Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

 Baibulo Limasintha Anthu

Kodi mayi amene ankazembetsa miyala ya diamondi komanso kuwabera abwana ake anasintha bwanji kukhala woona mtima? Kodi mayi amene ankafuna kudzipha maulendo awiri anayamba bwanji kusangalala ndi moyo wake? Kodi n’chiyani chinathandiza munthu wina amene ankamwa mowa kwambiri ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kuti asiye zinthu zimenezi? Onani zimene anena.

ZA MUNTHUYU

DZINA: MARGARET DEBRUYN

ZAKA: 45

DZIKO: BOTSWANA

POYAMBA: ANKAZEMBETSA KATUNDU NDIPONSO ANALI MBALA

KALE LANGA: Kwawo kwenikweni kwa bambo anga ndi ku Germany koma anadzakhala nzika ya dziko la South-West Africa (panopa ndi ku Namibia). Kwawo kwa amayi anga ndi ku Botswana ndipo anali a mtundu wa Mangologa. Ndinabadwira ku Gobabis, ku Namibia.

Mu 1970, boma la South Africa linkalamulira dziko la Namibia ndipo linkalimbikitsa malamulo atsankho m’matauni ndi m’midzi yonse. Makolo anga anali osiyana mitundu, ndipo zimenezi zinapangitsa kuti ukwati wawo uthe. Choncho ine ndi amayi anga komanso abale anga tinabwerera ku Botswana, ndipo tinakakhala ku Ghansi.

Mu 1979, ndinasamukira ku Lobatse ku Botswana komweko ndipo ndinkakhala ndi banja lina mpaka ndinamaliza sukulu. Kenako ndinayamba ntchito yaukalaliki pa galaja ina. Kuyambira ndili wamng’ono, ndinkakhulupirira kuti Mulungu samatisamalira ndipo tiyenera kuchita chilichonse, kaya zikhale zinthu zabwino kapena zoipa, kuti tipeze zomwe tikufuna komanso kuti tithe kusamalira mabanja athu.

Popeza ndinali ndi udindo wapamwamba kuntchito, ndinkagwiritsa ntchito mwayi umenewo kuba zitsulo za galimoto. Nthawi zonse sitima ikamadutsa usiku m’tawuni imene ndinkakhala, ine ndi anzanga tinkakwera ndi kuba chilichonse chomwe tingakwanitse. Komanso ndinayamba kuzembetsa miyala ya diamondi, ya golide ndiponso miyala ina. Ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuchita zachiwawa, ndiponso ndinali ndi zibwenzi zambiri.

Ndiyeno mu 1993, ndinagwidwa ndikuba ndipo anandichotsa ntchito. Azinzanga anandithawa, poopa kuti nawonso angagwidwe. Kundithawa kwa azinzangawa kunandipweteka zedi, ndipo sindinkakhulupiriranso aliyense.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Mu 1994, ndinakumana ndi amishonale  awiri a Mboni za Yehova, Tim ndi Virginia. Anandipeza kuntchito kwanga kwatsopano, ndipo anandithandiza kuphunzira Baibulo panthawi yopuma. Nditaona kuti ndikhoza kuwadalira, ndinawauza kuti tizichitira phunziroli kunyumba kwanga.

Posakhalitsa ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kusangalatsa Mulungu, ndiyenera kusintha khalidwe langa. Mwachitsanzo, ndinaphunzira pa 1 Akorinto 6:9, 10 kuti “adama, . . . akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” Ndinayamba kusiya pang’onopang’ono zoipa zimene ndinkachita. Ndinasiya kuba ndiponso kucheza ndi anthu achifwamba amene ndinkacheza nawo kuyambira ndili mwana. Komanso mwamphamvu ya Yehova ndinathetsa zibwenzi.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndimayesetsa kuti ndisamapse mtima msanga komanso kuti ndisamawakalipire kwambiri ana anga akalakwitsa zinthu. (Aefeso 4:31) Ndimayesetsa kulankhula modekha ndipo zimenezi zathandiza banja lathu kuti likhale logwirizana.

Anzanga akale, ndi anthu oyandikana nawo nyumba, tsopano akudziwa kuti ndine munthu wodalirika. Ndine wantchito woona mtima komanso wokhulupirika, wosamala katundu ndi ndalama zomwe. Chifukwa cha zimenezi ndimatha kudzisamalira popeza ndimathera nthawi yambiri ndikuthandiza anthu ena kudziwa Baibulo. Ndimaona kuti mawu a pa Miyambo 10:22 ndi oona kwambiri. Mawuwo amati: “Madalitso a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni.”

