Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ana Ayenera Kuphunzitsidwa Chiyani?

Kodi Ana Ayenera Kuphunzitsidwa Chiyani?

Kodi Ana Ayenera Kuphunzitsidwa Chiyani?

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.”​—2 TIMOTEYO 3:16.

ANA ayenera kuphunzitsidwa mfundo zoona zokhudza Mulungu. Kodi mfundo zimenezi zingapezeke kuti? Zingapezeke m’Baibulo, buku limene limalemekezedwa ndi zipembedzo zambiri padziko lonse.

Baibulo lili ngati kalata yochokera kwa Mulungu. M’kalatayi, Mulungu wafotokozamo makhalidwe ake ndiponso walembamo malangizo okhudza makhalidwe oti ana ake onse, aang’ono ndi aakulu omwe, azitsatira. Taonani zina mwa mfundo zimene Baibulo limaphunzitsa. Mfundozi ndi zothandizanso ngakhale kwa ana.

Kodi Mulungu amafuna kuti tidziwe mfundo zotani zokhudza iyeyo?

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”​—Salimo 83:18.

Zimene tikuphunzirapo: Mulungu si mphamvu chabe, koma ndi Munthu weniweni wauzimu ndipo ali ndi dzina.

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Yehova amasanthula mitima yonse ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse. Ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze.”​—1 Mbiri 28:9.

Zimene tikuphunzirapo: Yehova Mulungu amadera nkhawa anthu onse, kuphatikizapo ana aang’ono. (Salimo 10:14; 146:9) Yehova amafuna kuti anthufe tiphunzire za iye.

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Anthu inu musazunze . . . mwana wamasiye aliyense. Mukamuzunza ngakhale pang’ono, iye n’kundilirira, ndidzamva ndithu kulira kwake.”​—Ekisodo 22:22-24.

Zimene tikuphunzirapo: Yehova amamva mapemphero a anthu kuphatikizapo a ana aang’ono. Tingathe kulankhula ndi Mulungu nthawi zonse ndi kumuuza zakukhosi kwathu komanso mmene tikumvera.

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Mobwerezabwereza, anali kumuyesa Mulungu, ndipo anali kumvetsa chisoni Woyera wa Isiraeli.”​—Salimo 78:41.

Zimene tikuphunzirapo: Zolankhula ndiponso zochita zathu zingasangalatse Yehova kapena kumukhumudwitsa. Choncho ndibwino kuti tiziganiza kaye tisanalankhule kapena kuchita zinthu.

Kodi tiyenera kuwaona bwanji anthu omwe ndi osiyana ndi ifeyo?

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Zimene tikuphunzirapo: Ngati Mulungu amalandira anthu amtundu uliwonse, sitiyenera kuchitira anthu ena zinthu zoipa chifukwa chakuti khungu lawo kapena nkhope yawo ndi yosiyana ndi yathu.

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.”​—1 Petulo 3:15.

Zimene tikuphunzirapo: Tikamakambirana zachipembedzo, tiyenera kufotokoza maganizo athu molimba mtima koma osati mwaukali. Komanso tiyenera kulemekeza anthu amene amakhulupirira zosiyana ndi zimene ifeyo timakhulupirira.

Kodi tizichita bwanji zinthu ndi anthu a m’banja lathu?

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Ananu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye.”​—Akolose 3:20.

Zimene tikuphunzirapo: Ana omvera amasonyeza kuti amakonda makolo awo komanso amasonyeza kuti akufuna kusangalatsa Mulungu.

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”​—Akolose 3:13.

Zimene tikuphunzirapo: Anthu ena, kuphatikizapo a m’banja lathu, nthawi zina angatikhumudwitse. Koma ngati tikufuna kuti Mulungu azitikhululukira zimene timamulakwira, ifenso tiyenera kumakhululukira omwe atilakwira.​—Mateyu 6:14, 15.

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okoma mtima komanso kupewa bodza?

Zimene Baibulo limaphunzitsa: [Mutaye] chinyengo, [ndipo] aliyense wa inu alankhule zoona kwa mnzake.”​—Aefeso 4:25.

Zimene tikuphunzirapo: Tikamalankhula zoona timatsanzira Mulungu ndipo timasangalatsa mtima wake. Koma tikakhala ndi chizolowezi chonena bodza, timafanana ndi mdani wa Mulungu, Mdyerekezi, yemwe ndi “tate wake wa bodza.”​—Yohane 8:44; Tito 1:2.

Zimene Baibulo limaphunzitsa: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”​—Mateyu 7:12.

Zimene tikuphunzirapo: Tiyenera kumaganizira mmene anthu a m’banja lathu akumvera, zimene amaganiza komanso zosowa zawo ndipo tiyenera kuchitanso chimodzimodzi ndi anthu a m’dera lathu. Nthawi zambiri ‘tikamamvera ena chisoni,’ nawonso amatichitira zinthu mokoma mtima.​—1 Petulo 3:8; Luka 6:38.

Monga taonera, zimene Baibulo limaphunzitsa zingathandize kuti ana akadzakula adzakhale anthu oyamikira, aulemu komanso achifundo. Komano kodi ndani ayenera kuphunzitsa ana zinthu zimenezi?