Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Achinyamata Achite

Mulungu Amadana Ndi Zinthu Zopanda Chilungamo

Mulungu Amadana Ndi Zinthu Zopanda Chilungamo

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezani kuti inuyo mukuona zimene zikuchitikazo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mu mtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Ahabu, Yezebeli, Naboti ndi Eliya

Chidule cha nkhaniyi: Mfumu Ahabu inalimbikitsidwa ndi Yezebeli kuti iphe munthu n’cholinga chakuti itenge munda wa mpesa.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.—WERENGANI 1 MAFUMU 21:1-26.

Kodi mukuganiza kuti anthu awa, omwe atchulidwa m’nkhaniyi, ankaoneka bwanji?

Ahabu

Yezebeli ․․․․․

Naboti ․․․․․

Eliya ․․․․․

Pamene Ahabu ndi Yezebeli amalankhulana zimene zatchulidwa m’vesi 5 mpaka 7, kodi mukuganiza kuti mawu awo ankamveka bwanji?

․․․․․

Pomwe zimene zatchulidwa m’vesi 13 zinkachitika, kodi mukuganiza kuti panali phokoso lotani?

․․․․․

Pamene Eliya ndi Ahabu amalankhulana zimene zili m’vesi 20 mpaka 26, kodi mukuganiza kuti ankamva bwanji?

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Kodi vesi 7 ndi 25, likusonyeza kuti Yezebeli anali ndi makhalidwe otani?

․․․․․

Kodi vesi 4 likusonyeza kuti Ahabu anali ndi makhalidwe otani?

․․․․․

Kodi winanso ndani amene anaphedwa chifukwa choti Ahabu anafuna kutenga munda wa Naboti? (Werengani 2 Mafumu 9:24-26.)

․․․․․

Kodi Yehova ankaona kuti Ahabu anali munthu wotani? (Werenganinso vesi 25 ndi 26. Onaninso 1 Mafumu 16:30-33.)

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Mfundo yoti Yehova amaona zinthu zopanda chilungamo zimene zimachitika.

․․․․․

Mfundo yoti Yehova zimamukhudza akamaona anthu akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo.

․․․․․

Mmene Yehova amasonyezera kuti ndi Mulungu wachilungamo. (Werengani Deuteronomo 32:4.)

․․․․․

4 MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Kodi anthu ena masiku ano amasonyeza bwanji mtima ngati wa Yezebeli? (Werengani Chivumbulutso 2: 18-21.)

․․․․․

Kodi ndi pa zinthu ziti pamene inunso mungafunike kusonyeza kulimba mtima ngati mmene Eliya anachitira?

․․․․․

Anthu ena akamakuchitirani zinthu zopanda chilungamo, kodi muyenera kukhulupirira chiyani?

․․․․․

5 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Mungachite Izi: Yerekezani kuti ndinu mtolankhani ndipo mukupereka lipoti la nkhaniyi pa wailesi kapena pa TV. Fotokozani zimene zinachitika ndipo mufunse mafunso anthu amene akutchulidwa m’nkhaniyi komanso amene anaona pamene zinthuzo zinkachitika.

Mukhozanso Kuwerenga Nkhaniyi pa Adiresi iyi: www.jw.org/ny

Mungathenso Kuwerenga Baibulo pa Adiresi Yomweyi

Mungathe Kukopera Kapena Kupulinta Nkhaniyi