kumpingo kwathu kuti andithandize ndipo ndikuyesetsa kuti ndithetse vutoli. Akuluwo ananditsimikizira kuti Mulungu ndi wachikondi komanso wachifundo. Koma nthawi zina ndimaonabe kuti ndine wosafunika ndipo Yehova sangandikonde. Nditawerenga nkhani ya Victoria ndinazindikira kuti ndikamaganiza kuti Mulungu sangandikhululukire, ndiye kuti ndikutanthauza kuti nsembe ya Mwana wake siyokwanira kuphimba machimo anga. Nkhani imeneyi ndinaisunga kuti nthawi iliyonse imene ndayamba kudziona ngati wosafunika ndiziiwerenga n’kusinkhasinkha zimene ndawerengazo. Zikomo kwambiri chifukwa cha nkhani zimenezi.”—L. K.