Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsiku Losangalatsa Limene Ankaliyembekezera

Tsiku Losangalatsa Limene Ankaliyembekezera

Mwambo wa Omaliza Sukulu ya Giliyadi​Gulu la Nambala 130

Tsiku Losangalatsa Limene Ankaliyembekezera

N’ZOSAKAYIKITSA kuti anthu ankayembekezera kwambiri tsiku la mwambo wa omaliza maphunziro a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo a kalasi ya nambala 130. Mwambo umenewu unachitika Loweruka pa March 12, 2011 ndipo panafika anthu oposa 8,500. Ena mwa anthu amenewa anali ophunzira a m’kalasi limeneli limodzi ndi abale komanso mabwenzi awo. Anthu anali osangalala kwambiri chifukwa cha tsiku lapaderali komanso chifukwa cha zimene amishonale ophunzitsidwa bwino amenewa akachite akatumizidwa m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse kukaphunzitsa anthu choonadi cha m’Baibulo.

‘Odala Ndi Anthu Onse Amene Amayembekezera’ Yehova

Mawu olimbikitsa amenewa, ochokera palemba la Yesaya 30:18, anali mutu wa nkhani imene inakambidwa ndi M’bale Geoffrey Jackson, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Iye ndi amenenso anali tcheyamani wa mwambowu. Ndi mawu olimbikitsa komanso anthabwala, iye anayamikira ophunzirawo chifukwa chopirira mpaka kumaliza maphunziro awo a Giliyadi ndipo anawatsimikizira kuti zonse ziyenda bwino pa tsikuli. Kodi ophunzirawo anayenera kuyembekezera zotani? M’baleyu anatchula zinthu zitatu zimene angayembekezere zochokera pa Yesaya 30:18-21.

Choyamba M’bale Jackson anati: “Yembekezerani kuti Yehova azimva mapemphero anu.” Iye anatchula mawu olimbikitsa opezeka mu vesi 19, akuti: “[Mulungu] adzakukomera mtima akadzamva kulira kwako.” M’bale Jackson ananena kuti mawu akuti “adzakukomera mtima” akusonyeza kuti akulankhula ndi munthu mmodzi, zomwe zikutanthauza kuti Yehova amamvetsera mapemphero athu aliyense payekhapayekha. Iye anati: “Monga Atate, Yehova samatifunsa kuti, ‘Bwanji osangolimba mtima ngati mmene akuchitira mnzakoyo?’ M’malomwake, iye amamvetsera mwatcheru aliyense akamapemphera ndipo amamuyankha.”

Kachiwiri, wokamba nkhaniyo ananena kuti tiyenera kuyembekezera kuti tingakumane ndi mavuto nthawi zina. Iye anati: “Yehova satilonjeza kuti moyo wathu udzakhala wopanda mavuto koma iye amatilonjeza kuti tikakumana ndi mavutowo adzatithandiza.” Malinga ndi vesi 20, Mulungu analosera kuti dziko la Isiraeli likadzazunguliridwa ndi asilikali, masautso komanso kuponderezedwa zidzakhala zozolowereka ngati chakudya ndi madzi. Komabe, nthawi zonse Yehova adzakhala wokonzeka kupulumutsa anthu akewo. Nawonso ophunzira a Sukulu ya Giliyadiwa adzakumana ndi mavuto komanso zothetsa nzeru ngakhale kuti mavuto amenewa sangakhale amene ankayembekezera. M’bale Jackson anawonjezera kuti: “Koma muyenera kuyembekezera kuti Yehova adzakhala wokonzeka kukuthandizani kulimbana ndi vuto lililonse.”

