Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Sataya Anthu Ake Okhulupirika

Yehova Sataya Anthu Ake Okhulupirika

 Yehova Sataya Anthu Ake Okhulupirika

‘Yehova sataya okondedwa [“okhulupirika,” NW] ake: Asungika kosatha.’​—SAL. 37:28.

1, 2. (a) Kodi anthu okhulupirika a Mulungu anakumana ndi mayesero otani m’zaka za m’ma 900 B.C.E.? (b) Kodi Yehova anateteza anthu ake pa zinthu zitatu ziti?

ZAKA za m’ma 900 B.C.E. zinali zovuta kwa atumiki a Yehova. Inali nthawi yoti aganize mofatsa. Nkhondo yapachiweniweni inali itangolephereka pang’onong’ono chifukwa chakuti mafuko a kumpoto a Aisiraeli anapatsidwa ufulu wodzilamulira. Mfumu yawo yatsopano Yerobiamu, nthawi yomweyo inalamula kuti anthu onse m’dzikolo akhale a chipembedzo chimodzi chimene inakhazikitsa. Iye anafuna kuti nzika zake zonse zizimumvera. Kodi atumiki okhulupirika a Yehova anatani? Kodi anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu wawo? Ambiri anatero ndipo Yehova anali kuwateteza chifukwa cha kukhulupirika kwawo.​—1 Maf. 12:1-33; 2 Mbiri 11:13, 14.

2 Masiku anonso, atumiki okhulupirika a Mulungu akuyesedwa. Baibulo limachenjeza kuti: “Sungani maganizo anu, khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.” Kodi tingathe kukhala ‘olimba m’chikhulupiriro, ndi kulimbana naye’? (1 Pet. 5:8, 9) Tiyeni tione zina mwa zinthu zimene zinachitika pa nthawi imene Mfumu Yerobiamu amalumbiritsidwa kukhala Mfumu m’chaka cha 997 B.C.E. ndipo titengepo phunziro. Panthawi yovuta imeneyo, atumiki okhulupirika a Yehova anali kuponderezedwa, anali kulimbana ndi anthu opanduka, komanso anali kugwira ntchito yovuta. Panthawi zonsezi, Yehova sanataye anthu ake okhulupirika, ndipo sangawatayenso masiku ano.​—Sal. 37:28.

Akamaponderezedwa

3. N’chifukwa chiyani ulamuliro wa Mfumu Davide sunali wopondereza?

3 Tiyeni tione mmene zinthu zinalili panthawi ya ulamuliro wa Yerobiamu. Lemba la Miyambo 29:2 limati: “Pochuluka olungama anthu akondwa; koma polamulira woipa anthu ausa moyo.” Panthawi imene Mfumu Davide imalamulira Isiraeli, anthu sankausa moyo. Inde, Davide sanali wangwiro, komabe anali wokhulupirika kwa Mulungu. Ulamuliro wa Davide sunali wopondereza. Popangana pangano ndi Davide, Yehova anati: “Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.”​—2 Sam. 7:16.

4. Kodi Solomo ndi anthu ake anafunika kuchita chiyani kuti adalitsidwe?

4 Poyamba, ulamuliro wa Solomo mwana wa Davide, unali wamtendere ndiponso wabwino moti unali kuimiradi ulamuliro wa Yesu Khristu umene ukubwera m’tsogolo wa zaka 1,000. (Sal. 72:1, 17) Ndipo panalibe fuko lililonse pa mafuko 12 a Isiraeli limene linafuna kuukira ufumuwo. Komabe, kuti Solomo ndi anthu ake adalitsidwe anafunika kumvera Mulungu. N’chifukwa chake Yehova anauza Solomo kuti: “Ukamayenda iwe m’malemba anga, ndi kumachita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse  kuyendamo, pamenepo ine ndidzakhazikitsira iwe mawu anga amene ndinauza Davide atate wako. Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Isiraeli osawasiya anthu anga a Isiraeli.”​—1 Maf. 6:11-13.

5, 6. Kodi chinachitika n’chiyani Solomo atasiya kukhala wokhulupirika kwa Mulungu?

5 Solomo atakalamba, anasiya kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndipo anayamba kulambira konyenga. (1 Maf. 11:4-6) Pang’ono ndi pang’ono, Solomo anasiya kutsatira malamulo a Yehova ndipo anayamba kupondereza anthu kwambiri. Ndipo Solomo atafa anthu sanasiyebe kum’dandaula kwa mwana wake Rehobiamu amene analowa m’malo mwake ndipo anam’pempha kuti asinthe zinthu. (1 Maf. 12:4) Kodi Yehova anatani Solomo atasiya kukhala wokhulupirika?

