Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Agalatiya, Aefeso, Afilipi, ndi Akolose

Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Agalatiya, Aefeso, Afilipi, ndi Akolose

 Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’makalata Opita kwa Agalatiya, Aefeso, Afilipi, ndi Akolose

MTUMWI Paulo analembera “mipingo ya ku Galatiya” kalata yamphamvu, atamva kuti Ayuda osunga mwambo akupatutsa Akhristu ena pa kulambira koona. (Agal. 1:2) Kalatayi inalembedwa cha m’ma 50 mpaka 52 C.E., ndipo ili ndi malangizo achindunji ndi olimbikitsa.

Patatha zaka pafupifupi khumi ali “wandende mwa Khristu Yesu” ku Roma, Paulo analembera makalata mipingo ya ku Efeso, Filipi, ndi Kolose, kuwapatsa malangizo ndi kuwalimbikitsa mwachikondi. (Aef. 3:1) Ifenso tingapindule mwa kuwerenga uthenga wa m’mabuku a m’Baibulo a Agalatiya, Aefeso, Afilipi ndi Akolose.​—Aheb. 4:12.

AMAYESEDWA BWANJI OLUNGAMA?

(Agal. 1:1–6:18)

Popeza Ayuda osunga mwambo ankachita zinthu mochenjera kuti anthu asamam’khulupirire Paulo, iye anawatsimikizira kuti analidi mtumwi mwa kufotokoza mfundo zina zokhudza moyo wake. (Agal. 1:11–2:14) Potsutsa ziphunzitso zawo zonama, Paulo anati: “Munthu amayesedwa wolungama kokha mwa kukhulupirira Khristu Yesu, osati chifukwa cha ntchito za chilamulo, taika chikhulupiriro chathu mwa Khristu Yesu.”​—Agal. 2:16.

Paulo anati, Khristu ‘anamasula anthu okhala pansi pa chilamulo mwa kuwagula’ ndi kuwamasula kukhala paufulu wachikhristu. Iye analimbikitsa kwambiri Agalatiya kuti: “Chirimikani, ndipo musalole kumangidwanso m’goli la ukapolo.”​—Agal. 4:4, 5; 5:1.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

3:16-18, 28, 29—Kodi pangano la Abulahamu likugwirabe ntchito? Inde. Pangano la Chilamulo linali longowonjezera chabe, osati lolowa m’malo mwa pangano limene Mulungu anapangana ndi Abulahamu. Choncho, pangano la Abulahamu limagwirabe ntchito Chilamulo ‘chitathetsedwa.’ (Aef. 2:15) Zimene Abulahamu analonjezedwa zinagwiranso ntchito kwa Khristu Yesu, “mbewu” yaikulu komanso yeniyeni ya Abulahamu, ndiponso kwa amene ‘ali a Khristu.’

6:2—Kodi “chilamulo cha Khristu” n’chiyani? Chilamulo chimenechi ndi zinthu zonse zimene Yesu anaphunzitsa komanso zimene analamula makamaka lamulo lakuti ‘tizikondana wina ndi mnzake.’​—Yoh. 13:34.

6:8—Kodi ‘timafesera bwanji mzimu’? Timachita zimenezi mwa kulola mzimu wa Mulungu kutsogolera zochita zathu. Kuti munthu afesere mzimu, amafunika kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingachititse mzimuwo kugwira ntchito pamoyo wake.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:6-9. Akulu achikhristu amafunika kusamalira mwamsanga mavuto amene angabuke mu mpingo. Mwa kuganiza bwino komanso kugwiritsa ntchito Malemba, angathetse mwamsanga maganizo olakwika.

2:20. Dipo ndi mphatso imene Mulungu anapatsa munthu aliyense payekha. Ndipo tiziiona kuti anatipatsa ifeyo patokha.​—Yoh. 3:16.

5:7-9. Mayanjano oipa ‘angatisokoneze kuti tisapitirize kumvera choonadi.’ Choncho ndi nzeru kuwapewa.

6:1, 2, 5Anthu amene ali “oyenerera mwauzimu” angatithandize kunyamula mtolo, monga vuto linalake lolemetsa kapena lovutitsa maganizo limene labwera chifukwa chopatuka panjira mosadziwa. Koma, pankhani yonyamula katundu wathu wauzimu, umenewu ndi udindo wathu.