Chachitatu, M’bale Jackson anakumbutsa ophunzirawo zimene zili mu vesi 20 ndi 21. Iye anawauza kuti “ayenera kuyembekezera kuuzidwa njira yoyenera kutsatira, choncho afunika kuifufuza.” M’bale Jackson ananenanso kuti, masiku ano Mkhristu aliyense amafunika kumvetsera mosamala pamene Yehova akulankhula kudzera m’Baibulo komanso m’mabuku ophunzitsa Baibulo. M’baleyu analimbikitsa ophunzirawa kuti azichita khama kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku chifukwa zimenezi n’zofunika kwambiri kuti adzapeze moyo wosatha.

“Mantha a Yehova Akugwireni”

Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira anafotokoza tanthauzo la mawu a m’Baibulo akuti, “mantha a Yehova.” (2 Mbiri 19:7) Mawu amenewa sakunena za mantha amene amabwera chifukwa cha kuopsezedwa koma amanena za mtima wofunitsitsa kuchita zolondola chifukwa cha ulemu wochokera pansi pa mtima umene umamuchititsa munthu kunjenjemera ndi mantha. M’bale Morris analangiza ophunzirawo kuti: “Mukhale ndi mantha amenewa mukamapita ku ntchito yanu yaumishonale.” Kodi amishonalewa angasonyeze bwanji ulemu woterewu kwa Yehova? M’baleyu anatchula njira ziwiri.

Choyamba, M’bale Morris analimbikitsa ophunzirawo kutsatira malangizo opezeka pa Yakobo 1:19, akuti: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.” Iye ananena kuti ophunzirawa aphunzira zinthu zambiri pa miyezi isanu ya maphunziro awo koma ayenera kusamala kuti asakayambe kudzitama mu utumiki wawo chifukwa cha zimene aphunzirazo. Iye anawauza kuti: “Muzikamvetsera kaye. Muzikamvetsera zonena za akulu a mumpingo mwanu komanso za abale amene akutsogolera m’dziko limene mukuchita utumiki wanu. Muzikamvetsera zimene akunena zokhudza dzikolo komanso chikhalidwe chake. Musamakachite manyazi kunena kuti, ‘Sindikudziwa.’ Ngati mwapinduladi ndi sukuluyi, ndiye kuti zimene muzikaphunzira zizikakuchititsani kuzindikira kuti zimene mukudziwa ndi zochepa.”

Kenako, M’bale Morris anawerenga lemba la Miyambo 27:21 limene limati: “Siliva amamuyengera m’mbiya yoyengera ndipo golide amamuyengera m’ng’anjo, momwemonso chitamando choperekedwa kwa munthu chimasonyeza mmene iye alili.” Iye anafotokoza kuti monga mmene golide ndi siliva amafunikira kuyengedwa, nafenso tingayengedwe ndi zimene anthu amanena potitamanda. Kodi zimenezi zingachitike bwanji? Nthawi zina anthu akalankhula mawu otitamanda, amenewo amakhala mayesero athu. Zikhoza kutiyambitsa kunyada n’kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova, kapena zingatichititse kuzindikira kuti Yehova akutithandiza ndipo tingayesetse kutsatira mfundo zake nthawi zonse. Choncho M’bale Morris analimbikitsa ophunzirawo kuti nthawi zonse azikhala ndi maganizo oyenera munthu akanena zinthu zowatamanda. Aziona kuti umenewo ndi mwayi woti asonyeze kuti ali ndi “mantha a Yehova” oyenera.

“Musakaiwale Zomwe Mwapitira”

M’bale Guy Pierce, yemwe ali m’Bungwe Lolamulira, ndi amene anakamba nkhani yaikulu pa mwambowu. Iye anakamba nkhani ya mutu umene uli pamwambawo ndipo anafotokoza kuti mawu akuti “m’mishonale” amatanthauza “munthu amene watumidwa kudziko lina kuti akagwire ntchito inayake.” Iye ananena kuti, choncho n’zosadabwitsa kuti mabungwe ambiri amatumiza amishonale kuti apite m’mayiko ena kukagwira ntchito zosiyanasiyana. Ambiri mwa amishonale amenewa ntchito yawo yaikulu ndi kuchiritsa anthu ndiponso kufufuza njira zothetsera mavuto andale. Iye anati: “Koma inu ndinu osiyana ndi amishonale amenewa.” Kodi ndi osiyana bwanji?

