Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse?

Kodi Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse?

 Kodi Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse?

Ambiri amanena kuti:

▪ “Inde, Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse.”

▪ “Yesu ndi dzina la Mulungu atabwera padziko lino lapansi.”

Kodi Yesu anati chiyani?

▪ “Ngati munali kundikonda, mukanakondwera kuti ndikupita kwa Atate wanga, chifukwa Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28) Yesu ananena kuti iye ndi Atate wake si munthu mmodzi.

▪ “Ine ndikukwera kwa Atate wanga ndi Atate wanu, ndi kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17) Yesu sananene kuti iye ndi Mulungu, koma ananena kuti Mulungu ndi Munthu wina.

▪ “Sindinalankhulepo zongoganiza pandekha, koma Atate amene ananditumayo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula.” (Yohane 12:49) Yesu samaphunzitsa nzeru zake, koma zochokera kwa Atate.

YESU ananena kuti ndi Mwana wa Mulungu, osati Mulungu Wamphamvuyonse. Ngati Yesu ndi Mulungu, kodi ankapemphera kwa ndani ali pano padziko lapansi? (Mateyo 14:23; 26:26-29) Sizingakhale zomveka kuganiza kuti Yesu amangoyerekezera kuti akulankhula ndi munthu wina.

Ophunzira ake awiri atam’pempha malo apadera m’Ufumu wake, iye anati: “Kunena zokhala kudzanja langa lamanja ndi kumanzere kwanga, si ine wopereka mwayi umenewo, koma Atate wanga adzaupereka kwa amene Atatewo anawakonzera.” (Mateyo 20:23) Kodi Yesu anali kuwanamiza powauza kuti analibe udindo wochita zimene anapemphazo? Ayi, samanama. Iye modzichepetsa anazindikira kuti ndi udindo wa Mulungu yekha kuchita zimenezi. Yesu anafotokozanso kuti panali zinthu zina zimene iye ndi angelo samazidziwa, koma Atate okha ndi amene amazidziwa.​—Maliko 13:32.

Kodi Yesu anali wamng’ono kwa Mulungu ali padziko lapansi pano pokha? Ayi. Ngakhale atamwalira ndi kuukitsidwa, Baibulo limafotokoza kuti iye anali wamng’ono kwa Mulungu. Mtumwi Paulo amatiuza kuti “mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Baibulo limanena kuti kutsogoloku “zinthu zonse zikadzakhala pansi pake [pansi pa ulamuliro wa Khristu], Mwanayonso adzadziika pansi pa Uyo amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.”​—1 Akorinto 15:28.

N’zoonekeratu kuti Yesu si Mulungu Wamphamvuyonse. N’chifukwa chake anawatchula Atate wake kuti “Mulungu wanga.”​—Chivumbulutso 3:2, 12; 2 Akorinto 1:3, 4. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Kuti mumve zambiri pankhani imeneyi, onani buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? masamba 201 mpaka 204.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Yesu ananena kuti panali zinthu zina zimene iye ndi angelo samazidziwa, koma Atate okha ndi amene amazidziwa