 ‘KUSONKHANITSA ZINTHU ZONSE MWA KHRISTU’

(Aef. 1:1–6:24)

M’kalata yake yopita ku Efeso, Paulo anatsindika mfundo yonena za umodzi wachikristu. Iye anatchula za dongosolo limene lidzakhalepo, “ikadzatha nyengo yonse ya nthawi zoikika. . . . Kusonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu, zinthu za kumwamba ndi zinthu za padziko lapansi.” Khristu wapatsa “mphatso za amuna” kuti athandize onse ‘kufika pa umodzi m’chikhulupiriro.’​—Aef. 1:10; 4:8, 13.

Kuti Akhristu alemekeze Mulungu ndiponso athandize kuti umodzi upitirire, ayenera “kuvala umunthu watsopano” ndiponso ‘kugonjerana wina ndi mnzake poopa Khristu.’ Ayeneranso “kuchirimika polimbana ndi machenjera a Mdyerekezi” mwa kuvala zida zonse zankhondo zauzimu.​—Aef. 4:24; 5:21; 6:11.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:4-7—Kodi Akhristu odzozedwa anawasankhiratu motani asanabadwe? Anawasankhiratu monga gulu, osati mmodzimmodzi. Zimenezi zinachitika anthu oyambirira atachimwa koma asanakhale ndi ana. Ulosi wa pa Genesis 3:15, umene unanenedwa makolo ochimwawa asanayambe kubereka ana, umasonyeza kuti Mulungu analinganiza zoti otsatira Khristu ena adzalamulire naye kumwamba.​—Agal. 3:16, 29.

2:2—Kodi mzimu wa dziko umafanana bwanji ndi mpweya, ndipo umalamulira bwanji dzikoli? “Mzimu wa dziko,” womwe ndi mzimu wofuna kudzilamulira komanso wosafuna kumvera ena ndi wofala kwambiri ngati mpweya. (1 Akor. 2:12) Umalamulira dziko chifukwa ndi wamphamvu komanso nthawi zonse umalimbikitsa anthu kuchita zosokonekera.

2:6—Kodi Akhristu odzozedwa angakhale bwanji “m’malo akumwamba” ali padziko pano? Mawu akuti “m’malo akumwamba” palembali sakunena za mphoto yawo yopita kumwamba imene analonjezedwa. Komano, akunena za ubwenzi wawo wapadera umene ali nawo ndi Mulungu chifukwa chakuti ‘aikidwa chisindikizo cha mzimu woyera wolonjezedwawo.’​—Aef. 1:13, 14.

Zimene Tikuphunzirapo:

4:8, 11-15. Yesu Khristu “anagwira anthu ukapolo” kutanthauza kuti anatenga amuna m’dziko la Satanali n’cholinga chakuti agwire ntchito yolimbikitsa mpingo wachikhristu. Tonse ‘tingakule m’zinthu zonse, kudzera mwa iye amene ali Khristu’ ngati timvera ndi kugonjera anthu amene akutitsogolera ndiponso tikamatsatira zimene akonza mumpingo.​—Aheb. 13:7, 17.

5:22-24, 33. Mkazi ayenera kugonjera ndi kulemekeza mwamuna wake. Angachite zimenezi mwa kusonyeza “mzimu wabata ndi wofatsa” ndiponso mwa kuyesetsa kunena zabwino zokhudza mwamuna wake ndi kugwirizana ndi zimene mwamunayo wasankha kuchita kuti zinthu ziyende bwino.​—1 Pet. 3:3, 4; Tito 2:3-5.

5:25, 28, 29. Monga mmene mwamuna ‘amadzidyetsera’ yekha, afunikanso kusamalira bwino mkazi wake mwa kum’pezera zinthu zofunika pamoyo, kum’thandiza maganizo, ndiponso pankhani zauzimu. Iye afunikanso kum’samalira mwa kucheza naye mokwanira ndiponso kum’sonyeza chikondi polankhula ndi pochita zinthu.

6:10-13. Kuti tipewe mzimu wa ziwanda, tifunika kuvala mokwanira zovala zankhondo zauzimu zochokera kwa Mulungu.

TIPITIRIZE KUYENDA MOYENERA”

(Afil. 1:1–4:23)

Kalata imene Paulo analembera Afilipi, imatsindika kufunika kwa chikondi. Iye anati: “Ine ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirize kukula, limodzi ndi kudziwa zinthu molondola, komanso kuzindikira zinthu bwino lomwe.” Powathandiza kuti apewe mzimu wodzidalira, iye anawalimbikitsa kuti: “Pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwa mantha ndi kunjenjemera.”​—Afil. 1:9; 2:12.