Ophunzirawa anaphunzira m’Baibulo nkhani zambiri zokhudza kuchiritsa. Yesu ataukitsa kamtsikana, makolo amtsikanayo “anasangalala kwambiri.” (Maliko 5:42) Komanso Yesu atachiritsa mozizwitsa anthu akhungu, anthuwo anasangalala kwambiri. Zozizwitsa zimenezi zinachitika pofuna kutisonyeza zimene Khristu adzachite m’dziko latsopano limene likubweralo. Pa nthawi imeneyo, “khamu lalikulu la anthu” olungama amene adzapulumuke mapeto a dzikoli adzachiritsidwa ku matenda awo onse. (Chivumbulutso 7:9, 14) Nawonso okondedwa awo amene adzaukitsidwe adzakhala atachiritsidwa ku matenda onse. Tangoganizani mmene anthu adzasangalalire.

Komabe monga mmene M’bale Pierce anafotokozera, padzachitikanso kuchiritsa kwina komwe ndi kofunika kwambiri kuposa kuchiritsidwa mwakuthupi. Anthu amene Yesu anawachiritsa patapita nthawi anadwalanso. Komanso anthu amene anawaukitsa anafanso patapita nthawi. Kuchiritsa anthu mwauzimu kumene Yesu anachita ndi kumene kunali kofunika kwambiri. Nawonso amishonale amatumidwa kuti akagwire ntchito yochiritsa anthu mwauzimu. Iwo amathandiza anthu kuti ayanjanenso ndi Atate wathu wakumwamba n’cholinga chakuti akhale ndi moyo mwauzimu. Anthu okhawo amene akuchiritsidwa mwauzimu ndi amene adzapeze moyo wosatha. M’bale Pierce ananena kuti: “Kuchiritsa mwauzimuku n’kumene kumachititsa anthu kutamanda Mulungu komanso n’kumene kumachititsa kuti zinthu zizikuyenderani bwino mu utumiki wanu.”

Nkhani Zina Zapamwambowu

“Kodi Lero Zinthu Zitiyendera Bwino?” M’bale Robert Rains, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya ku United States, anakamba nkhani ya mutu umenewu. Iye analimbikitsa ophunzirawo kuti azikachita zinthu zimene zingathandize kuti tsiku lililonse liziwayendera bwino pa ntchito yawo yaumishonale. Anawauza kuti, kuti zimenezi zitheke azikagwiritsa ntchito bwino nthawi yawo, azikadalira Mawu a Mulungu pakakhala zinthu zina zimene zikuwadetsa nkhawa komanso azikapemphera kwa Yehova posonyeza kumudalira.

“Kodi Mukalola Kuti Lamulo Lakale Likhale Latsopano?” M’bale Mark Noumair, yemwe ndi mlangizi wa Sukulu ya Giliyadi, anafunsa funso limeneli m’nkhani yake. Iye anafotokoza lemba la 1 Yohane 2:7, 8 pamene mtumwi Yohane anatchula za “lamulo lakale” lomwe linalinso “lamulo latsopano.” Malamulo awiri onsewa akunena za lamulo limodzi, loti otsatira a Khristu ayenera kukondana komanso ayenera kusonyeza mtima wololera kuvutikira ena. (Yohane 13:34, 35) Yohane ananena kuti lamulo limeneli ndi lakale chifukwa linali loti Khristu analipereka kwa otsatira ake zaka zambiri m’mbuyomo. Komabe iye ananenanso kuti ndi latsopano chifukwa Akhristu pa nthawiyo ankakumana ndi mavuto oti sanakumanepo nawo ndipo anafunika kusonyezana chikondi kwambiri m’njira zinanso zatsopano. Amishonale nawonso amakumana ndi zinthu zoti sanakumanepo nazo ndipo afunika kuphunzira kusonyezana chikondi m’njira zina zatsopano. Kodi chinsinsi choti athe kuchita zimenezi chagona pati?

