Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

 Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kulambira mulungu wonyenga Baala ndi chiwerewere?

Akanani ankakhulupirira kuti mulungu wawo Baala ankapereka mphamvu zobereka. Anthu olambira Baala ankakhulupirira kuti iye ndi amene ankathandiza kuti mbewu ndiponso ziweto zawo zizibereka kwambiri. N’chifukwa chake buku lina linanena kuti: “Anthu ankachita zachiwerewere kuti Baala nayenso agonane ndi mkazi wake Asera, n’cholinga choti mbewu ndi ziweto zawo zibereke kwambiri.”​—Manners and Customs in the Bible.

Akanani ankakhulupirira kuti Baala ankathawira pansi padziko m’nthawi ya chilimwe akagonjetsedwa ndi Moti, mulungu amene ankachititsa chilala ndiponso imfa. Komabe, nyengo ya mvula ikayamba, iwo ankakhulupirira kuti Baala wayambanso kulamulira, zimene zinkachititsa kuti mbewu ndiponso ziweto zibereke kwambiri. Panthawi imeneyi Akanani ankasangalala pochita maphwando omwenso ankachitapo zachiwerewere. N’chifukwa chake Aisiraeli atayamba kulambira Baala wa ku Peori “anayamba kuchita chigololo ndi ana aakazi a Moabu.”​—Numeri 25:1-3.

N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti alembi ndi Afarisi anali ofanana ndi “manda opaka laimu woyera”?

Yesu anadzudzula alembi ndi Afarisi kuti anali onyenga ndipo anawauza kuti: “Mumafanana ndi manda opaka laimu woyera, amene kunja kwake amaonekadi okongola, koma mkati mwake muli mafupa a anthu akufa ndi zonyansa za mitundu yonse.” (Mateyo 23:27) Ayuda ankakonda kupaka manda laimu woyera n’cholinga chakuti azionekera kwambiri. Ankachita zimenezi chakumapeto kwa dzinja, patsiku la 15 la mwezi wa Adara, kutatsala mwezi umodzi kuti Pasika achitike. Koma panthawi ya mvula laimuyo ankachoka.

Malinga ndi buku lina, manda ankapakidwa laimu poteteza “anthu ambiri kuti asadetsedwe akamabwera ku Yerusalemu ku mwambo wa Pasika.” (The Jewish Encyclopedia) Lamulo la pa Numeri 19:16 limafotokoza kuti munthu aliyense wokhudza mtembo, kaya mafupa ake, kapena manda, ankakhala wodetsedwa kwa masiku 7. M’nthawi ya Aisiraeli, munthu akakhala wodetsedwa sankaloledwa kuchita mwambo uliwonse wokhudza kulambira ndipo akapanda kumvera zimenezi ankaphedwa. (Levitiko 15:31) Chifukwa chakuti Yesu ananena fanizoli patangotsala masiku ochepa kuti Pasika achitike, anthu ambiri analimvetsa chifukwa panthawiyi manda ambiri anali atapakidwa laimu. Choncho, mfundo ya Yesu inali yakuti adani ake anali osiyana ndi mmene ankaonekera kunja ndipo kugwirizana nawo kunali kodetsa mwauzimu.

[Chithunzi patsamba 15]

Chithunzi cha Baala cha m’ma 1300 ndi 1200 B.C.E.

[Mawu a Chithunzi]

Musée du Louvre, Paris