ZA MUNTHUYU

DZINA: GLORIA ELIZARRARÁS DE CHOPERENA

ZAKA: 37

DZIKO: MEXICO

POYAMBA: ANKAFUNA KUDZIPHA

KALE LANGA: Ndinakulira m’dera lolemera la Naucalpan, m’dziko la Mexico. Kuyambira ndili mwana, ndinali wamphulupulu ndipo ndinkakonda kupita kumaphwando. Ndinayamba kusuta fodya ndili ndi zaka 12, kumwa mowa ndili ndi zaka 14, ndipo ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndili ndi zaka 16. Patapita zaka zochepa, ndinachoka pakhomo pa makolo anga. Anzanga ambiri anali ochokera m’mabanja osokonekera, ndipo anali andewu ndi olalata. Moyo sunkandikomera moti ndinayesa kudzipha kawiri konse.

Ndili ndi zaka 19, ndinayamba ntchito yojambulitsa zinthuzi zotsatsira malonda. Ntchito imeneyi inachititsa kuti ndizicheza ndi anthu andale ndiponso azisudzo. Patapita nthawi ndinakwatiwa ndipo ndinali ndi ana, komabe ine ndi amene ndinkasankha zochita zonse m’banja lathu. Ndinapitiriza kusuta ndi kumwa mowa, ndipo ndinkangokhalira kupita ku zisangalalo. Ndinkakonda nkhani ndi nthabwala zotukwana komanso ndinkapsa mtima msanga.

Anthu ambiri amene ndinkacheza nawo analinso ndi makhalidwe omwewa. Iwo ankaona kuti ndinkasangalala kwambiri. Koma moyo wanga unali wosasangalatsa, wopanda cholinga.

 MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova mu 1998. Ndinaphunzira m’Baibulo kuti moyo uli ndi cholinga. Ndinaphunziranso kuti Yehova Mulungu akufuna kubwezeretsa dzikoli kukhala Paradaiso. Ndiponso kuti adzaukitsa akufa komanso kuti ndikhoza kudzakhala nawo m’dziko limeneli.

Ndipo ndinaphunziranso kuti tingasonyeze kuti timamukonda Mulungu mwa kumumvera. (1 Yohane 5:3) Poyamba zimenezi zinali zondivuta chifukwa sindinkamvera munthu aliyense. Komabe, m’kupita kwa nthawi ndinazindikira kuti zinthu sizingandiyendere bwino ngati ndiyendera nzeru zanga zokha. (Yeremiya 10:23) Ndinapempha Yehova kuti anditsogolere komanso kuti andithandize kusintha moyo wanga kuti ugwirizane ndi malamulo ake. Ndinamupemphanso kuti andithandize kuphunzitsa ana anga kukhala ndi moyo wosiyana ndi umene ndinali nawo poyamba.

Zinkandivuta kwambiri kusintha khalidwe, koma ndinayamba kutsatira malangizo opezeka pa Aefeso 4:22-24, akuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale. . . ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo choona ndi kukhulupirika.” Kuti ndivale umunthu watsopano ndinafunika kusiya makhalidwe oipa monga kusuta ndi kutukwana, n’kuyamba kulankhula bwino. Zinanditengera zaka pafupifupi zitatu kuti ndisiyiretu makhalidwe amenewa n’kufika pobatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova.

Ndinayamba kuona udindo wanga monga wokwatiwa ndiponso mayi kukhala wofunika. Ndinayamba kutsatira malangizo a pa 1 Petulo 3:1, 2 akuti: “Inu akazi, muzigonjera amuna anu, kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.”

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa tsopano ndikudziwa kuti moyo uli ndi cholinga. Ndikuona kuti ndakhala munthu wabwino ndipo ndikutha kulera bwino ana anga. Nthawi zina, ndimavutika mu mtima chifukwa cha zimene ndinkachita kale, koma Yehova amadziwa mtima wanga. (1 Yohane 3:19, 20) Ndithudi, kutsatira mfundo za m’Baibulo kwanditeteza ndiponso kwandithandiza kukhala ndi mtendere wa mu mtima.

ZA MUNTHUYU

DZINA: JAILSON CORREA DE OLIVEIRA

ZAKA: 33

DZIKO: BRAZIL

POYAMBA: ANKAMWA MOWA KWAMBIRI NDI KUGWIRITSA NTCHITO MANKHWALA OSOKONEZA BONGO

KALE LANGA: Ndinabadwira ku Brazil mu mzinda wa Bagé, wa anthu pafupifupi 100,000. Mzindawu uli m’malire a dziko la Brazil ndi Uruguay. Anthu a m’derali ankadalira ulimi ndi kuweta ziweto. Ndinakulira m’boma losauka kumene kunali achifwamba oopsa kwambiri, ndipo achinyamata ankakonda kumwa mowa kwambiri ndi kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Nditasiya sukulu, ndinayamba kumwa mowa, kusuta chamba ndi kumvetsera nyimbo za phokoso kwambiri. Sindinkakhulupirira Mulungu ndipo ndinkaona kuti mavuto komanso chipwirikiti cha m’dzikoli ndi umboni wakuti kunja kuno kulibe Mulungu.

