Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumalankhula Bwino “Chinenero Choyera”?

Kodi Mumalankhula Bwino “Chinenero Choyera”?

 Kodi Mumalankhula Bwino “Chinenero Choyera”?

“Ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera [“chinenero choyera,” NW], kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova.”​—ZEF. 3:9.

1. Kodi Yehova anatipatsa mphatso yapadera yotani?

MPHATSO ya chinenero siinachokere kwa anthu koma kwa Mlengi wawo, Yehova Mulungu. (Eks. 4:11, 12) Mulungu anapatsa munthu woyamba, Adamu, luso lolankhula komanso lopanga mawu atsopano. (Gen. 2:19, 20, 23) Iyitu ndi mphatso ya mtengo wapatali. Mphatso imeneyi yathandiza anthu kuti azitha kulankhula ndi Atate wawo wakumwamba komanso kuti azitamanda dzina lake loyera.

2. Kodi n’chifukwa chiyani anthu salankhula chinenero chimodzi?

2 Kwa zaka 1,700 zoyambirira munthu atalengedwa, anthu onse ankalankhula chinenero chimodzi, kapena kuti “chilankhulidwe chimodzi.” (Gen. 11:1) Komano anthu a m’nthawi ya Nimrode atapanduka, zinthu zinasokonekera. Posatsatira malangizo a Yehova, anthu osamvera anasonkhana pamalo amene anadzatchedwa kuti Babele n’cholinga chakuti anthu onse azikhala pamodzi. Iwo anayamba kumanga nsanja yaitali, osati n’cholinga cholemekeza Yehova, koma kuti “adzipangire okha dzina.” Choncho, Yehova anasokoneza chinenero chawo ndipo iwo anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana. Ndiyeno anamwazikana padziko lonse lapansi.​—Werengani Genesis 11:4-8.

3. Kodi chinachitika n’chiyani Yehova atasokoneza chinenero cha anthu opanduka pa nsanja ya Babele?

3 Masiku ano anthu amalankhula zinenero zambiri, ena amati pali zinenero zoposa 6,800. Anthu olankhula chinenero chilichonse cha  zimenezi ali ndi kaganizidwe kawokawo. Zikuoneka kuti Yehova Mulungu atasokoneza chinenero cha anthu opandukawo, anafufutiratu m’maganizo mwawo chinenero chawo choyambacho. Ndiyeno anawapatsa zinenero zina zimene zinali ndi kaganizidwe komanso malamulo atsopano. N’chifukwa chake malo amene panamangidwa nsanjapo anatchedwa Babele, kutanthauza kuti chisokonezo. N’zochititsa chidwi kuti ndi Baibulo lokha limene limafotokoza bwino chifukwa chake pali zinenero zosiyanasiyana chonchi.

Chinenero Choyera

4. Kodi Yehova analosera kuti chidzachitike n’chiyani masiku athu ano?

4 Nkhani ya m’Baibulo ya zimene Mulungu anachita pa nsanja ya Babele ndi yochititsa chidwi, koma masiku athu ano pali chinthu china chochititsa chidwi kuposa zimenezi. Kudzera mwa mneneri wake Zefaniya, Yehova analosera kuti: “Pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera [“chinenero choyera”], kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kum’tumikira ndi mtima umodzi.” (Zef. 3:9) Kodi “chinenero choyera” chimenechi ndi chiti, ndipo tingaphunzire bwanji kuchilankhula bwino?

5. Kodi chinenero choyera n’chiyani, ndipo chathandiza anthu kuchita chiyani?

5 Chinenero choyera ndicho choonadi chonena za Yehova Mulungu ndi chifuniro chake chopezeka m’Mawu ake, Baibulo. Kuti munthu adziwe “chinenero” chimenechi afunika kumvetsa bwino choonadi cha Ufumu wa Mulungu, mmene udzayeretsere dzina la Yehova, mmene udzatsimikizirire kuti Iye ndiye woyenera kulamulira, ndiponso mmene udzadalitsire anthu okhulupirika. Kodi chinenero chimenechi chathandiza anthu kuchita chiyani? Chachititsa kuti anthu ‘aitanire pa dzina la Yehova’ ndi ‘kum’tumikira ndi mtima umodzi.’ Mosiyana ndi zimene zinachitika pa Babele, chinenero choyera chachititsa anthu kutamanda dzina la Yehova ndipo chathandiza kuti anthu ake akhale ogwirizana.

Kuphunzira Chinenero Choyera

6, 7. (a) Kodi n’chiyani chimafunika pophunzira chinenero chatsopano, ndipo zimenezi zingatithandize bwanji pophunzira chinenero choyera? (b) Kodi tsopano tikambirana chiyani?

