Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Amamva Mapemphero Athu?

Kodi Ndani Amamva Mapemphero Athu?

 Kodi Ndani Amamva Mapemphero Athu?

NGATI pali winawake amene amamvetsera mapemphero athu ndiye kuti ayenera kukhala Mlengi. Tikutero chifukwa palibe aliyense amene amadziwa zamumtima mwa munthu kupatulapo amene analenga ubongo wa anthu. Choncho iye ndi amene angamve mapemphero a anthu ndi kuwapatsa zofunika zawo. Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi pali chifukwa chokhulupirira zoti kuli Mlengi?’

Anthu ambiri amaganiza kuti n’zosatheka kuti munthu amene amakhulupirira zimene asayansi amasiku ano amanena, azikhulupiriranso zoti kuli Mulungu. Komatu maganizo oti kukhulupirira Mulungu n’kosagwirizana ndi sayansi si oona. Taganizirani chitsanzo chotsatirachi.

▪ Zotsatira za kafukufuku amene anachitika posachedwapa, pomwe anafunsa aphunzitsi asayansi okwana 1,646 ochokera m’mayunivesite akuluakulu 21 a ku America, zinasonyeza kuti mphunzitsi mmodzi yekha pa atatu alionse ndi amene samakhulupirira Mulungu.

Apa zikuonekeratu kuti akatswiri ambiri asayansi amakhulupirira zoti kuli Mulungu.

Umboni Wakuti Kuli Mlengi

Kodi ndi bwino kungokhulupirira zoti kuli Mulungu popanda umboni uliwonse? Ayi. Maganizo oti munthu wachikhulupiriro ayenera kumangokhulupirira zilizonse popanda umboni si olondola. Baibulo limafotokoza kuti chikhulupiriro ndi “umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” (Aheberi 11:1) Baibulo lina linamasulira kuti chikhulupiriro ndi “kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu.” (Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Mwachitsanzo, simungathe kuona mphepo. Koma mukaona masamba a mitengo akugwedera, mumazindikira kuti mphepo ikuwomba. Choncho mumadziwa kuti mphepo iliko ngakhale kuti sitingaione. N’chimodzimodzinso ndi Mulungu, ngakhale kuti sitingathe kumuona, tingathe kuona  umboni umene ulipo womwe ungatithandize kutsimikizira kuti iye alipodi.

Kodi tingapeze kuti umboni wakuti Mulungu alikodi? Umboni umenewu umapezeka paliponse pamene tili. Baibulo limafotokoza kuti: “N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheberi 3:4) Kodi mukukhulupirira kuti mawu amenewa ndi oona? Mukaganizira za zinthu monga, dongosolo la zinthu m’chilengedwechi, mmene moyo umayambira, mmene ubongo wa munthu, womwe ndi chinthu chodabwitsa kwambiri padziko lonse lapansi, umagwirira ntchito, mwina mumaona kuti payenera kuti pali winawake amene analenga zimenezi. *

Komabe sikuti chilengedwe chingatiphunzitse zonse zokhudza Mulungu. Kudziwa kuti Mulungu alipo pogwiritsa ntchito chilengedwe tingakuyerekezere ndi kudziwa kuti kunja kwa nyumba yanu kukubwera munthu pongomvera mdidi ngakhale kuti munthuyo simukumuona. Kuti mudziwe kuti munthuyo ndi ndani mufunika kutsegula chitseko. Tiyeneranso kuchita chimodzimodzi kuti tidziwe amene analenga zinthu zonse.

Baibulo lili ngati chitseko chomwe tingatsegule kuti tidziwe Mulungu. Kuwerenga Baibulo komanso kuphunzira mmene maulosi ena anakwaniritsidwira, kungakuthandizeni kutsimikiza kuti Mulungu alikodi. * Kuwonjezera pamenepo, nkhani zokhudza mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi anthu zimatithandiza kudziwa makhalidwe a Mulungu yemwe ndi Wakumva pemphero.

Kodi Wakumva Pemphero Ameneyu Ndi Wotani?

Baibulo limatiuza zokhudza Wakumva pemphero  ameneyu ndipo tingathe kumudziwa bwino. Iye amamvetsera tikamapemphera ndipo amamvetsa zimene tikunenazo. Baibulo limati: “Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu,” ndipo mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri. (Salimo 65:2) Baibulo limasonyeza kuti iye ali ndi dzina ndipo amamva mapemphero a anthu amene amapemphera kwa iye ndi chikhulupiriro. Baibulo limati: “Yehova amakhala kutali ndi anthu oipa, koma amamva pemphero la anthu olungama.”—Miyambo 15:29.