 Ndinkaimba gitala ndi kulemba nyimbo ndipo nthawi zambiri ndinkachita zimenezi chifukwa cha zimene ndinkawerenga m’Baibulo m’buku la Chivumbulutso. Gulu langa loimba silinkachita bwino monga mmene ndinkayembekezera, choncho ndinayamba kugwiritsa ntchito kwambiri mankhwala osokoneza bongo. Sindinkaopa kuti ndingafe ndi mankhwalawa chifukwa oimba ambiri amene ndinkawakonda anafanso imfa yotero.

Ndinkabwereka ndalama zogulira mankhwalawa kwa agogo anga amene anandilera. Akandifunsa kuti ndalama n’zachiyani, ndinkawanamiza. Ndinafika pokhulupirira mizimu komanso zamatsenga, poganiza kuti zizindithandiza kuti ndizilemba nyimbo zabwino.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Nditayamba kuphunzira Baibulo ndi kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova, khalidwe langa linayamba kusintha. Pang’onopang’ono ndinayamba kusangalala ndi moyo. Chifukwa choti ndinasintha mwanjira imeneyi, ndinaganizanso zometa tsitsi langa limene linali lalitali. Poyamba sindinkameta pofuna kusonyeza mtima wovutitsa. Ndiyeno ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kuti Mulungu azindikonda, ndiyenera kusiya kumwa mowa kwambiri, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso kusiya kusuta. Ndinaonanso kuti ndinayenera kusintha nyimbo zimene ndinkakonda.

Paulendo woyamba kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova, ndinawerenga lemba la m’Baibulo pakhoma. Linali lochokera pa Miyambo 3:5, 6, limene limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” Poganizira lemba limeneli, ndinaona kuti Yehova andithandiza kusintha moyo wanga, ndikamulola kutero.

Komabe, kusiya makhalidwe amene ndinkawakonda kwambiri ndiponso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kunali kovuta kwambiri ngati kudula dzanja langa. (Mateyo 18:8, 9) Sindikanakwanitsa kusiya makhalidwe amenewa pang’onopang’ono. Ndinkadziwa kuti sindingathe kusiya mwanjira imeneyi, motero ndinaganiza zosiya kamodzin’kamodzi. Ndinasiyanso kupita malo onse amene akanandipangitsa kuyambiranso moyo wanga wakale ndipo ndinasiyanso kucheza ndi anthu amakhalidwe oipa.

Ndinaphunzira kusangalala ndi zimene ndakwanitsa kuchita tsiku lililonse, osati kuganizira kwambiri zimene ndalephera kuchita. Ndinkaona kuti ndi mwayi wapadera kukhala woyera mwakuthupi, mwamakhalidwe ndiponso mwauzimu kuti ndikhale paubwenzi wabwino ndi Yehova. Ndinkapemphera kuti Yehova andithandize kuti ndiziika maganizo pa zam’tsogolo osati pa kale langa. Nthawi zina ndinkapezeka kuti ndachita zinthu zoipa zimene ndinkachita kale. Ngakhale kuti nthawi zina ndinkakhala ndi matsire, ndinkalolabe kuti munthu amene ankandiphunzitsa Baibulo apitirize kundiphunzitsa.

Ndinaphunzira choonadi cha m’Baibulo chakuti Mulungu amasamalira munthu aliyense payekha, kuti adzawononga chipembedzo chonyenga, ndiponso kuti akuthandiza anthu pantchito yolalikira yapadziko lonse. Ndipo ndinaona kuti mfundo zimenezi n’zomveka. (Mateyo 7:21-23; 24:14; 1 Petulo 5:6, 7) Kenako ndinapatulira moyo wanga kwa Mulungu pofuna kusonyeza kuyamikira zonse zimene anandichitira.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopa ndimaona kuti moyo wanga uli ndi cholinga. (Mlaliki 12:13) Ndipo m’malo mobera abale anga, ndakwanitsa kuwabwezera. Ndinkawauza agogo anga zimene ndinkaphunzira kuchokera m’Baibulo, ndipo ndikunena pano anadzipatulira kwa Yehova. Anthu ena angapo m’banja lathu ndiponso wina amene ankaimba m’gulu lathu anachitanso chimodzimodzi.

Panopo ndinakwatira, ndipo ine ndi mkazi wanga timathera nthawi yambiri tikuthandiza anthu kuphunzira Baibulo. Ndikuona kuti ndapindula kwambiri chifukwa chophunzira ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wanga wonse.’

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Pang’onopang’ono ndinayamba kusangalala ndi moyo”