Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungaphunzitsire Ana Zinthu Zokhudza Mulungu—Kodi Njira Zabwino Ndi Ziti?

Mmene Mungaphunzitsire Ana Zinthu Zokhudza Mulungu—Kodi Njira Zabwino Ndi Ziti?

 Mmene Mungaphunzitsire Ana Zinthu Zokhudza Mulungu​—Kodi Njira Zabwino Ndi Ziti?

“Mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako, ndi kuwakhomereza mwa ana ako. Uzilankhula nawo za mawuwo ukakhala pansi m’nyumba mwako, poyenda pamsewu, pogona ndi podzuka.”​—DEUTERONOMO 6:6, 7.

NTHAWI zina makolo amaona kuti kuphunzitsa ana awo ndi udindo waukulu kwambiri woti sangaukwanitse. Komanso akati afufuze malangizo amene angawathandize pa nkhaniyi, amapeza mfundo zambirimbiri ndipo zimenezi zimangowawonjezera nkhawa. Achibale ndiponso anzawo nthawi zambiri amawauza maganizo awo pa nkhani ya mmene angaphunzitsire ana. Ndiye palinso mabuku, nkhani za m’magazini komanso nkhani zopezeka pa Intaneti zomwe zili ndi malangizo ambirimbiri opita kwa makolo ndipo nthawi zina malangizo amenewa amakhala otsutsana.

Koma m’Baibulo muli malangizo odalirika opita kwa makolo onena za zimene angaphunzitse ana awo komanso mmene angawaphunzitsire. Lemba la m’Baibulo lili pamwambali likusonyeza kuti tsiku lililonse makolo ayenera kupeza njira imene angalankhulire ndi ana awo zinthu zokhudza Mulungu. Taonani njira zinayi izi zochokera m’Baibulo zimene zathandiza makolo ambiri kuphunzitsa ana awo zinthu zokhudza Mulungu.

1. Aphunzitseni pogwiritsa ntchito zinthu za m’chilengedwe. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Zingakhale zothandiza kwambiri ngati makolo angagwiritse ntchito zinthu zimene Mulungu analenga, pothandiza ana awo kuona kuti Mulungu ndi weniweni ndipo kenako n’kuthandiza anawo kuzindikira makhalidwe a Mulungu amene zinthu zachilengedwe zimatiphunzitsa.

Yesu anagwiritsa ntchito njira imeneyi pamene ankaphunzitsa ophunzira ake. Mwachitsanzo iye anati: “Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga chakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” (Mateyu 6:26) Pamenepa Yesu ankafotokoza mfundo yakuti, Yehova ndi wachikondi komanso wachifundo. Koma sizokhazo. Iye anathandizanso ophunzira ake kuganizira mmene Mulungu amasonyezera makhalidwe amenewa kwa ana ake.

Solomo, yemwe anali mfumu yanzeru, anatchulapo kuti Mulungu anapatsa nyerere nzeru ndipo anagwiritsa ntchito zolengedwa zing’onozing’ono zimenezi pofuna kutsindika mfundo yofunika kwambiri. Iye analemba kuti: “Pita kwa nyerere waulesi iwe, ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru. Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri,  kapitawo, kapena wolamulira, imakonza chakudya chake m’chilimwe. Imasonkhanitsa zakudya zake pa nthawi yokolola.” (Miyambo 6:6-8) Imeneyitu ndi njira yabwino kwambiri yophunzitsira ana kufunika kokhala ndi zolinga zaphindu kenako n’kugwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu watipatsa kukwaniritsa zolingazo.

Makolo angatsanzire njira yophunzitsira imeneyi, imene Yesu ndi Solomo anagwiritsa ntchito, pochita zinthu zitatu izi: (1) Kufunsa ana awo zomera ndiponso nyama zimene zimawachititsa chidwi. (2) Kuphunzira zambiri za zomera ndiponso nyama zimenezo. (3) Kuganizira zimene akuphunzira zokhudza Mulungu, kuchokera ku zinthu zimenezo.

