Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zinachititsa Kuti Dzikoli Lisakhale Paradaiso

Zimene Zinachititsa Kuti Dzikoli Lisakhale Paradaiso

 Zoti Achinyamata Achite

Zimene Zinachititsa Kuti Dzikoli Lisakhale Paradaiso

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthuwo akumvera.

ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI GENESIS 3:1-24.

Kodi mukuganiza kuti Hava anatani njoka itayamba kumulankhula?

․․․․․

Adamu ndi Hava atachimwa mwadala, kodi mukuganiza kuti anamva bwanji mumtima mwawo, malinga ndi zimene zili mu vesi 7 mpaka10?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti zinali bwanji pamene Adamu ndi Hava ankatulutsidwa m’munda mwa Edeni, monga afotokozera mu vesi 22 mpaka 24?

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Kodi maso a Hava anathandizira bwanji kuti iye achimwe? (Werenganinso vesi 6.)

․․․․․

N’chifukwa chiyani chipatsocho chinaoneka ‘chokoma m’maso’ kwa Hava? (Werenganinso vesi 4 ndi 5.)

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimene chinachititsa Adamu kuti achimwe ngati mkazi wake Hava? (Werenganinso vesi 6.)

․․․․․

Kodi kuchimwa kwawo kunakhudza bwanji ubwenzi wa amuna ndi akazi a m’tsogolo? (Werenganinso vesi 16.)

․․․․․

Kodi tikudziwa bwanji kuti ubwenzi wa Adamu ndi Hava unasokonezeka atachimwa? (Werenganinso vesi 12.)

․․․․․

Kodi Yehova anatani kuti cholinga chake chisasokonezeke? (Werenganinso vesi 15.)

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Kuipa kwa mtima wofuna kudzilamulira.

․․․․․

Mmene maso angachititsire munthu kuchita zoipa.

․․․․․

Kuipa konamizira ena tikalakwitsa zinthu.

․․․․․

M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․