6 Ngati munthu akufuna kuphunzira chinenero china, samangoloweza mawu okha, koma amafunikanso kuphunzira kaganizidwe ka anthu a chinenerocho. Anthu a zinenero zosiyana amapanga ziganizo ndiponso amachita nthabwala mosiyanasiyana. Komanso kuti athe kutchula mawu atsopano, afunikira kuphunzira katchulidwe katsopano. N’chimodzimodzinso ndi kuphunzira chinenero choyera cha choonadi cha m’Baibulo. Pamafunika zambiri osati kungophunzira mfundo zoyambirira za m’Baibulo zokha. Kuti tichidziwe bwino chinenero chimenechi, tifunika kusintha kwambiri kaganizidwe kathu.​—Werengani Aroma 12:2; Aefeso 4:23.

7 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizimva chinenero choyera komanso tizichilankhula bwino? Mofanana ndi kuphunzira chinenero, pali zinthu zimene zingatithandize kuti tizilankhula bwino chinenero cha choonadi cha m’Baibulo. Tiyeni tione zinthu zina zimene zimathandiza anthu pophunzira chinenero china ndiponso mmene zingatithandizire kuphunzira chinenero chatsopano chophiphiritsa.

Kulankhula Bwino Chinenero Choyera

8, 9. Kodi tiyenera kutani ngati tikufuna kuphunzira chinenero choyera, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika?

8 Kumvetsera mwatcheru. Munthu akamayamba kuphunzira chinenero china, amavutika kumva mawu a chinenerocho. (Yes. 33:19) Koma munthuyo akamamvetsera mwatcheru zimene akuphunzirazo amayamba kuzindikira mawu ena ndi ena ndiponso mmene ziganizo zikunenedwera. Mofanana ndi zimenezi, timalangizidwa kuti: “N’kofunika kuti tisamalire mwapadera, koposa mwa nthawi zonse, zinthu zimene tinamva, kuti tisatengeke konse pang’onopang’ono kusiya chikhulupiriro.” (Aheb. 2:1) Yesu analangizanso otsatira ake mobwerezabwereza kuti: “Amene ali ndi makutu amve.” (Mat.  11:15; 13:43; Maliko 4:23; Luka 14:35) Indedi, tifunika ‘kumvetsera ndi kuzindikira tanthauzo’ la zimene tikumva kuti tichidziwe bwino chinenero choyera.​—Mat. 15:10; Maliko 7:14.

9 Kumvetsera kumafunika chidwi, ndipo n’kopindulitsa. (Luka 8:18) Tikakhala pa misonkhano yachikhristu, kodi timamvetsera mwachidwi kapena timaganiza zina? N’kofunika kwambiri kumvetsera mwachidwi zimene zikukambidwa pamisonkhanopo. Apo ayi, timakhala ogontha m’kumva kwathu.​—Aheb. 5:11.

10, 11. (a)  N’chiyani chimene tiyenera kuchita kuwonjezera pa kumvetsera mwatcheru? (b) Kodi tikufunikanso kuchita chiyani kuti tizilankhula chinenero choyera?

10 Kutsanzira Amene Amalankhula Bwino. Anthu amene akuphunzira chinenero china amalimbikitsidwa kuti azimvetsera mwatcheru komanso kutsanzira mmene anthu ochidziwa bwino chinenerocho amalankhulira. Zimenezi zimathandiza ophunzirawo kuti asaphunzire katchulidwe ka mawu kolakwika kamene kangachititse kuti anthu asamawamve akamalankhula. Tikamaphunziranso chinenero choyera tifunika kutsanzira anthu amene ali ndi “luso la kuphunzitsa.” (2 Tim. 4:2) Ndi bwino kupempha ena kuti akuthandizeni. Mukalakwitsa muzimvera zimene akukulangizani.​—Werengani Aheberi 12:5, 6, 11.

11 Kulankhula chinenero choyera kumaphatikizapo kukhulupirira choonadi komanso kuuza ena choonadicho ndiponso kutsatira malamulo ndi mfundo za Mulungu pamoyo wathu. Kuti tithe kuchita zimenezi, tifunika kutsanzira ena. Zimenezi zikuphatikizapo kutsanzira chikhulupiriro ndi changu chawo komanso kutsanzira moyo wa Yesu. (1 Akor. 11:1; Aheb. 12:2; 13:7) Tikamayesetsa kuchita zimenezi, timakhala ogwirizana komanso timalankhula chinenero chimodzi monga anthu a Mulungu.​—1 Akor. 4:16, 17.