2. Tsanzirani mmene Yesu ankaonera anthu amene ankawaphunzitsa. Pa anthu onse amene anakhala padzikoli, Yesu ndi amene anali ndi zinthu zofunika kwambiri zoti auze anthu. Koma iye nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito mafunso. Iye ankafunitsitsa kudziwa zimene anthu akuganiza komanso mmene akumvera mumtima mwawo pa nkhani zosiyanasiyana. (Mateyu 17:24, 25; Maliko 8:27-29) Nawonso makolo ali ndi zinthu zambiri zofunika zoti aphunzitse ana awo. Koma kuti aziphunzitsa mogwira mtima, ayenera kutsanzira Yesu n’kumalimbikitsa ana awo kufotokoza maganizo awo momasuka.

Nanga kodi makolo angatani ngati ana awo akusonyeza kuti ayamba khalidwe loipa kapena ngati akuchedwa kugwira mfundo zofunika zimene akuwaphunzitsa? Taganizirani mmene Yesu ankachitira zinthu ndi atumwi ake. Iwo nthawi zina ankakangana kwambiri ndipo zinawatengera nthawi kuti aphunzire kufunika kokhala odzichepetsa. Koma Yesu anawalezera mtima ndipo mobwerezabwereza anawaphunzitsa kufunika kokhala odzichepetsa. (Maliko 9:33, 34; Luka 9:46-48; 22:24, 25) Makolo amene amatsanzira Yesu amalangiza ana awo moleza mtima ndipo nthawi zina amabwereza zimene akuwaphunzitsazo mpaka anawo atamvetsa bwino kufunika kwake. *

3. Aphunzitseni mwa kuwasonyeza chitsanzo. Makolo angachite bwino kutsatira malangizo amene mtumwi Paulo anapatsa Akhristu a ku Roma. Iye anawalembera kuti: “Kodi iwe wophunzitsa enawe, sudziphunzitsa wekha? Iwe amene umalalikira kuti ‘Usabe,’ umabanso kodi?”​—Aroma 2:21.

Malangizo amenewa ndi ofunika zedi chifukwa ana amatsatira kwambiri zimene makolo amachita kusiyana ndi zimene amanena. Ndipotu makolo akamachita zimene amaphunzitsa ana awo, anawo amatsatiradi zimene makolowo amawaphunzitsa.

4. Yambani kuwaphunzitsa ali aang’ono. Timoteyo, yemwe ankayenda ndi mtumwi Paulo pa maulendo ake aumishonale, anali ndi mbiri yabwino kwambiri kudera lakwawo. (Machitidwe 16:1, 2) Chifukwa chimodzi chimene chinachititsa zimenezi n’chakuti, kuyambira ali “wakhanda” anaphunzitsidwa “malemba oyera.” Amayi ndiponso agogo a Timoteyo sankangomuwerengera Malemba, koma ankamuthandizanso kuganizira kwambiri za choonadi chopezeka m’Malembawo.​—2 Timoteyo 1:5; 3:14, 15.

Kumene Mungapeze Thandizo

A Mboni za Yehova amafalitsa mabuku ambiri amene anakonzedwa n’cholinga chakuti athandize makolo kuphunzitsa ana awo choonadi ponena za Mulungu. Ena mwa mabuku amenewa anawalemba ndi cholinga chakuti athandize ana. Ndiponso mabuku ena angathandize makolo ndi ana awo achinyamata kuti azitha kulankhulana momasuka. *

Koma kuti makolo athe kuphunzitsa ana awo zinthu zokhudza Mulungu, ayenera kudziwa mayankho a mafunso ena ovuta amene anawo angafunse. Mwachitsanzo, kodi makolonu mungayankhe bwanji mafunso awa: Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika? Kodi Mulungu analengeranji dziko lapansili? Kodi akufa ali kuti? A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani kupeza mayankho a mafunso amenewa ndi enanso ambiri n’cholinga chakuti inuyo ndi banja lanu mukhale pa ubwenzi ndi Mulungu.​—Yakobo 4:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mawu achiheberi amene pa Deuteronomo 6:7 anawamasulira kuti ‘kukhomereza,’ amatanthauza kunena mfundo mobwerezabwereza.

^ ndime 15 Pophunzitsa ana aang’ono, makolo angagwiritse ntchito buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso limene limafotokoza kwambiri zimene Yesu Khristu anaphunzitsa, kapena lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo limene limafotokoza mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo m’njira yosavuta. Pophunzitsa achinyamata, makolo angagwiritse ntchito mabuku akuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa​—Buku Loyamba ndi Lachiwiri.