Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa . . .

Kodi Mulungu Ali Ndi Malo Enieni Amene Amakhala?

Kodi Mulungu Ali Ndi Malo Enieni Amene Amakhala?

Zipembedzo zambiri zimanena kuti Mulungu amakhala ponseponse, kutanthauza kuti Mulungu amapezeka pamalo ambirimbiri pa nthawi imodzi. Mwachitsanzo, buku lina limanena kuti Mulungu “amapezeka pamalo alionse komanso mu chinthu chilichonse.” (New Catholic Encyclopedia) Mofanana ndi zimenezi, John Wesley, yemwe anayambitsa tchalitchi cha Methodist, analemba ulaliki wa mutu wakuti “Mulungu Amakhala Ponseponse.” Mu ulalikiwu iye ananena kuti, “palibe malo alionse kapena chinthu, mmene simupezeka Mulungu.”

Koma kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhaniyi? Kodi n’zoona kuti Mulungu amakhala paliponse, kutanthauza kumwamba, padziko lapansi komanso mwa munthu aliyense?

Baibulo limanena kuti Mulungu ali ndi malo ake enieni amene amakhala, omwe ndi kumwamba. M’Baibulo muli pemphero la Mfumu Solomo yomwe inapempha Mulungu kuti: “Inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika.” (1 Mafumu 8:43) Pamene Yesu Khristu ankaphunzitsa ophunzira ake kupemphera, anawauza kuti mapemphero awo azipita kwa “Atate wathu wakumwamba.” (Mateyu 6:9) Baibulo limanena kuti Khristu ataukitsidwa, analowa ‘kumwamba kwenikweniko kuti aonekere pamaso pa Mulungu.’​—Aheberi 9:24.

Mavesi amenewa akuchita kusonyezeratu kuti Yehova Mulungu amakhala kumwamba kokha basi, osati paliponse. N’zoona kuti mawu akuti “kumwamba” amene ali m’mavesi amenewa sakutanthauza mlengalenga kapena kumwamba kumene timaonaku. Mlengi wa zinthu zonse sangakwane kumwamba kumene timaonaku. (1 Mafumu 8:27) Baibulo limatiuza kuti “Mulungu ndiye Mzimu.” (Yohane 4:24) Iye amakhala kumwamba kosaoneka, komwe ndi kosiyana ndi kumwamba kumene timaonaku.​—1 Akorinto 15:44.

Komano n’chifukwa chiyani mavesi ena a m’Baibulo amasonyeza ngati Mulungu amapezeka paliponse? Mwachitsanzo, pa Salimo 139:7-10, ponena za Mulungu, Davide anati: “Ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu, ndipo ndingapite kuti kuthawa nkhope yanu? Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko. Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda, taonani! inunso mudzakhala komweko. Ngati ndingakwere pamapiko a m’bandakucha, kuti ndikakhale m’nyanja ya kutali kwambiri, kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera.” Kodi mavesi amenewa akutanthauza kuti Mulungu amakhala paliponse ndipo amapezeka m’malo onse amene atchulidwawa?

Taonani kuti Davide anayamba ndi kufunsa kuti: “Ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu?” * Kudzera mwa mzimu wake woyera, Mulungu angathe kuona chilichonse komanso kusonyeza mphamvu zake kulikonse ndipo kuti achite zimenezi sikuti amachita kufunika kupita komweko kapena kukhala kumalo amenewo. Mwachitsanzo, zaka zaposachedwapa asayansi akwanitsa kuyeza dothi lapapulaneti yotchedwa Mars yomwe ili kutali kwambiri ndi dziko lapansili. Kodi iwo atha bwanji kuchita zimenezi? Sikuti iwo amapita ku Mars, koma amangotumiza zipangizo zofufuzira zimene zimajambula zithunzi n’kuzitumiza padziko lapansi pano. Pogwiritsa ntchito zithunzi zimenezi, iwo amatha kudziwa mmene zinthu zilili papulanetilo.

N’chimodzimodzinso ndi Yehova Mulungu. Iye safunika kukhala pamalo alionse kuti adziwe zimene zikuchitika m’chilengedwechi. Mawu a Mulungu amati: “Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.” (Aheberi 4:13) Choncho, mphamvu ya Yehova yogwira ntchito, kapena kuti mzimu woyera, imafika paliponse ndipo imachititsa kuti iye azitha kuona chilichonse komanso azitha kukwaniritsa cholinga chake ali kumwamba, omwe ndi ‘malo ake oyera okhalako.’​—Deuteronomo 26:15.

^ ndime 8 Mawu achiheberi amene palembali anawamasulira kuti “mzimu” akutanthauza mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito. Mphamvu imeneyi ndi imene Mulungu amagwiritsa ntchito pokwaniritsa cholinga chake.