Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amatipatsa Ufulu Wosankha Zochita

Yehova Amatipatsa Ufulu Wosankha Zochita

 Yandikirani Mulungu

Yehova Amatipatsa Ufulu Wosankha Zochita

Deuteronomo 30:11-20

MAYI wina wachikhristu yemwe ankaganiza kuti sangathenso kuchita zinthu zabwino chifukwa cha zimene zinamuchitikira ali mwana, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimaopa kuti mwina ndikhoza kulakwira Yehova.” Kodi nanunso mumaona choncho? Kodi n’zoona kuti sitingathe kuchita zinthu zabwino? Ayi, chifukwa Yehova Mulungu watipatsa ufulu wosankha zochita. Choncho tikhoza kusankha zimene tikufuna kuchita pamoyo wathu. Koma Yehova amafuna kuti tizisankha kuchita zoyenera ndipo Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, limatiuza mmene tingachitire zimenezi. Taganizirani mawu a Mose opezeka pa Deuteronomo chaputala 30.

Kodi n’zosatheka kudziwa zimene Mulungu amafuna kuti tizichita? Nanga kodi n’zovuta kuchita zimene Mulungu amafuna kuti tizichitazo? * Mose ananena kuti: “Lamulo ili ndikuuzani lerolino, silikulakani kulizindikira, kapena silikhala kutali.” (Vesi 11) Yehova safuna kuti tichite zimene sitingathe. Malamulo ake ndi oti tingakwanitse kuwatsatira. Komanso ndi odziwika bwino kwambiri. Sitifunikira kukwera “m’mwamba” kapena kupita ‘kutsidya la nyanja,’ kuti tidziwe zimene Mulungu amafuna kuti tizichita. (Vesi 12 ndi 13) Baibulo limatiuza momveka bwino zimene tiyenera kuchita pamoyo wathu.​—Mika 6:8.

Komabe, Yehova satikakamiza kuti tizimumvera. Mose ananena kuti: “Ndaika pamaso panu lerolino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa.” (Vesi 15) Tili ndi ufulu wosankha pakati pa moyo ndi imfa, zabwino kapena zoipa. Tingasankhe kulambira Mulungu kuti atidalitse kapena kusamvera malamulo ake n’kukumana ndi zotsatirapo zake. Choncho, ufulu wosankha ndi wathu.​—Vesi 16-18; Agalatiya 6:7, 8.

Kodi zimene tasankha kuchita zimam’khudza Yehova? Inde, zimam’khudza. Mouziridwa ndi Mulungu, Mose anena kuti: “Sankhani moyo.” (Vesi 19) Ndiyeno kodi tingatani kuti tisankhe moyo? Mose anafotokoza kuti chofunika ndi “kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira.” (Vesi 20) Ngati timakonda Yehova, tidzayesetsa kumumvera ndi kutsatira mokhulupirika malamulo ake, zivute zitani. Tikamachita zimenezi ndiye kuti tikusankha moyo ndipo tidzakhala osangalala panopo komanso tingadzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.​—2 Petulo 3:11-13; 1 Yohane 5:3.

Mawu amene Mose ananenawa ndi oona. Kaya mwakumana ndi zotani m’dziko loipali, sizikutanthauza kuti simungathe kuchita zinthu zabwino. Yehova wakupatsani mwayi wapadera wosankha nokha zochita. Mungasankhe kukonda Yehova, kumumvera ndiponso kuchita zinthu zosonyeza kuti ndinu wokhulupirika. Mukasankha kuchita zimenezi, Yehova adzakudalitsani kwambiri.

Mfundo yoti munthu aliyense angasankhe yekha kukonda ndiponso kutumikira Yehova inam’limbikitsa mayi amene tamutchula koyambirira uja. Iye anati: “Ndimakondadi Yehova. Koma nthawi zina ndimaiwala kuti chofunika kwambiri n’choti ndimakonda Yehova. Choncho ndingathe kukhala wokhulupirika.” Inunso mungathe kuchita zimenezi mothandizidwa ndi Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Onani nkhani yakuti “Yandikirani Mulungu​—Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizichita Chiyani?” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2009.