M’bale Noumair analangiza ophunzirawo kuti: “Musamachite zinthu zimene mumadana nazo.” Iye anachenjeza kuti, tikaona munthu akuchita khalidwe limene timadana nalo, koma ifeyo n’kumatsanzira khalidwe limenelo, ndiye kuti tikuchita zimene timadana nazo. Kuchita zimenezo kungatibweretsere mavuto. Koma ngati pa zinthu zoterezi timapeza njira zatsopano zosonyezera chikondi, timasonyeza “kuwala kwenikweni” ndipo timathamangitsa mdima wauzimu.

“Senzani Katundu.” Mlangizi wina wa Sukulu ya Giliyadi dzina lake Michael Burnett anakamba nkhani ya mutu umenewu. Iye anafotokoza za anthu a m’mayiko a ku Africa omwe amatha kusenza katundu wolemera. Kuti asamve kuwawa pamutu pawo akasenza katundu, anthu amenewa amagwiritsa ntchito nkhata ndipo nkhatayo imathandizanso kuti azitha kuyenda bwinobwino atasenza katunduyo. Amishonale a Sukulu ya Giliyadiwo akapita m’mayiko amene atumizidwa, akafunika kusenza katundu wolemera yemwe ndi maudindo osiyanasiyana. Koma iwo apatsidwa chinthu chomwe tingachiyerekezere ndi nkhata ndipo chinthu chimenechi ndi mfundo zochokera m’Baibulo zimene aphunzira. Akamakagwiritsa ntchito zimene aphunzirazo, akatha kukwanitsa maudindo awo bwinobwino.

Zokumana Nazo Komanso Kucheza Ndi Ophunzira

Ngati mbali ya maphunziro awo, ophunzira a Sukulu ya Giliyadi amapita kukalalikira limodzi ndi mipingo ya Mboni za Yehova yapafupi. M’bale William Samuelson, yemwe ndi woyang’anira wa Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu, anafunsa ophunzira ena kuti afotokoze zimene anakumana nazo ndipo mutu wa zokambirana zawo unali wakuti: “Dzanja Lako Lisapume.” (Mlaliki 11:6) Ophunzirawo anachita zitsanzo zosonyeza khama limene anasonyeza mu utumiki. Iwo ankafufuza njira zolalikirira uthenga wabwino pamabwalo a ndege, m’malesitilanti komanso m’malo ogulitsira mafuta. Iwo ankalalikiranso kunyumba ndi nyumba, kudzera m’makalata komanso kwa anthu amene angokumana nawo pochita zinthu zosiyanasiyana. Tingati iwo sanalole kuti dzanja lawo lipume ndipo zotsatira zake zinali zabwino kwambiri.

Kenako M’bale Kenneth Stovall, yemwe amagwira ntchito zina zokhudzana ndi Sukulu ya Giliyadi, anakamba nkhani ya mutu wakuti: “Muyeseni Yehova Ndipo Mudzapeza Madalitso.” (Malaki 3:10) Iye anafunsa mafunso abale atatu amene achita umishonale kwa nthawi yaitali. Abale amenewa ndi Barry Hill yemwe anatumikirapo ku Ecuador ndi ku Dominican Republic, Eddie Mobley yemwe anatumikirapo ku Côte d’Ivoire, komanso Tab Honsberger yemwe anatumikirapo ku Senegal, ku Benin ndi ku Haiti. Zimene abale amenewa anafotokoza zinali zogwirizana kwambiri ndi mutu wa nkhani umenewu. Mwachitsanzo, M’bale Hill anafotokoza mmene iye ndi mkazi wake anavutikira kuti azolowere nyengo ya ku Ecuador yomwe nthawi zina imakhala yotentha ndiponso yafumbi koma nthawi zina imakhala yotentha komanso yamatope. Iye anafotokozanso kuti kwa zaka ziwiri ndi hafu ankagwiritsa ntchito baketi posamba. Koma iwo sanaganize zobwerera kwawo chifukwa ankaona kuti utumiki wawo ndi madalitso ochokera kwa Yehova. M’bale Hill anati: “Tinazolowera moyo umenewu moti sitinkadandaula.”

