Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?

Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?

Kodi Mulungu Ali ndi Dzina?

Ambiri amanena kuti:

▪ “Dzina lake ndi Mulungu.”

▪ “Alibe dzina lake lenileni.”

Kodi Yesu anati chiyani?

▪ “Choncho inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.’” (Mateyo 6:9) Yesu ankakhulupirira kuti Mulungu ali ndi dzina.

▪ “Dzina lanu ndalidziwitsa kwa iwo ndipo ndidzalidziwitsabe, kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.” (Yohane 17:26) Yesu anathandiza anthu kudziwa dzina la Mulungu.

▪ “Simudzandionanso kufikira pamene mudzanena kuti, ‘Wodalitsika iye wobwera m’dzina la Yehova!’” (Luka 13:35; Salmo 118:26) Yesu ankagwiritsa ntchito dzina la Mulungu.

MULUNGU anatiuza yekha dzina lake. Iye ananena kuti: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli.” * (Yesaya 42:8) M’chichewa, dzina lodziwika kwambiri lochokera ku dzina lachiheberi limene Mulungu anadzipatsa ndi lakuti Yehova. Mungadabwe kumva kuti dzina lachiheberi lapaderali limapezeka maulendo ambiri m’mipukutu yakale ya Baibulo. Ndipo ndi limene limapezeka kwambiri m’Baibulo kuposa mayina ena onse.

Anthu ena akafunsidwa kuti, “Kodi dzina la Mulungu ndani? Amayankha kuti, “Mulungu ndi Mulungu.” Munthu woyankha choncho angafanane ndi munthu amene angayankhe kuti “Wopikisana,” atafunsidwa kuti, “Kodi ndani wapambana pa chisankho?” Mayankho amenewa siomveka chifukwa mayina akuti “Mulungu” ndi “Wopikisana” si mayina enieni.

Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anatiuza dzina lake? Anachita zimenezi kuti timudziwe bwino. Mwachitsanzo, munthu angatchedwe kuti Bambo, Bwana kapena Agogo malingana ndi udindo umene ali nawo. Mayina aulemu amenewa amasonyeza kenakake ponena za munthuyo. Koma dzina lake lenileni limatikumbutsa zonse zimene tikudziwa za munthuyo. N’chimodzimodzi ndi mayina aulemu monga akuti Ambuye, Wamphamvuyonse, Atate, ndiponso Mlengi, amatikumbutsa zosiyanasiyana zimene Mulungu wachita. Koma ndi dzina lake lenileni lokha, lakuti Yehova, limene limatikumbutsa zonse zimene tikudziwa ponena za iye. Ndithudi, sitingamudziwe Mulungu popanda kudziwa dzina lake.

M’pofunika kwambiri kudziwa dzinali ndiponso kuligwiritsa ntchito. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Baibulo limatiuza kuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”​—Aroma 10:13; Yoweli 2:32.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Kuti mumve tanthauzo la dzina la Mulungu komanso kuti mudziwe chifukwa chake m’Mabaibulo ena mulibe dzinali, onani buku lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? masamba 195 mpaka 197.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Munthu angatchedwe kuti Bambo, Bwana kapena Agogo malingana ndi udindo umene anali nawo. Koma dzina lake lenileni limatikumbutsa zonse zimene tikudziwa za munthuyo