Yehova ali ndi makhalidwe abwino osiyanasiyana ndiponso amakhudzidwa ndi zochita za anthu. Iye ndi “Mulungu wachikondi” komanso ndi “Mulungu wachimwemwe.” (2 Akorinto 13:11; 1 Timoteyo 1:11) Baibulo limafotokoza kuti Yehova “zinam’pweteka kwambiri mumtima” pa nthawi yomwe padzikoli pankachitika zinthu zoipa kwambiri. (Genesis 6:5, 6) Zimene anthu ena amanena zoti Mulungu amachititsa mavuto pofuna kuyesa anthu, si zoona. Baibulo limati: “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe.” (Yobu 34:10) Komabe mwina mungadabwe kuti, ‘Ngati Mulungu ndi Mlengi Wamphamvuyonse, n’chifukwa chiyani walola kuti mavuto azipitirirabe?’

Yehova anapatsa anthu ufulu wosankha zochita ndipo zimenezi zimatithandiza kudziwa kuti iye ndi Mulungu wotani. Kodi sitiyamikira kuti tili ndi ufulu wosankha zimene tikufuna kuchita pa moyo wathu? Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri samagwiritsa ntchito bwino ufulu umenewu ndipo amadzibweretsera mavuto komanso amabweretsa mavuto kwa anthu ena. Choncho funso lofunika kwambiri kuliganizira ndi lakuti: Kodi Mulungu adzachotsa bwanji mavuto padzikoli popanda kuwaphera anthu ufulu? Nkhani yotsatira ikuyankha funso limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yakuti Mulungu aliko, onani kabuku kachingelezi kakuti The Origin of Life—Five Questions Worth Asking komanso buku lachingelezi lakuti Is There a Creator Who Cares About You? Mabuku amenewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 10 Kabuku kakuti Buku la Anthu Onse ndiponso buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? omwe ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova analembedwa n’cholinga chokuthandizani kudziwa umboni wakuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu.

[Bokosi patsamba 5]

Kodi Zinthu Zoipa Zomwe Chipembedzo Chimachita Zimakuchititsani Kukayikira Zoti Kuli Mulungu?

N’zomvetsa chisoni kuti chipembedzo ndi chimene chimachititsa kuti anthu ambiri azikayikira ngati kuli Mulungu wachikondi yemwe amamva mapemphero. Zimene chipembedzo chimachita monga kulowerera mu nkhondo, kuchita zinthu zauchigawenga komanso kulekerera khalidwe lochitira nkhanza ana, zapangitsa anthu ambiri, ngakhalenso opemphera, kunena kuti: “Sindikhulupirira kuti kuli Mulungu.”

Kodi n’chifukwa chiyani nthawi zambiri chipembedzo chimachita zinthu zoipa? Mwachidule tingati n’chifukwa chakuti, anthu ena amachita zinthu zoipa m’dzina la chipembedzo. Baibulo linalosera kuti anthu ena azidzagwiritsa ntchito chipembedzo pofuna kukwaniritsa zofuna zawo zoipa. Mtumwi Paulo anauza oyang’anira achikhristu kuti: “Pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.”—Machitidwe 20:29, 30.

Mulungu amanyansidwa kwambiri ndi zipembedzo zonyenga. Ndipotu Mawu ake, Baibulo, amati zipembedzo zonyenga zili ndi mlandu ‘wamagazi a . . . onse amene anaphedwa padziko lapansi.’ (Chivumbulutso 18:24) Zipembedzo zonyenga zalephera kuwaphunzitsa anthu zoona zokhudza Mulungu, yemwe khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. Chifukwa cha zimenezi Mulungu amaona kuti zipembedzozi zili ndi mlandu wamagazi.—1 Yohane 4:8.

Mulungu, yemwe ndi Wakumva pemphero, amakhudzidwa kwambiri akamaona anthu akuponderezedwa ndi zipembedzo zonyenga. Chifukwa chakuti Mulungu amakonda anthu, posachedwapa iye adzagwiritsa ntchito Yesu kuweruza anthu amene amati amamupembedza koma amachita zinthu zachinyengo. Yesu anati: “Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosere m’dzina lanu?’ . . . Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: Sindikukudziwani ngakhale pang’ono! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.”—Mateyu 7:22, 23.