Kumapeto kwa mwambowu mmodzi mwa ophunzirawo anawerenga kalata yokhudza mtima kwambiri imene ophunzirawa analemba. Kalatayi inali yoyamikira zimene anaphunzira m’sukulu imeneyi. Kalatayo inali ndi mawu akuti: “Sukuluyi yalimbitsa chikhulupiriro chathu. Komabe tikudziwa kuti padakali zambiri zoti tiphunzire.” Ophunzira onse analandira zikalata zosonyeza kuti amaliza maphunziro awo ndipo anatumizidwa m’mayiko osiyanasiyana. Pomaliza mwambowu, M’bale Jackson anatsimikizira ophunzirawo kuti asakayikire zoti Yehova akawathandiza makamaka pa mavuto amene angakakumane nawo. Anthu onse amene anapezeka pa mwambowu anali osangalala kwambiri ndipo ankayembekezera kuti anthu amene amaliza maphunziro awowa akachita zambiri ku mayiko kumene akupita. Sitikukayikira kuti Yehova achita zinthu zabwino zambiri pogwiritsa ntchito amishonale atsopanowa.

[Tchati/​Mapu patsamba 31]

ZA OPHUNZIRAWO

Mayiko amene ophunzira achokera: 9

Avereji ya zaka zobadwa: 34

Avereji ya zaka zimene akhala Mboni kuchokera pamene anabatizidwa: 18.6

Avereji ya zaka zimene akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse: 13.1

[Mapu]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ophunzirawa anatumizidwa kumayiko amene ali pansipa

KUMENE AMISHONALE ANATUMIZIDWA

ARGENTINA

ARMENIA

BURKINA FASO

BURUNDI

CONGO (KINSHASA)

CZECH REPUBLIC

HAITI

HONG KONG

INDONESIA

KENYA

LITHUANIA

MALAYSIA

MOZAMBIQUE

NEPAL

PAPUA NEW GUINEA

ROMANIA

SENEGAL

TANZANIA

UGANDA

ZIMBABWE

[Chithunzi patsamba 31]

Gulu la Nambala 130 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Giliyadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pamndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mumzera uliwonse mayina tawandandalika kuyambira dzina la munthu amene ali kumanzere kupita kumanja.

(1) Molina, Z.; Bassolino, S.; Alatsis, C.; Arroyo, A.; Niño, L.; Merkling, S.; Clark, M.

(2) Little, C.; Tibaudo, S.; Jakobsson, S.; Moreno, J.; Rodriguez, A.; Lee, K.; Cárdenas, H.; Aguilar, L.

(3) Clairbush, A.; Polley, A.; Caldwell, S.; Adame, J.; Hildebrandt, S.; Shoemaker, I.; Grohman, N.; Galvez, G.

(4) Clark, J.; Bassolino, A.; Packham, K.; Adame, J.; Knaus, M.; Niño, M.; Moreno, R.; Galvez, J.

(5) Rodriguez, D.; Geynes, M.; Molina, J.; Aguilar, A.; Alatsis, I.; Manno, A.; Grohman, R.; Packham, J.

(6) Geynes, S.; Cárdenas, M.; Arroyo, C.; Manno, C.; Merkling, J.; Lee, H.; Clairbush, X.; Jakobsson, P.

(7) Little, J.; Hildebrandt, B.; Shoemaker, M.; Knaus, K.; Caldwell, J.; Tibaudo, F.; Polley, C.