Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

• Kodi Akhristu ena amakumana ndi mavuto aakulu otani akakwatirana, ndipo ayenera kuyesetsa kuchita chiyani?

Akhristu ena amayamba kuzindikira kuti akusiyana maganizo pa zinthu zambiri ndi mwamuna kapena mkazi wawo. Podziwa kuti kusudzulana popanda chifukwa cha m’Malemba si njira yabwino yothetsera mavuto a m’banja, amayesetsa kuti ukwati wawo usathe.​—4/15, tsamba 17.

• Kodi Akhristu okalamba amene amakhala ku malo osungirako anthu okalamba amakumana ndi mavuto otani?

Okalamba akasamukira ku malo amenewa, angapezeke kuti ali m’gawo la mpingo wachilendo. Kumeneko iwo amakhala ndi anthu ambiri azikhulupiriro zina ndipo anthu amenewa amafuna kuti Akhristuwa azichita nawo mapemphero. Achibale awo omwe ndi Akhristu ndiponso anthu a mumpingo wa m’gawolo ayenera kudziwa mavuto amenewa ndi kuwathandiza.​—4/15, masamba 25-27.

• Kodi ndi njira zinayi ziti zimene zingathandize okwatirana kuthetsa mavuto?

Sankhani nthawi yoti mukambirane vutolo. (Mlal. 3:1, 7) Fotokozani maganizo anu mosabisa kanthu ndiponso mwaulemu. (Aef. 4:25) Mvetserani ndiponso zindikirani mmene mnzanuyo akumvera. (Mat. 7:12) Gwirizanani njira yothetsera vutolo. (Mlal. 4:9, 10)​—5/1, masamba 10-12.

• Kodi anthu a m’Bungwe Lolamulira amatumikira m’makomiti ati?

Komiti ya Oyang’anira; Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli; Komiti Yoona Zantchito Yofalitsa Mabuku; Komiti ya Utumiki; Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa; Komiti Yoona za Ntchito Yolemba.​—5/15, tsamba 29.

• Kodi tingatsimikize bwanji kuti chigumula cha Nowa chinachitikadi pa dziko lonse?

Yesu ankakhulupirira kuti chigumula chinachitikadi ndipo chinachitika padziko lonse. Machenjezo a m’Baibulo amatsimikizira kuti chigumula chinachitikadi padziko lonse.​—6/1, tsamba 8.

• Kodi makhalidwe oipa amene akufotokozedwa pa Aroma 1:24-32, akunena za Ayuda kapena anthu omwe sanali Ayuda?

Ngakhale kuti zimene anafotokoza zingakhudze magulu onse awiri, mtumwi Paulo anali kunena makamaka za Aisiraeli akale amene kwa zaka zambiri sanatsatire Chilamulo. Iwo ankadziwa malamulo olungama a Mulungu, koma sanafune kuwatsatira.​—6/15, tsamba 29.

• Kodi mzinda wa Tel Arad uli kuti, ndipo ndi wofunika chifukwa chiyani?

Mzinda umenewu uli ku Israel cha kumadzulo kwa Nyanja Yakufa, pafupi ndi bwinja la mzinda wakale wa Aradi. Pamalo amenewa, ofukula mabwinja apezapo mapale amene anthu ankalembapo zinthu. Pa mapale ena panalembedwa mayina a anthu a m’Baibulo, ndipo zikusonyeza kuti dzina la Mulungu linali kugwiritsidwa ntchito kwambiri.​—7/1, masamba 23-24.

• Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kusadzipanikiza kuti tikhale achimwemwe?

Ngati tidzipanikiza pofuna kuchita zimene sitingathe, tingangodzipweteka. Komabe, tiyenera kusamala kuti tisakhale aulesi n’kubwerera m’mbuyo muutumiki wachikhristu, podzikhululukira n’kumaganiza kuti zimene tikuchitazo ndi zokhazo zimene tingathe.​—7/15, tsamba 29.

• Kodi n’chiyani chingalepheretse makolo kulankhulana ndi ana awo achinyamata?

Zinthu monga manyazi ndi kufuna kukhala paokha, zimachititsa kuti kulankhulana ndi achinyamata kukhale kovuta. Makolo ayenera kulankhulana ndi ana pamene akucheza nawo ndipo aziyesetsa kumvetsa tanthauzo la zimene ana awo akunena.​—8/1, masamba 10-11.