Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Uthenga Wabwino Ukupezeka M’zinenero 500

Uthenga Wabwino Ukupezeka M’zinenero 500

 Uthenga Wabwino Ukupezeka M’zinenero 500

PANTHAWI ya nkhondo yapachiweniweni ku Rwanda, kagulu kena ka anthu omasulira mabuku kanasiya katundu wawo, n’kuthawira kumalo osungirako anthu othawa nkhondo. Komabe, iwo anakwanitsa kutenga makompyuta awo am’manja. Iwo anatenga makompyutawo n’cholinga choti azikamasulira mabuku ofotokoza Baibulo m’chinenero cha Kinyarwanda.

Nayenso mayi wina wachitsikana wa kudera lakum’mwera chakum’mawa kwa Asia, ankatayipa pakompyuta mpaka pakati pa usiku. Iye ankachita zimenezi ngakhale kuti ankakhala wotopa, kunja kunkatentha kwambiri ndiponso magetsi ankathimathima, zomwe zinkasokoneza ntchito yake yomasulira. Cholinga chake chinali choti amalize kumasulira mabuku, tsiku losindikiza lisanafike.

Anthu amenewa ali m’gulu la anthu pafupifupi 2,300, omwe amagwira ntchito yomasulira mabuku mongodzipereka m’madera oposa 190 padziko lonse. Anthuwa ndi azaka zapakati pa 20 mpaka pafupifupi 90 ndipo amagwira ntchito mwakhama n’cholinga choti anthu alandire uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo, m’zinenero 500.​—Chivumbulutso 7:9.

Kumasulira Mabuku M’zinenero Zosiyanasiyana

M’zaka zaposachedwapa, ntchito ya Mboni za Yehova yomasulira mabuku yapita patsogolo kwambiri. Mwachitsanzo, mu 1985, Nsanja ya Olonda inkatuluka m’zinenero 23 panthawi imodzi. Zimenezi zinali zochititsa chidwi kwambiri panthawi imeneyo. Koma masiku ano, magazini a Nsanja ya Olonda akupezeka m’zinenero 176, ndipo magazini onsewa amatuluka panthawi yofanana n’cholinga choti anthu padziko lonse awerenge magaziniwa panthawi yofanana.

Ndiponso m’zinenero pafupifupi 50, Nsanja ya Olonda ndi magazini yokhayo imene imatuluka nthawi zonse. N’chifukwa chiyani zili choncho? Makampani olemba ndi kusindikiza mabuku amaona kuti kusindikiza mabuku m’zinenerozo n’kopanda phindu. Koma Mboni za Yehova padziko lonse zimapereka ndalama mwakufuna kwawo ndipo zimenezi zimathandiza kuti Mawu a Mulungu ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo azipezeka kwa anthu onse.​—2 Akorinto 8:14.

Anthu amasangalala kwambiri akamawerenga Baibulo m’chinenero chawo. Chaposachedwapa, mabuku ofotokoza Baibulo amasuliridwa m’Chimisikito, chinenero chomwe chimalankhulidwa ndi anthu pafupifupi 200,000 ku Nicaragua. Mwachitsanzo, mayi wina anaitanitsa Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo * la m’Chimisikito. Ndipo pomwe mayiyo ankalandira bukulo, panali m’busa wina yemwe anapempha kuti likhale lake ataona kuti bukulo n’lokongola. Mayiyo sanalole ngakhale kuti m’busayo anamuuza kuti asinthane  bukulo ndi thumba la nthanga za khofi lolemera makilogalamu 20.

Pa zaka 10 zapitazi, mabuku ofotokoza Baibulo amasuliridwa m’zinenero zoposa 12 za ku Mexico. Zina mwa zinenerozi ndi Chimaya, Chinawato ndiponso Chitsotsilu. Pa zaka zosakwana 10, mipingo ya Mboni za Yehova kuphatikizapo ya chinenero chamanja ku Mexico, yawonjezeka kuchoka pa 72 mpaka kupitirira pa 1,200. Mboni za Yehova zimadzala uthenga wa m’Baibulo m’mitima ya anthu koma Mulungu ndi amene amakulitsa mbewu za choonadi m’mitima ya anthuyo.​—1 Akorinto 3:5-7.

Baibulo Lamakono Lamasuliridwa M’zinenero 80

M’zaka zaposachedwapa, Mboni za Yehova zagwira ntchito mwakhama kuti zitulutse Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, lathunthu kapena mbali yake ina, m’zinenero 80. Zimenezi zathandiza kwambiri. Mwachitsanzo, ponena za Baibulo la Chitswana, munthu wina wa Mboni ku South Africa anati: “Baibuloli ndi labwino kwambiri chifukwa lindithandiza kuti ndizikonda kwambiri Mawu a Mulungu komanso ndi losavuta kuwerenga.” Ndipo munthu winanso wolankhula Chitsonga ku Mozambique analemba kuti: “Tinali ndi mabuku ambiri ofotokoza Baibulo, koma zimenezi zinali ngati kunja kwa mabingu ndi ziphaliwali koma kopanda mvula. Komabe, mvula inayamba kugwa pamene Baibulo la New World Translation linatuluka m’Chitsonga.”

Anthu amene amamasulira ndiponso kufalitsa uthenga wabwino wa m’Baibulo, akukwaniritsa mochititsa chidwi ulosi winawake wa m’Baibulo womwe Yesu Khristu ananena. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.”​—Mateyo 24:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

BAIBULO LA MABUKU NEW WORLD TRANSLATION ENA

Lathunthu kapena mbali yake

1950 1*

1970 7*

1990 13*

2000 36*

2010 80*

MABUKU ENA

1950 88*

1960 125*

1970 165*

1980 190*

1990 200*

2010 500*

*ZINENERO

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Anthu pafupifupi 2,300 ongodzipereka, akumasulira mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero 500

BENIN

SLOVENIA

ETHIOPIA

BRITAIN