Zimene Owerenga Amafunsa
N’chifukwa Chiyani Mulungu Anauza Aisiraeli Kuti Asamakwatirane ndi Anthu a Mitundu Ina?
▪ Chilamulo chimene Mulungu anapereka ku mtundu wa Isiraeli chinalinso ndi lamulo ili lokhudza anthu a mitundu ina: “Usadzachite nawo mgwirizano wa ukwati. Usadzapereke ana ako aakazi kwa ana awo aamuna ndipo usadzatenge ana awo aakazi ndi kuwapereka kwa ana ako aamuna.” (Deuteronomo 7:3, 4) Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anapereka lamuloli?
Chifukwa choyamba n’chakuti, Yehova anadziwa kuti Satana ankafuna kusokoneza anthu a Mulungu powachititsa kuti azitumikira milungu yonyenga. N’chifukwa chake ponena za anthu a mitundu ina Mulungu anawauza anthu ake kuti: “Adzapatutsa ana ako aamuna kuti asanditsatire ndipo adzatumikira ndithu milungu ina.” Nkhani imeneyi inali yaikulu chifukwa Mesiya anayenera kubadwira mu mtundu wa Isiraeli. Koma Aisiraeli akanayamba kutumikira milungu ina, Mulungu akanasiya kuwakonda komanso kuwateteza ndipo izi zikanachititsa kuti adani awo awagonjetse. Zimenezi zikanachititsa kuti mtunduwu usatulutse Mesiya wolonjezedwa. Apa n’zoonekeratu kuti Satana ankafuna kuti Aisiraeli akwatire anthu a mitundu ina n’cholinga choti asokoneze mzere wobadwira wa Mesiya.
Chifukwa chachiwiri n’chakuti Mulungu ankadera nkhawa anthu ake aliyense payekha. Iye ankadziwa kuti, kuti munthu akhale wosangalala ayenera kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kodi Yehova anali ndi chifukwa chomveka choletsera kuti anthu ake asamakwatirane ndi anthu a mitundu ina? Taganizirani chitsanzo cha Mfumu Solomo. Iye ankadziwa chenjezo limene Yehova anapereka lokhudza akazi amene satumikira Mulungu lakuti: “Adzapotoza mitima yanu kuti itsatire milungu yawo.” Popeza iye anali wanzeru kwambiri, mwina ankaganiza kuti sakufunika kumvera malangizo a Mulungu chifukwa malangizowo sakumukhudza. Choncho iye sanamvere malangizo a Mulungu pa nkhaniyi. Kodi zotsatira zake zinali zotani? “Akazi amenewa anapotoza mtima wa Solomo . . . moti iye anali kutsatira milungu ina.” Zimenezi zinalitu zomvetsa chisoni kwambiri. Yehova anasiya kumukonda Solomo ndiponso chifukwa cha kusakhulupirika kwakeko Aisiraeli anagawanika.—1 Mafumu 11:2-4, 9-13.
Anthu ena angaganize kuti pa nthawi ina kukwatira anthu a mitundu ina kunalibe vuto kwa Aisiraeli. Mwachitsanzo, Mwisiraeli wina dzina lake Maloni anakwatira mkazi wachimowabu dzina lake Rute ndipo patapita nthawi Rute anayamba kulambira Yehova. Koma zimene Maloni anachitazi zinali zosayenera. Komanso iye anafa adakali mnyamata Rute asanayambe kulambira Yehova. Nayenso Kiliyoni, yemwe anali mchimwene wake wa Maloni, anakwatira mkazi wachimowabu dzina lake Olipa ndipo Olipayo anapitirizabe kulambira “milungu yake.” Koma patapita nthawi Boazi anakwatira Rute ndipo pa nthawiyi n’kuti Rute atayamba kulambira Yehova. Ndipotu Ayuda ankaona kuti Rute “ankalambira Yehova mokhulupirika.” Rute ndi Boazi anadalitsidwa ndi Mulungu.—Rute 1:4, 5, 15-17; 4:13-17.
Si bwino kuganiza kuti chitsanzo cha Maloni ndi Rute chikusonyeza kuti zimene Yehova anauza Aisiraeli sizinali zoona. Kuganiza zimenezi kungafanane ndi kuona munthu wina amene wawina ndalama zambiri pa juga n’kuyamba kuganiza kuti juga ilibe vuto ndipo munthu angathe kumachita juga kuti azisamalira banja lake.
Masiku anonso Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti azikwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.” Limachenjezanso Akhristu kuti sayenera ‘kumangidwa m’goli ndi osakhulupirira, chifukwa ndi osiyana.’ Malangizo amenewa akupita kwa Akhristu oona amene akufuna munthu woti akwatirane naye. Kwa anthu amene anakwatirana kale ndi munthu amene amakhulupirira zosiyana ndi zimene iwowo amakhulupirira, Baibulo limawapatsa malangizo amene angawathandize kudziwa zochita pa mavuto amene amakumana nawo. (1 Akorinto 7:12-16, 39; 2 Akorinto 6:14) Malangizo onsewa amasonyeza kuti Yehova Mulungu, yemwe ndi amene anayambitsa ukwati, amafuna kuti atumiki ake azikhala osangalala, kaya ali pa banja kapena ayi.