Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Bodza Lachitatu: Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba

Bodza Lachitatu: Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba

Kodi bodzali linayamba bwanji?

Chakumayambiriro kwa m’ma 100 C.E., atumwi a Yesu atatha kufa, anthu ena amene ankatchedwa Abambo a Tchalitchi anayamba kutchuka. Pofotokoza zimene ankaphunzitsa, buku lina limanena kuti: “Mfundo imene ankakonda kuphunzitsa inali yakuti mizimu ya anthu akufa imayeretsedwa ndipo kenako imakalowa kumwamba kukasangalala.”​—New Catholic Encyclopedia (2003), Voliyumu 6, tsamba 687.

Kodi Baibulo limati chiyani?

Limanena kuti: “Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.”​Mateyo 5:5.

Ngakhale kuti Yesu analonjeza ophunzira ake kuti akupita kumwamba ‘kukawakonzera malo,’ iye sanasonyeze kuti anthu onse olungama amapita kumwamba. (Yohane 3:13; 14:2, 3) Ndiponso, kodi Yesu sanapemphere kuti chifuniro cha Mulungu chichitike “monga kumwamba, chomwechonso pansi pano”? (Mateyo 6:9, 10) Zoona zake n’zakuti pali malo awiri amene anthu olungama angayembekeze kudzakhala. Anthu ochepa adzapita kumwamba kukalamulira ndi Khristu, koma anthu ambiri adzakhala ndi moyo kosatha padziko lino lapansi.​—Chivumbulutso 5:10.

Patapita nthawi, tchalitchi choyambirira chinasiya udindo wake padziko lapansili. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Buku lina linati: “Tchalitchichi chinasiya kuyembekezera Ufumu wa Mulungu.” (The New Encyclopædia Britannica) Ndipo pofuna kuti tchalitchichi chikhale ndi mphamvu, chinayamba kulowerera ndale ponyalanyaza malangizo omveka bwino a Yesu akuti otsatira ake ‘sali mbali ya dzikoli.’ (Yohane 15:19; 17:14-16; 18:36) Ndipo mfumu ina yachiroma, dzina lake Kositantini, inalimbikitsa anthu a m’tchalitchichi kusiya zimene ankakhulupirira poyamba, monga nkhani yonena za mmene Mulungu alili.

Yerekezani ndi mavesi awa: Salmo 37:10, 11, 29; Yohane 17:3; 2 Timoteyo 2:11, 12

ZOONA N’ZAKUTI:

Anthu ambiri abwino adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi kosatha, osati kumwamba