6 Baibulo limatiuza kuti: “Yehova anakwiya ndi Solomo, pokhala mtima wake unapambuka kwa . . . Mulungu wa Isiraeli, amene adamuonekera kawiri.” Yehova anauza Solomo kuti: “Popeza . . . sunasunga chipangano changa ndi malemba anga amene ndinakulamulira, zedi, ndidzakung’ambira ufumu ndi kuupatsa mnyamata wako.”​—1 Maf. 11:9-11.

7. Ngakhale kuti Yehova anam’siya Solomo, kodi Iye anasamalira bwanji anthu ake okhulupirika?

7 Ndiyeno Yehova anatumiza mtumiki wake Ahiya kukadzoza Yerobiamu munthu amene anadzapulumutsa anthu Ake. Iye anali munthu wanzeru amene anagwira ntchito mu ulamuliro wa Solomo. Ngakhale kuti Yehova anali wokhulupirika ku pangano la Ufumu limene anapanga ndi Davide, iye anavomereza kuti ufumu wa mafuko 12 ugawidwe. Yerobiamu anatenga mafuko khumi ndipo mafuko awiri anakhalabe ku banja la Davide, limene mfumu yake panthawiyi inali Rehabiamu. (1 Maf. 11:29-37; 12:16, 17, 21) Yehova anauza Yerobiamu kuti: “Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m’njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga, pamenepo ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinam’mangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Isiraeli.” (1 Maf. 11:38) Apatu Yehova anathandiza anthu ake kuchoka ku ulamuliro wopondereza.

8. Kodi anthu a Mulungu akukumana ndi mavuto otani masiku ano?

8 Kuponderezana ndi kupanda chilungamo n’kofala masiku ano. Lemba la Mlaliki 8:9 limati: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” Pamakhala mavuto azachuma chifukwa cha dyera pankhani za malonda ndiponso ulamuliro woipa. Nthawi zambiri, atsogoleri a boma, a zamalonda, ndiponso a zachipembedzo sapereka chitsanzo chabwino. N’chifukwa chake, mofanana ndi munthu wolungama Loti, masiku ano anthu okhulupirika a Mulungu ‘amavutika mtima kwambiri ndi anthu ophwanya malamulo mwa kulowerera kwawo khalidwe lotayirira.’ (2 Pet. 2:7) Ndipotu, tikamayesetsa kutsatira mfundo za Mulungu, nthawi zambiri timazunzidwa ndi olamulira odzikuza.​—2 Tim. 3:1-5, 12.

9. (a) Kodi n’chiyani chimene Yehova wachita kuti apulumutse anthu ake? (b) N’chifukwa chiyani tili otsimikiza kuti Yesu adzakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu?

9 Komabe, tiyenera kukhulupirira mfundo yofunika iyi: Yehova sataya anthu ake okhulupirika. Tangoganizirani zimene wachita kale kuti achotse olamulira oipa a dzikoli. Ufumu wa Mulungu wa Mesiya wolamulidwa ndi Khristu Yesu unakhazikitsidwa kale. Yesu Khristu watha zaka pafupifupi 100 akulamulira kumwamba. Posachedwapa iye adzathetsa mavuto onse a anthu amene amaopa dzina la Mulungu. (Werengani Chivumbulutso 11:15-18.) Yesu anakhala wokhulupirika kwa Mulungu mpaka imfa. Choncho, sadzakhumudwitsa nzika zake monga anachitira Solomo.​—Aheb. 7:26; 1 Pet. 2:6.

10. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika? (b) Tikamavutika, kodi tisamakayike chiyani?

10 Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni limene lidzathetsa mavuto onse ndipo ifeyo timakhulupirira Yehova Mulungu ndi Ufumu wakewu. Chifukwa chodalira kwambiri Ufumuwu, timapewa makhalidwe oipa a dzikoli ndipo timalimbikira kuchita ntchito zabwino. (Tito 2:12-14) Timayesetsa kuti tisadetsedwe ndi dziko lino.  (2 Pet. 3:14) Kaya tikumane ndi mavuto otani, timakhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzatiteteza kuti tisavulale mwauzimu. (Werengani Salmo 97:10.) Komanso lemba la Salmo 116:15 limatitsimikizira kuti: “Imfa ya okondedwa ake ndi ya mtengo wake pamaso pa Yehova.” Yehova amaona kuti atumiki ake ndi amtengo wapatali ndipo sadzalola kuti onse awonongeke.