12. Kodi kuloweza kumathandiza bwanji pophunzira chinenero?

12 Kuloweza. Munthu amene akuphunzira chinenero china amafunika kuloweza mawu ndi zinthu zina zambiri. Kuloweza n’kothandizanso kwambiri kwa Akhristu kuti achidziwe bwino chinenero choyera. Tingachite bwino kwambiri kuloweza mayina a mabuku a m’Baibulo m’ndondomeko yake. Ena amachita khama kuloweza Malemba ndi mawu ake omwe. Ena aona kuti n’zothandiza kuloweza nyimbo za Ufumu, mayina a mafuko a Aisiraeli ndi a atumwi 12 a Yesu, komanso makhalidwe a chipatso cha mzimu. Kale Aisiraeli ambiri ankaloweza masalmo pamtima. M’nthawi yathu ino, mnyamata wina analoweza mavesi a m’Baibulo oposa 80 ndipo ankatha kutchula bwinobwino mawu onse a m’mavesiwa ali ndi zaka 6. Kodi nafenso tingayesetse kugwiritsa ntchito luso limeneli?

13. Kodi kuwerenga mobwerezabwereza n’kofunika chifukwa chiyani?

13 Kuwerenga mobwerezabwereza kumathandiza kuti tizikumbukira zimene tikuwerenga. Ndipo kukumbutsidwa zinthu mobwerezabwereza n’kofunikanso kwambiri pa maphunziro  athu achikhristu. Mtumwi Petulo anati: “Nthawi zonse ndizikukumbutsani zinthu zimenezi, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu okhazikika molimba m’choonadi chimene munachilandira.” (2 Pet. 1:12) N’chifukwa chiyani timafunika kukumbutsidwa? Chifukwa chakuti kumatithandiza kumvetsa zinthu, kudziwa zinthu zambiri, ndiponso kumatithandiza kumvera Yehova. (Sal. 119:129) Kuwerenga malangizo ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu nthawi zonse kumatithandiza kudziunika tokha ndi kupewa kukhala anthu “ongomva chabe.” (Yak. 1:22-25) Ngati tisiya kukumbukira mfundo za choonadi, tingayambe kuganiza zinthu zina ndipo tingaleke kulankhula bwino chinenero choyera.

14. Kodi n’chiyani chingatithandize pophunzira chinenero choyera?

14 Kuwerenga mokweza. (Chiv. 1:3) Anthu ena amakonda kuwerenga chamumtima chinenero chimene akuphunzira. Koma izi sizothandiza kwenikweni. Tikamaphunzira chinenero choyera, nthawi zina tifunika kuwerenga ‘molingirira’ kapena kuti motulutsa mawu chapansipansi kuti maganizo athu akhale pa zimene tikuwerenga. (Werengani Salmo 1:1, 2.) Zimenezi zimathandiza kuti tisaiwale zimene tikuwerengazo. Mu Chiheberi, mawu akuti ‘kulingirira’ ndi ofanana kwambiri ndi mawu akuti kusinkhasinkha. Monga mmene chakudya chifunikira kugayidwa m’thupi kuti chitipatse zofunikira, kusinkhasinkha n’kofunikanso kwambiri kuti timvetse zimene tikuwerengazo. Kodi tikamawerenga timakhala ndi nthawi yokwanira yosinkhasinkha? Tikamaliza kuwerenga Baibulo, tiyenera kusinkhasinkha zimene tawerengazo.

15. Kodi tingaphunzire bwanji malamulo a chinenero choyera?

15 Kuphunzira malamulo a chinenero. Mukamaphunzira chinenero, nthawi ina mumafunika kuphunzira malamulo ake, komanso mmene ziganizo zimapangidwira m’chinenerocho. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti timvetse mmene amayalira mawu m’chinenerocho ndipo izi zimatithandiza kuti tizilankhula bwino. Mofanana ndi zimenezi, chinenero choyera cha m’Malemba chilinso ndi malamulo ake omwe ndi “chitsanzo cha mawu opindulitsa.” (2 Tim. 1:13) Tifunikira kutengera “chitsanzo” chimenechi.

16. Kodi tifunikira kupewa chiyani, ndipo tingachite bwanji zimenezi?

16 Kupitiriza kuphunzira. Munthu atha kuphunzira chinenero mpaka kumalankhula bwinobwino  koma kenako n’kuleka kuphunzira. Izinso zingachitikire amene akuphunzira chinenero choyera. (Werengani Aheberi 5:11-14.) Kodi tingathetse bwanji vutoli? Tiyenera kupitirizabe kuphunzira mawu atsopano a chinenerochi. “Pamene tasiya chiphunzitso choyambirira cha Khristu tsopano, tiyeni tiyesetse mwakhama kufika pa uchikulire. Tisayambe kuyalanso maziko, ndiwo kulapa ntchito zakufa, chikhulupiriro mwa Mulungu, chiphunzitso cha maubatizo, kuika manja, kuuka kwa akufa ndi chiweruzo chamuyaya.”​—Aheb. 6:1, 2.

