Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ndani?

Kodi Mulungu Ndani?

 Kodi Mulungu Ndani?

KODI mungayankhe bwanji funso limeneli? Anthu ena amaganiza kuti amamudziwa bwino Mulungu, moti amati ndi bwenzi lawo lapamtima. Komabe anthu ena amamuona kuti si bwenzi lawo kwenikweni. Iwo amangokhulupirira kuti Mulungu aliko koma samudziwa bwino. Ngati mumakhulupirira Mulungu, kodi mungayankhe bwanji mafunso awa:

1. Kodi Mulungu ndi munthu weniweni?

2. Kodi Mulungu ali ndi dzina?

3. Kodi Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse?

4. Kodi Mulungu amasamala za ine?

5. Kodi Mulungu amavomereza kulambira kwina kulikonse?

Mutafunsa anthu ena mafunso amenewa, angayankhe mosiyanasiyana. Choncho n’zosadabwitsa kuti pali nkhani zabodza komanso zikhulupiriro zosiyanasiyana zonena za Mulungu.

N’Chifukwa Chiyani N’kofunika Kudziwa Mayankho a Mafunso Amenewa?

Yesu Khristu akulankhula ndi mayi wina wopemphera amene anakumana naye pachitsime, anatsindika kuti n’kofunika kudziwa zoona ponena za Mulungu. Mayi ameneyu, yemwe anali wachisamariya, anavomereza kuti Yesu anali mneneri. Koma chinachake chinali kumuvutitsa maganizo. Iye anali m’chipembedzo chosiyana ndi cha Yesu. Atamuuza vutoli, Yesu anamuuza momveka bwino kuti: “Inu mumalambira chimene simuchidziwa.” (Yohane 4:19-22) Apa n’zoonekeratu kuti Yesu ankadziwa kuti si anthu onse opemphera amene amamudziwadi Mulungu.

 Kodi mawu a Yesu amenewa akutanthauza kuti palibe angamudziwedi Mulungu? Ayi, sakutanthauza zimenezo, chifukwa Yesu anauza mayi uja kuti: “Olambira oona adzalambira Atate ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:23) Kodi inuyo muli m’gulu la anthu amene amalambira Mulungu “ndi mzimu ndi choonadi”?

N’kofunika kwambiri kuti mudziwe yankho la funso limeneli. Kodi n’chifukwa chiyani tikutero? Yesu anatsindika kuti kudziwa zolondola n’kofunika kwambiri. Iye anapemphera kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.” (Yohane 17:3) Inde, moyo wanu wam’tsogolo ukudalira kwambiri kudziwa zoona ponena za Mulungu.

Kodi n’zothekadi kudziwa zoona ponena za Mulungu? Inde, n’zotheka. Koma kodi mungamudziwe bwanji? Ponena za iyemwini, Yesu anati: “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Iye ananenanso kuti: “Atateyo palibe amene akum’dziwa bwino koma Mwana yekha, ndi amene Mwanayo wakonda kuwaululira za Atateyo.”​—Luka 10:22.

Choncho, chinsinsi chodziwa Mulungu chagona pa zimene Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu anaphunzitsa. Ndipotu, Yesu analonjeza kuti: “Ngati mukhala m’mawu anga, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga, mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:31, 32.

Koma kodi Yesu angayankhe bwanji mafunso asanu ali kumayambiriro aja?

[Chithunzi patsamba 4]

Kodi mumalambira Mulungu amene simum’dziwa bwino?