Polimbana ndi Anthu Opanduka

11. Kodi zinakhala bwanji kuti Yerobiamu akhale wosakhulupirika?

11 Ulamuliro wa Mfumu Yerobiamu ukanathetsa mavuto a anthu a Mulungu. Koma m’malo mwake, zochita zake zinayesa atumiki okhulupirika a Mulungu. Yerobiamu sanakhutire ndi ufumu wake motero anayamba kufuna njira zolimbitsira ufumuwo. Iye anaganiza kuti: “Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m’nyumba ya Yehova m’Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wawo, kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda.” Choncho, Yerobiamu anakhazikitsa malo atsopano olambirirapo mafano a ana a ng’ombe awiri agolidi. “Ndipo anaimika mmodzi ku Beteli, naimika wina ku Dani. Koma chinthu ichi chinasanduka tchimo, ndipo anthu anamka ku mmodziyo wa ku Dani. Iye namanga nyumba za m’misanje, nalonga anthu achabe akhale ansembe, osati ana a Levi ayi.” Yerobiamu anaika tsiku lakelake la ‘madyerero a ana a Aisiraeli’ ndipo ‘anapereka nsembe pa guwa la nsembe, nafukiza zonunkhira.’​—1 Maf. 12:26-33.

12. Kodi anthu okhulupirika mu ufumu wa kumpoto anatani Yerobiamu atayambitsa kulambira mafano a ana a ng’ombe mu Isiraeli?

12 Kodi anthu a ufumu wa kumpoto amene anali okhulupirika kwa Mulungu akanatani tsopano? Mofanana ndi makolo awo okhulupirika, Alevi okhala m’mizinda imene anapatsidwa kudera la ufumu wa kumpoto anachitapo kanthu nthawi yomweyo. (Eks. 32:26-28; Num. 35:6-8; Deut. 33:8, 9) Iwo anasiya chuma chawo ndipo anasamukira chakum’mwera ku Yuda ndi mabanja awo, kumene anapitiriza kulambira Yehova popanda kudodometsedwa. (2 Mbiri 11:13, 14) Aisiraeli ena amene ankakhala mongoyembekezera ku Yuda anaganiza zongokhazikika konko m’malo mobwerera kwawo. (2 Mbiri 10:17) Yehova anaonetsetsa kuti pakhale njira yobwezeretsera kulambira koona kuti m’tsogolo anthu ena a ufumu wa kumpoto adzathe kusiya kulambira mafano a ana a ng’ombe ndi kubwerera ku Yuda.​—2 Mbiri 15:9-15.

13. Kodi anthu opanduka akuwayesa bwanji anthu a Mulungu masiku ano?

13 Zochita za anthu opanduka zimakhudza anthu a Mulungu masiku  ano. Olamulira ena akhazikitsa chipembedzo chimodzi m’dziko lawo, n’kumakakamiza nzika zawo kulowa chipembedzocho. Atsogoleri achipembedzo ndiponso anthu ena odzikuza amati iwo ndi ansembe a Ufumu wa Mulungu. Koma, ndi pakati pa Akhristu oona okha pamene pali “ansembe achifumu” enieni, omwe ndi odzozedwa.​—1 Pet. 2:9; Chiv. 14:1-5.

14. Kodi tizichita chiyani ndi mfundo za anthu opanduka?

14 Mofanana ndi Alevi okhulupirika a m’zaka za m’ma 900 B.C.E., masiku ano anthu okhulupirika a Mulungu satengeka ndi mfundo za anthu opanduka. Anthu odzozedwa ndiponso Akhristu anzawo amapewa ndi kukana mofulumira mfundo za anthu opanduka. (Werengani Aroma 16:17.) Ngakhale kuti timamvera malamulo a boma, sitilowa nawo ndale komanso ndife okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu. (Yoh. 18:36; Aroma 13:1-8) Sitigwirizana ndi anthu amene amati amatumikira Mulungu koma amene amam’kana ndi khalidwe lawo.​—Tito 1:16.

15. N’chifukwa chiyani timafunika kukhala okhulupirika kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?

15 Onaninso kuti Yehova wathandiza anthu oona mtima kuchoka m’dziko loipali n’kukhala m’paradaiso wauzimu amene iye wawakonzera. (2 Akor. 12:1-4) Timasangalala kumvera “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuyang’anira antchito ake a pakhomo, kuwapatsa chakudya chawo panthawi yoyenera.” Khristu wasankha kapolo ameneyu “kuyang’anira zinthu zake zonse.” (Mat. 24:45-47) Choncho, ngakhale titapanda kumvetsa mfundo zina zimene gulu la kapolo limanena, palibe chifukwa choti tikanire mfundozo kapena tibwerere ku dziko la Satana. M’malo mwake, kukhulupirika kumatithandiza kukhala odzichepetsa ndi kudikira Yehova kuti akonze zinthu.