17. N’chifukwa chiyani tifunika kukhala ndi nthawi yophunzira nthawi zonse? Fotokozani.

17 Kukhala ndi nthawi yeniyeni yophunzira. N’kwabwino kukhala ndi nthawi yochepa yophunzira mokhazikika kusiyana ndi kuphunzira nthawi yaitali koma mwa apo ndi apo. Werengani pa nthawi imene mukuona kuti mutha kuikirapo mtima kwambiri pa zimene mukuwerengazo ndiponso simungadodometsedwe. Kuphunzira chinenero china kuli ngati kulambula njira m’nkhalango. Njirayo ikamadutsidwa kawirikawiri, m’pamene kumakhala kosavuta kuyendamo. Koma ngati njirayo sidutsidwa, simuchedwa kumeranso thengo. Choncho, pamafunika kugwiritsa ntchito njirayo mosalekeza. (Dan. 6:16, 20) N’chimodzimodzinso ndi chinenero choyera, tiyenera kupemphera ndi ‘kukhala maso mosalekeza’ pankhani yolankhula chinenero choyera cha m’Baibulo.​—Aef. 6:18.

18. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumalankhulalankhula chinenero choyera?

18 Kulankhulalankhula. Ena amene akuphunzira chinenero china sachilankhula chifukwa cha manyazi kapena kuopa kulakwitsa. Koma zimenezi zimawabwezera m’mbuyo. Kulankhulalankhula n’kofunika pophunzira chinenero. Munthu akamalankhulalankhula m’pamene amadziwa kulankhula bwino chinenerocho. Chimodzimodzinso chinenero choyera, tiyenera kuchilankhulalankhula kuti tichidziwe bwino. Baibulo limati: “Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mu mtima mwake kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyera chikhulupiriro chake kuti apulumuke.” (Aroma 10:10) ‘Timalengeza poyera’ chikhulupiriro chathu osati panthawi ya ubatizo yokha komanso nthawi iliyonse pamene tikulankhula za Yehova, kuphatikizapo pamene tili mu utumiki. (Mat. 28:19, 20; Aheb. 13:15) Misonkhano yachikhristu imatipatsa mwayi wolankhula bwino chinenero choyera.​—Werengani Aheberi 10:23-25.

Kulankhula Chinenero Choyera Mogwirizana Potamanda Yehova

19, 20. (a) Kodi Mboni za Yehova masiku ano zikuchita chinthu chodabwitsa chotani? (b) Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

19 Anthu amene anali ku Yerusalemu, Lamlungu pa Sivani 6 m’chaka cha 33 C.E., ayenera kuti anasangalala kwambiri. Tsiku limeneli nthawi itatsala pang’ono kukwana 9 koloko m’mawa, anthu onse amene anasonkhana m’chipinda chapamwamba ‘anayamba kulankhula malilime.’ (Mac. 2:4) Masiku ano, atumiki a Mulungu salankhula malilime. (1 Akor. 13:8) Komabe, Mboni za Yehova zimalengeza uthenga wabwino wa Ufumu m’zinenero zoposa 430.

20 Ngakhale timalankhula zinenero zosiyanasiyana, ndife osangalala kuti timagwirizana polankhula chinenero choyera cha choonadi cha m’Baibulo. Zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi zimene zinachitika pa nsanja ya Babele. Zili ngati kuti anthu a Yehova akutamanda dzina lake ndi chilankhulo chimodzi. (1 Akor. 1:10) Titsimikize mtima kupitiriza kutumikira ndi “mtima umodzi” ndi abale komanso alongo athu padziko lonse pamene tikuphunzira kulankhula bwino chinenero chimodzi chimenechi, kuti tilemekeze Atate wathu wa kumwamba Yehova.​—Werengani Salmo 150:1-6.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi chinenero choyera n’chiyani?

• Kodi tifunika kutani kuti tiphunzire chinenero choyera?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kulankhula bwino chinenero choyera?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 23]

Phunzirani Kulankhula Bwino Chinenero Choyera mwa

kumvetsera mwatcheru.

Luka 8:18; Aheb. 2:1

kutsanzira amene amalankhula bwino.

1 Akor. 11:1; Aheb. 13:7

kuloweza ndi kuwerenga mobwerezabwereza.

Yak. 1:22-25; 2 Pet. 1:12

kuwerenga mokweza.

Sal. 1:1, 2; Chiv. 1:3

kuphunzira malamulo a chinenero.

2 Tim. 1:13

kupitiriza kuphunzira.

Aheb. 5:11-14; 6:1, 2

kukhala ndi nthawi yeniyeni yophunzira.

Dan. 6:16, 20; Aef. 6:18

kulankhulalankhula.

Aroma 10:10; Aheb. 10:23-25

[Zithunzi patsamba 24]

Anthu a Yehova amalankhula chinenero choyera mogwirizana