Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena
Kodi Zochita za Angelo Ndiponso Ziwanda Zimakhudza Bwanji Anthufe?
Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.
1. Kodi angelo ndi ndani?
Angelo ndi zolengedwa zauzimu ndipo amakhala kumwamba. Iwo ndi apamwamba kwambiri kuposa anthu. Mulungu woona, yemwe nayenso ndi mzimu, ndi amene analenga angelo asanalenge dziko lapansi. (Yobu 38:4, 7; Mateyu 18:10) Pali angelo mamiliyoni ambiri okhulupirika amene amatumikira Mulungu.—Werengani Salimo 103:20, 21; Danieli 7:9, 10.
2. Kodi angelo amathandiza anthu?
Angelo anathandiza Loti yemwe anali munthu wolungama. Loti ankakhala mumzinda wina umene Mulungu anafuna kuuwononga chifukwa choti anthu a mumzindawo ankachita zoipa. Angelo awiri anachenjeza Loti ndi banja lake kuti atuluke mumzindawo. Anthu ena sanamvere chenjezolo chifukwa ankazitenga ngati zamasewera. Koma Loti ndi ana ake aakazi anapulumuka chifukwa anamvera chenjezo limene Mulungu anawapatsa kudzera mwa angelowo.—Werengani Genesis 19:1, 13-17, 26.
Baibulo limasonyeza kuti masiku anonso angelo akuthandiza anthu. Iwo akuchita zimenezi mwa kutsogolera anthu amene akugwira mokhulupirika ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Uthenga wabwino umene anthuwa amalalikira ukuphatikizapo kuchenjeza anthu. Ngati mmene zinalili ndi chenjezo limene Loti anauzidwa, zimene anthu akuchenjezedwazi zidzachitikadi. Chenjezo limeneli ndi lochokera kwa Mulungu ndipo akugwiritsa ntchito angelo ake.—Werengani Chivumbulutso 1:1; 14:6, 7.
Mulungu akhoza kugwiritsa ntchito angelo kutithandiza tikakumana ndi mayesero. Iye anagwiritsanso ntchito mngelo kuti alimbikitse Yesu.—Werengani Luka 22:41-43.
Posachedwapa Mulungu agwiritsa ntchito angelo kuwononga anthu oipa amene amayambitsa mavuto padzikoli. Zimenezi zidzabweretsa mpumulo kwa anthu olungama.—Werengani 2 Atesalonika 1:6-8.
3. Kodi zochita za ziwanda zimakhudza bwanji anthu?
Mofanana ndi mmene zilili padziko lapansi kuti anthu ambiri samvera Mulungu, kumwambanso angelo ena anapandukira Mulungu. (2 Petulo 2:4) Angelo osamverawa amatchedwa ziwanda ndipo mtsogoleri wawo ndi Satana Mdyerekezi. Satana ndi ziwanda zake amasocheretsa anthu.—Werengani Chivumbulutso 12:9.
Satana amagwiritsa ntchito anthu achinyengo ochita malonda, maboma komanso zipembedzo zonyenga kuti achititse anthu kuti asamalambire Mulungu. Choncho Satana ndi amene amachititsa kupanda chilungamo, chiwawa komanso mavuto amene anthu akukumana nawo.—Werengani 1 Yohane 5:19.
4. Kodi ziwanda zimasocheretsa bwanji anthu?
Satana amanyenga anthu ambiri ndi chiphunzitso chakuti anthu akufa amakakhala mizimu imene ingalankhule ndi anthu. Komatu Baibulo limaphunzitsa kuti akufa sangachite chilichonse. (Mlaliki 9:5) Koma ziwanda zimanyenga anthu mwa kulankhula mawu ofanana ndi a anthu amene anamwalira n’cholinga chakuti anthu aziganiza kuti akufawo ndi amene akulankhula. (Yesaya 8:19) Ziwanda zimanyenganso anthu kudzera m’zinthu monga asing’anga, olosera, kuwombeza komanso kukhulupirira nyenyezi. Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti tizipewa zinthu zimenezi. Choncho tiyenera kutaya chilichonse chokhudzana ndi ziwanda komanso matsenga.—Werengani Deuteronomo 18:10, 11; Machitidwe 19:19.
Ngati timakonda Yehova, palibe chifukwa choopera ziwanda. Tikamaphunzira Mawu a Mulungu komanso kutsatira zimene tikuphunzirazo, tingathe kutsutsa zofuna za Mdyerekezi ndi kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa ziwanda komanso angelo ake okhulupirika angatilimbikitse tikakumana ndi mavuto.—Werengani Salimo 34:7; Yakobo 4:7, 8.
Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 10 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.