Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Bodza Lachiwiri: Anthu Oipa Amakapsa Kumoto

Bodza Lachiwiri: Anthu Oipa Amakapsa Kumoto

Kodi bodzali linayamba bwanji?

Buku lina limati: “Pa akatswiri onse achigiriki a maphunziro a nzeru zapamwamba, Plato ndi yemwe anakopa anthu ambiri.”​—Histoire des enfer (Mbiri ya Moto wa Helo), lolembedwa ndi Georges Minois, tsamba 50.

Buku linanso linati: “Kuyambira chapakati pa zaka za m’ma 100 AD, Akhristu amene anaphunzira nzeru za Agiriki anayamba kuganiza kuti n’kofunika kuti aziphunzitsa zimene iwo ankakhulupirira mogwirizana ndi nzeru za anthu amenewa . . . Ndipo iwo anasankha kuti azitsatira nzeru za Plato.”​—The New Encyclopædia Britannica (1988), Voliyumu 25, tsamba 890.

Buku lina lachikatolika limati: “Zimene tchalitchichi chimaphunzitsa zimatsimikizira kuti anthu amakapsa kumoto kwa muyaya. Munthu woipa akangofa, mzimu wake umapita kumoto, kumene ‘umakazunzika kwamuyaya.’ Pamenepa, chilango chachikulu chimakhala kusayanjananso ndi Mulungu.”​—Catechism of the Catholic Church, la mu 1994, tsamba 270.

Kodi Baibulo limati chiyani?

Limanena kuti: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, . . . pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”​—Mlaliki 9:5, 10.

Kodi lembali likusonyeza kuti chimachitika n’chiyani munthu akafa? Kodi amakapsa kumoto pomulanga chifukwa cha machimo amene anachita? Ayi, chifukwa lembali likuti: “Sadziwa kanthu.” N’chifukwa chake panthawi imene Yobu ankavutika kwambiri chifukwa cha matenda aakulu, anapempha Mulungu kuti: “Mukadandibisa kumanda.” (Yobu 14:13) Zimenezi zikanakhala zosamveka zikanakhala kuti kumanda kumene anthu amapita amakapsa ndi moto. Mfundo ndi yakuti anthu akufa sachita chilichonse.

Ndiponso Mulungu ndi wachikondi ndipo palibe mlandu umene munthu angapalamule umene ungamuchititse kuti azunzidwe mpaka kalekale. (1 Yohane 4:8) Koma ngati zili zabodza kuti anthu oipa amakapsa kumoto, nanga bwanji nkhani yakuti anthu abwino amapita kumwamba?

Yerekezani ndi mavesi awa: Salmo 146:3, 4; Machitidwe 2:25-27; Aroma 6:7, 23

ZOONA N’ZAKUTI:

Mulungu saotcha anthu