Paulo analimbikitsa anthu okhwima mwauzimu kuyesetsa ‘mpaka akapate mphoto ya  chiitano cha Mulungu.’ Iye anati: “Pa mlingo uliwonse, mulimonse mmene tapitira patsogolo, tipitirize kuyenda moyenera m’njira yomweyo.”​—Afil. 3:14-16.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:23—Kodi Paulo anapanikizidwa ndi ‘zinthu ziwiri’ ziti, nanga anafuna “kumasuka” ku chiyani? Chifukwa cha mmene zinthu zinalili pamoyo wa Paulo, iye anapanikizika kuti asankhe pakati pa zinthu ziwiri izi, moyo kapena imfa. (Afil. 1:21) Ngakhale kuti sananene zimene anasankha, iye anasonyeza zimene ankafuna, “kumasuka ndi kukhala ndi Khristu.” (Afil. 3:20, 21; 1 Ates. 4:16) “Kumasuka” kumeneku kunapangitsa Paulo kulandira mphoto imene Yehova anamukonzera panthawi ya kukhalapo kwa Khristu.​—Mat. 24:3.

2:12, 13—Kodi Mulungu amatithandiza motani ‘kufuna ndiponso kuchita’ utumiki wake? Mzimu woyera wa Yehova ungagwire ntchito m’mitima ndi m’maganizo athu kuti tikulitse mtima wofuna kuchita zimene tingathe pom’tumikira. Choncho, amatithandiza pamene ‘tikupitiriza kukonza chipulumutso chathu.’

Zimene Tikuphunzirapo:

1:3-5. Ngakhale kuti Afilipi anali osauka, iwo anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pankhani yogawira ena zinthu.​—2 Akor. 8:1-6.

2:5-11. Monga mmene chitsanzo cha Yesu chikusonyezera, kudzichepetsa si mantha koma kulimba mtima. Komanso, Yehova amakweza anthu odzichepetsa.​—Miy. 22:4.

3:13. “Zinthu za kumbuyo” zingakhale zinthu monga ntchito yapamwamba, kukhala m’banja lachuma kwambiri, kapena machimo aakulu amene tinalapa ndipo ‘tinasambitsidwa n’kukhala oyera.’ (1 Akor. 6:11) Tiyenera kuiwala zinthu zimenezi, tisiye kuziganizira, ndipo ‘tikalamire za kutsogolo.’

“KUKHAZIKIKA M’CHIKHULUPIRIRO”

(Akol. 1:1–4:18)

M’kalata imene analembera Akolose, Paulo anatchula maganizo olakwika a aphunzitsi onyenga. Iye anati, chipulumutso sichidalira pa kutsatira Chilamulo, koma ‘kupitiriza kukhazikika m’chikhulupiriro.’ Paulo analimbikitsa Akolose ‘kuyenda mogwirizana [ndi Khristu]. Kukhalabe ozikika mozama, . . . kupitiriza kumangidwa mwa iye ndi kukhazikika m’chikhulupiriro.’ Kodi kukhazikika kumeneku kukanawathandiza bwanji?​—Akol. 1:23; 2:6, 7.

Paulo analemba kuti: “Valani chikondi, pakuti ndicho chomangira umodzi changwiro. Komanso, mtendere wa Khristu ulamulire m’mitima yanu.” Mtumwiyu anawauza kuti: “Chilichonse chimene mukuchita, muchichite ndi moyo wanu wonse, monga kuchitira Yehova, osati anthu.” Ponena za anthu akunja, iye anati: “Pitirizani kuyenda mwanzeru” kwa iwo.​—Akol. 3:14, 15, 23; 4:5.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

2:8—Kodi “mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli” zimene Paulo anachenjeza n’chiyani? Zimenezi ndi zinthu za m’dziko la Satanali, zomwe ndi mfundo zimene zimatsogolera kapena zimene anthu m’dzikoli amayendera. (1 Yoh. 2:16) Zinthu zimenezi ndi monga nzeru za anthu, kukonda chuma, ndiponso zipembedzo zonyenga za dzikoli.

4:16—Kodi n’chifukwa chiyani kalata yopita kwa anthu a ku Laodikaya sinalembedwe m’Baibulo? Chingakhale chifukwa chakuti kalatayi inalibe zinthu zothandiza masiku ano. Kapena mwina inali ndi mfundo zofanana ndi zimene zinali m’makalata ena.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:2, 20. Chifukwa cha chisomo chake, Mulungu anapereka dipo limene lingatithandize kuti tikhale ndi chikumbumtima chabwino komanso mtendere wa mumtima.

2:18, 23. “Kudzichepetsa kwachinyengo,” komwe ndi kunamizira kudzichepetsa n’cholinga chokopa ena mwina pokana chuma kapena kudzimana monyanyira, ndi chizindikiro chakuti munthuyo ‘amadzitukumula ndi maganizo ake aumunthu.’