Potumikira Mulungu

16. Kodi mneneri wochokera ku Yuda anapatsidwa ntchito yotani?

16 Yehova anakana Yerobiamu chifukwa cha kupanduka kwake. Iye anatuma mneneri kuchoka ku Yuda kupita kumpoto ku Beteli kuti akalankhule ndi Yerobiamu, ndipo anam’peza Yerobiamuyo akupereka nsembe pa guwa. Mneneriyo anapereka uthenga wachiweruzo kwa Yerobiamu. Kunena zoona, imeneyi inali ntchito yovuta zedi.​—1 Maf. 13:1-3.

17. Kodi Yehova anateteza bwanji mneneri wake?

17 Yerobiamu anakwiya kwambiri atamva chiweruzo cha Yehova. Iye anatambasulira dzanja lake kwa mtumiki wa Mulungu, ndipo anauza amuna amene anali pafupi kuti: “M’gwireni.” Nthawi yomweyo, munthu wina aliyense asanachite kanthu, “dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanatha kulifunyatitsanso. Ndiponso guwalo linang’ambika, ndi phulusa la pa guwalo linatayika.” Moti Yerobiamu anafika pongomuuza mneneriyo kuti am’pempherere kwa Yehova kuti am’chiritse dzanja lakelo. Mneneriyo anapempheradi, ndipo Yerobiamu anachira. Umu ndi mmene Yehova anatetezera mneneri wakeyu.​—1 Maf. 13:4-6.

18. Kodi Yehova amatiteteza bwanji tikamachita utumiki wopatulika mopanda mantha?

18 Pamene tikugwira ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu mokhulupirika ndiponso popanga ophunzira, nthawi zina timapeza anthu ovuta ndi aukali. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Koma tisalole kuti mantha achepetse changu chathu. Monga mneneri wa m’nthawi ya Yerobiamu, tili ndi ‘mwayi wochita utumiki wopatulika kwa Yehova mokhulupirika.’ * (Luka 1:74, 75) Ngakhale kuti masiku ano sitiyembekezera kuti Yehova  angatithandize mozizwitsa, iye akutitetezabe monga Mboni zake pogwiritsa ntchito mzimu woyera ndi angelo. (Werengani Yohane 14:15-17; Chivumbulutso 14:6.) Mulungu sadzataya anthu amene amalalikira mawu ake mopanda mantha.​—Afil. 1:14, 28.

Yehova Amateteza Anthu Ake Okhulupirika

19, 20. (a) Kodi tingatsimikize bwanji kuti Yehova sadzatitaya? (b) Kodi tikambirana mafunso otani m’nkhani yotsatira?

19 Yehova ndi Mulungu wokhulupirika. (Chiv. 15:4; 16:5) Iye ndi ‘wokhulupirika m’njira zake zonse.’ (Sal. 145:17) Ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti: “Atchinjiriza njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa [“okhulupirika,” NW.] ake.” (Miy. 2:8) Atumiki a Mulungu okhulupirika akamakumana ndi mavuto, akamalimbana ndi mfundo za a anthu opanduka kapena akamagwira ntchito yovuta, sakayikira kuti Yehova adzawatsogolera ndi kuwathandiza.

20 Aliyense akufunika kudzifunsa kuti: Kodi chingandithandize kukhala wokhulupirika kwa Yehova pamavuto kapena poyesedwa n’chiyani? Kapena mungadzifunse kuti, kodi ndingatani kuti ndikhalebe wokhulupirika kwa Mulungu?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Mneneriyu sanatchulidwe dzina, ndipo m’nkhani yotsatira tiona ngati anapitiriza kumvera Yehova kapena ayi, ndipo tionanso zimene zinam’chitikira.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti sataya anthu ake okhulupirika akamaponderezedwa?

• Kodi tizitani ndi mfundo za anthu opanduka?

• Kodi Yehova amateteza bwanji anthu ake okhulupirika pa utumiki wachikhristu?

[Mafunso]

[Mapu/​Chitunzi patsamba 5]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

UFUMU WA KUMPOTO (Yerobiamu)

Dani

SEKEMU

Beteli

UFUMU WA KUMWERA (Rehabiamu)

YERUSALEMU

[Chithunzi]

Yehova sanataye anthu ake okhulupirika Yerobiamu atayambitsa kulambira mafano a ana a ng’ombe

[Chithunzi patsamba 3]

Kuti Solomo ndi anthu ake adalitsidwe anafunika kumvera Mulungu